Zamkati
WIKI YA APRIL 2-8, 2018
3 Tengelani Cikhulupililo ndi Kumvela kwa Nowa, Danieli, na Yobu
WIKI YA APRIL 9-15, 2018
8 Kodi Mumam’dziŵa Yehova Monga Mmene Nowa, Danieli, na Yobu Anam’dziŵila?
Nowa, Danieli ndi Yobu anakumana na mavuto ambili monga amene timakumana nawo masiku ano. Kodi n’ciani cinawathandiza kukhalabe okhulupilika ndi omvela? Kodi kum’dziwa bwino Yehova kunawathandiza bwanji kuti akhalebe na mtima wosagawanika? Nkhani ziŵilizi zidzayankha mafunso amenewa.
13 Mbili Yanga—Zinthu Zonse N’zotheka kwa Yehova
WIKI YA APRIL 16-22, 2018
18 Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauzanji?
WIKI YA APRIL 23-29, 2018
23 Pitani Patsogolo Monga Munthu Wauzimu
M’nkhani yoyamba, tidzakambilana tanthauzo la kukhala munthu wauzimu komanso zimene tingaphunzile pa zitsanzo za anthu auzimu. M’nkhani yaciŵili, tidzakambilana zimene tingacite kuti tikhale anthu auzimu ndi mmene kukhala munthu wauzimu kungatithandizile mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku.