Mau oyamba
KODI KUTSOGOLO KULI CIANI?
Kodi munadzifunsapo kuti umoyo wanu na banja lanu udzakhala bwanji kutsogolo? Baibo imakamba kuti:
“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Nsanja ya Mlonda ino, idzakuthandizani kumvetsetsa bwino colinga ca Mulungu cokhudza anthu na dziko lapansi, na zimene muyenela kucita kuti mupindule na colinga cimeneci.