LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 April masa. 26-30
  • Tinapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tinapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Nkhani Zofanana
  • “Zilumba Zambili Zisangalale”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 April masa. 26-30
M’bale Winston na mlongo Pam Payne, m’zaka zawo zaunyamata, akhala pa mwala m’mbali mwa nyanja

MBILI YATHU

Tinapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”

Kukambilana na M’bale Winston komanso Mlongo Pamela Payne

M’BALE Winston na mlongo Pamela (Pam) Payne, akutumikila pa ofesi ya nthambi ya ku Australasia. Iwo akhala akutumikila Yehova pamodzi mwacimwemwe. Koma pali mavuto ena amene anakumana nawo, monga kupita padela kwa mlongo Pam, komanso kuvutika kujaila cikhalidwe catsopano. Mosasamala kanthu za mavuto amenewa, iwo apitiliza kukonda Yehova na anthu ake, komanso kukhala acimwemwe mu utumiki wawo. Lekani kuti iwo atifotokozeleko zina zokhudza umoyo wawo..

M’bale Winston, tiuzenkoni mmene munaphunzilila coonadi ponena za Mulungu.

N’nakulila pa famu inayake ku Queensland, m’dziko la Australia, ndipo makolo anga sanali acipembedzo ciliconse. Popeza kuti famuyo inali kwayokha-yokha, sitinali kuonana ndi anthu ena kaŵili-kaŵili, kupatulapo abale anga amene n’nali kukhala nawo. Pamene n’nali na zaka pafupi-fupi 12, n’nayamba kufuna-funa coonadi ponena za Mulungu. M’kupita kwa nthawi, n’nacoka pafamu na kupita ku Adelaide, kumwela kwa dziko la Australia. Kumeneko n’napeza nchito. Nili na zaka 21, n’nakumana na Pam mumzinda wa Sydney, pamene n’nali pachuti. Iye ananiuza za gulu linalake lacipembedzo lochedwa British-Israel, limene limakamba kuti anthu a ku Britain ni mbadwa za mafuko obalalika a Isiraeli. Gululi limakamba kuti anthu a ku Britain anacokela ku mafuko 10 a Ufumu wa Kumpoto wa Isiraeli, amene anatengedwa kupita ku ukapolo m’zaka za m’ma 700 B.C.E. Conco, n’tabwelela ku Adelaide, n’nafunsa za nkhani imeneyi kwa mnzanga wina wa kunchito, amene anali kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova. Pambuyo pokambilana naye kwa maola ocepa, maka-maka zokhudza cikhulupililo ca Mboni, n’nazindikila kuti Yehova wayankha pemphelo limene n’napeleka nili wacicepele. N’nazindikilanso kuti zimene anali kufotokoza cinali coonadi ponena za Mlengi komanso Ufumu wake. Umu ni mmene n’napezela “ngale . . . yamtengo wapatali.”—Mat. 13:45, 46.

Mlongo Pam, na imwe munayamba kufuna-funa ngale ya coonadi kuyambila muli wacicepele, kodi munaipeza bwanji?

N’nakulila mumzinda wa Coffs Harbour ku New South Wales, ndipo makolo anga anali acipembedzo. Ambuya anga komanso amayi na atate anali kukhulupilila ziphunzitso za gulu lacipembedzo la British-Israel. Conco, kuyambila tili ana, ine, mlongosi wanga, mkulu wanga, komanso acibululu ena, tinali kuphunzitsidwa kuti Mulungu amakonda cabe mbadwa za ku Britain. Koma ine sin’nali kukhululupilila zimenezi, ndipo n’nali na njala yauzimu. Pamene n’nali na zaka 14, n’napita ku machechi ambili a m’dela lathu, monga ya Anglican, Baptist, komanso ya Seventh-day Adventist. Ngakhale n’conco, machechiwo sananithandize kudziŵa Mulungu.

Patapita nthawi, banja lathu linakukila kumzinda wa Sydney, kumene n’nakumana ndi Winston pamene anali kucita chuti kumeneko. Monga mmene wakambilapo kale, makambilano athu okhudza nkhani za cipembedzo anacititsa kuti iye ayambe kuphunzila Baibo na Mboni. Pambuyo pake, anayamba kunilembela makalata. M’makalatamo anali kukonda kulembamo malemba ambili. Kukamba zoona, paciyambi izi zinali kunidetsa nkhaŵa, mpaka kufika ponikwiyitsa nthawi zina. Koma m’kupita kwa nthawi, n’nazindikila kuti zimene anali kunilembela cinali coonadi.

Mu 1962, n’napita kukakhala kumzinda wa Adelaide, kufupi na kwawo kwa Winston. Iye anapanga makonzedwe akuti nizikhala na m’bale Thomas Sloman na mkazi wake Janice, amene kale anali kutumikila monga amishonale ku Papua New Guinea. Panthawiyo, n’nali na zaka 18 cabe. Banjalo linali kunisamalila mokoma mtima, ndipo linanithandiza kwambili mwauzimu. Conco, na ine n’nayamba kuphunzila Mawu a Mulungu, ndipo posapita nthawi n’nazindikila kuti napeza coonadi. Ine na m’bale Winston titakwatilana, nthawi yomweyo tinayamba utumiki wanthawi zonse. N’zoona kuti takumana na mavuto osiyana-siyana mu utumikiwu. Koma mavutowo atithandiza kukhala na mtima woyamikila kwambili ngale yamtengo wapatali ya coonadi imene tinapeza.

M’bale Winston, tiuzenkoni zokhudza ciyambi ca utumiki wanu.

Mapu yoonetsa maulendo a m’bale na mlongo Payne pa nchito yawo ya m’dela; masitampa a m’zisumbu zina; cisumbu ca Funafuti ku Tuvalu

A. Mapu yoonetsa maulendo amene tinayenda pamene tinali m’nchito ya m’dela

B. Masitampa a m’zisumbu zina. Zisumbu za Kiribati na Tuvalu, kale zinali kudziŵika kuti Gilbert na Ellice

C. Cisumbu cokongola ca Funafuti m’dziko la Tuvalu. Funafuti ni cimodzi mwa zisumbu zimene tinatumikilalo akalibe kutumizako amishonale

Patapita nthawi yocepa kucokela pamene tinakwatilana, Yehova anayamba kutipatsa mautumiki osiyana-siyana apadela. (1 Akor. 16:9) Mwayi woyamba wautumiki umene tinakhala nawo unali upainiya wanthawi zonse. M’bale Jack Porter na mkazi wake, ndiwo anatilimbikitsa kuyamba upainiya. Panthawiyo, m’baleyo ndiye anali woyang’anila dela wathu, koma tsopano tikutumikila naye m’komiti ya nthambi ya ku Australasia. Ine na Pam tinatumikila monga apainiya kwa zaka zisanu. Pamene n’nali na zaka 29, n’nauzidwa kuti nikatumikile monga woyang’anila dela pamodzi na mkazi wanga ku zisumbu za ku South Pacific, zimene panthawiyo zinali kuyang’anilidwa na nthambi ya ku Fiji. Zisumbu zimenezi zinali American Samoa, Samoa, Kiribati, Nauru, Niue, Tokelau, Tonga, Tuvalu, na Vanuatu.

M’masiku amenewo, anthu ena a m’zisumbu zimenezi anali kukayikila Mboni za Yehova. Conco, tinafunika kucita zinthu mosamala. (Mat. 10:16) Mipingo ya kumeneko inali ing’ono-ing’ono, moti m’mipingo ina, abale sanali kukwanitsa kutipezela malo ogona. Conco, tinali kusakila malo okhala kwa anthu ena m’midzi ya kumeneko, ndipo nthawi zonse anthuwo anali kutikomela mtima kwambili.

M’bale Winston, tiona kuti muli na cidwi kwambili na nchito yomasulila. Kodi cidwi cimeneci cinayamba bwanji?

M’bale Winston Payne akucititsa sukulu ya akulu ku Samoa

Nikucititsa sukulu ya akulu ku Samoa

Pamene tinali kutumikila pa pacisumbu ca Tonga, kunali tumabuku na tumathilakiti tocepa cabe m’citundu ca kumeneko cochedwa Tonga. Abale akapita muulaliki, pophunzitsa anthu Baibo, anali kucita kuseŵenzetsa buku la Cizungu la Coonadi Cimene Cimatsogolela ku Moyo Wamuyaya. Conco, pa sukulu ya akulu ya mawiki anayi, akulu atatu anadzipeleka kumasulila bukulo m’citundu ca Tonga, olo kuti sanali kucidziŵa bwino Cizungu. Mkazi wanga ndiye anali kutaipa zimene iwo anali kumasulila, ndipo atatsiliza, tinazitumiza ku nthambi ya ku America kuti akapulinte. Nchito yonse inatenga mawiki 8. Ngakhale kuti bukulo silinamasulidwe mwaukatswili kweni-kweni, linathandiza anthu ambili okamba citundu ca Tonga kuphunzila coonadi. Ine na mkazi wanga sindife omasulila, koma zimene zinacitika nthawiyo zinatithandiza kukhala na cidwi pa nchito yomasulila.

Mlongo Pam, kodi umoyo wa kuzisumbu unali wosiyana bwanji na umoyo wa ku Australia?

M’bale Winston na mlongo Pam Payne aimilila pafupi na basi, amodzi mwa malo awo ogona pamene anali m’nchito ya m’dela

Amodzi mwa malo athu ogona pamene tinali mu nchito ya m’dela

Unali wosiyana kwambili! Kuzisumbu zina tinali kuvutika na udzudzu, makoswe, kutentha, matenda, ndipo nthawi zina tinali kusoŵa cakudya. Komabe, tsiku lililonse m’madzulo tinali kutsitsimulidwa tikakhala m’kanyumba kathu kochedwa fale n’kumayang’ana kunyanja. Fale ni dzina la Cisamowa la kanyumba kaudzu kokhala ngati khumbi. Nthawi zina kukada madzulo, mitengo ya makokonati inali kuonekela bwino cifukwa ca kuwala kwa mwezi, ndiponso cithunzi-thunzi ca mweziwo cinali kuonekela panyanja. Panthawi zotsitsimula zimenezo, tinali kusinkha-sinkha na kupemphela, ndipo izi zinali kutithandiza kusumika maganizo athu pa zinthu zolimbikitsa osati zofooketsa.

Tinali kukonda ana. Iwo anali kutisangalatsa komanso anali kucita cidwi kwambili akaona ife azungu ocokela kudziko lina. Pamene tinali kucisumbu ca Niue, kamnyamata kena kanacita cidwi na mikono ya mwamuna wanga, imene inali na ceya cambili. Kanabwela n’kuyamba kusisita mkono wake, ndipo kenako kanati, “Koma muli na nthenga zabwino.” Mwacionekele, kamnyamatako kanali kasanaonepo munthu wokhala na mikono ya ceya cambili conco, ndipo sikanadziŵe mochulila.

Zinali kutimvetsa cisoni kuona mmene anthu anali kuvutikila cifukwa ca umphawi. Dela limene anali kukhala linali lokongola, koma kunalibe cithandizo cokwanila ca mankhwala, komanso madzi anali ocepa. Ngakhale n’conco, abale athu analibe nkhaŵa. Iwo anali atazoloŵela kukhala umoyo wotelo. Anali kukondwela kukhala na banja lawo, kukhala na malo olambilila, komanso kukhala na mwayi wotamanda Yehova. Citsanzo cawo cinatiphunzitsa kuika zinthu zofunika patsogolo muumoyo wathu, komanso kukhala na umoyo wosalila zambili.

Mlongo Pam, nthawi zina munali kufunika kudzipezela mwekha madzi, komanso kudziphikila mwekha cakudya m’dela limene umoyo unali wosiyana kwambili na kwanu. Kodi munakwanitsa bwanji kucita zimenezi?

Ku cisumbu ca Tonga, mlongo Pam akuwacha zovala poseŵenzetsa dishi na baketi

Mkazi wanga Pam akuwacha zovala tili pa cisumbu ca Tonga

Atate anga ananiphunzitsa mocitila zimenezi, ndipo nimawayamikila kwambili. Ananiphunzitsa zinthu zambili zofunika, monga kusonkha moto, kuphikila pa moto wa nkhuni, komanso kugwilitsila nchito mwanzelu zinthu zocepa zimene tili nazo. Pa nthawi ina tili ku Kiribati, tinali kukhala m’kanyumba kakang’ono kansungwi, ka mtenje wa udzu, ndipo pansi pake panali potsila na dothi. N’nakumba kadzenje m’nyumbayo kosonkhapo moto na kuphikilapo. Nkhuni zophikila zinali makoko a kokonati. Madzi n’nali kukatapa kucitsime pamodzi na azimayi ena a komweko. Tinali kukhala pamzela. Kuti atape madzi, azimayiwo anali kuseŵenzetsa kamtengo kakatali mamita aŵili, ndipo kutsogolo kwake anali kumangililako nthambo. Cinali kuoneka monga coŵedzela nsomba. Koma kothela kwa nthamboyo anali kuikako cikopo, osati mbedza. Mzimayi akafuna kutapa madzi, anali kuponya cipangizoco mwaluso n’kutukula kamtengoko mbali imodzi. Akatelo, cikopoco cinali kupendeka mbali imodzi, moti anali kukwanitsa kutapa madzi. N’nali kuganiza kuti n’zopepuka, mpaka pamene cinafika panga. N’naponya cipangizoco kambili ndithu, koma cikopo cinali kungochaya madzi n’kuyandama. Azimayiwo anayamba kuniseka. Atasiya kuniseka, mmodzi wa iwo ananithandiza. Nthawi zonse, anthu a kumeneko anali kutithandiza komanso kuticitila zinthu mokoma mtima.

Nonse aŵili munafika poukonda kwambili utumiki wanu wa pa zisumbuzi. Kodi mungatisimbileko zocitika zina zocititsa cidwi za kumeneko?

M’bale Winston: Zinatitengela kanthawi kuti tijaile miyambo ina ya kumeneko. Mwacitsanzo, nthawi zambili tikapita kukawacezela abale, anali kutipatsa cakudya conse cimene anali naco patsikulo. Malinga ndi mwambo wa kumeneko, iwo anali kuyembekezela kuti tidzasiyako cakudyaco. Koma poyamba sitinadziŵe zimenezi, moti tinali kudya cakudya conse cimene atipatsa, osasiyako! Titadziŵa zimenezo, tinayamba kuwasiilako. Abale amenewo anali kutimvetsetsa olo kuti tinali kulakwitsa zinthu zina. Ndipo pamene n’nali kutumikila monga woyang’anila dela, iwo anali kukondwela kwambili tikapita kukacezela mpingo wawo pambuyo pa miyezi 6 kapena kuposelapo. Panthawiyo, abale a kumeneko analibe mwayi woonana na abale a m’mipingo ina, kupatulapo ine na mkazi wanga.

M’bale Winston akutsogolela kagulu ka ulaliki ku cisumbu ca Niue; onse ali pa mahonda

Nikutsogolela kagulu ka ulaliki pa cisumbu ca Niue

Tikapita kukawacezela, zinali kupelekanso umboni wabwino kwa anthu a kumeneko. Anthu ambili a kumeneko anali kuganiza kuti abale athu anangodzipangila okha cipembedzo catsopano. Conco, pamene ine na mkazi wanga tinapita kukacezela abalewo, anthu a kumeneko anazindikila kuti abalewo anali m’cipembedzo codziŵika bwino, ndipo izi zinawacititsa cidwi kwambili.

Mlongo Pam: Cimodzi mwa zinthu zocititsa cidwi kwambili, n’zimene zinacitika pamene tinali kucezela mpingo wina waung’ono ku Kiribati. Mumpingo umenewo munali cabe mkulu mmodzi, dzina lake Itinikai Matera. Iye anacita zonse zotheka potisamalila. Tsiku lina anabwela kukationa, atanyamula basiketi imene munali dzila limodzi la nkhuku. Atafika anati: “Nakubweletselani mphatso iyi.” Panthawi imeneyo, dzila lankhuku linali mphatso yapadela. Mphatso yooneka ngati yaing’ono imeneyi, koma yoonetsa kuwoloŵa manja, inatikhudza mtima kwambili.

Patapita nthawi, mlongo Pam anakhala na pakati koma anapita padela. Mlongo Pam, kodi n’ciani cinakuthandizani kupilila vuto limeneli?

Mu 1973, pamene ine na amuna anga tinali kutumikila ku South Pacific, n’nakhala na pakati. Conco, tinabwelela ku Australia, ndipo patapita miyezi inayi, n’napita padela. Zinatipweteka mtima kwambili. M’kupita kwa nthawi, cisoni cinayamba kucepa, koma sicinatheletu mpaka pamene tinalandila magazini ya Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009. Nkhani ya “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” ya m’magaziniyo inali na funso lakuti, “Ngati mwana wabadwa wakufa, kodi pali ciyembekezo cakuti mwanayo adzauka?” Magaziniyo inatitsimikizila kuti nkhani imeneyi ili m’manja mwa Yehova, amene amacita zinthu mwacilungamo nthawi zonse. Iye adzathetsa mavuto ambili-mbili amene timakumana nawo m’dziko loipali, pamene adzalamula Mwana wake kuti ‘awononge nchito za Satana.’ (1 Yoh. 3:8) Nkhani ya m’magaziniyo inatithandizanso kukhala na mtima woyamikila kwambili “ngale” yamtengo wapatali ya coonadi imene ife atumiki a Yehova tili nayo. Kaamba ka ciyembekezo ca Ufumu cimene tili naco, timatonthozedwa ngakhale kuti timakumana na mavuto m’dziko loipali.

Patapita nthawi kucokela pamene tinatayikilidwa mwana, tinayambilanso utumiki wa nthawi zonse. Tinatumikila pa Beteli ya ku Australia kwa miyezi ingapo, ndipo pambuyo pake tinapitiliza kugwila nchito ya m’dela. Mu 1981, titatumikila kwa zaka zinayi ku madela akumidzi a ku New South Wales komanso mumzinda wa Sydney, anatiitananso kuti tikatumikile pa nthambi ya Australia. Panthawiyo, nthambi imeneyi inali kudziŵika na dzina limeneli, koma m’kupita kwa nthawi inayamba kuchedwa nthambi ya Australasia. Ndipo kucokela nthawiyo, takhala tikutumikila pa nthambiyi.

Mbale Winston, kodi kutumikila pa zisumbu za ku South Pacific kwakuthandizani pa utumiki wanu monga ciwalo ca Komiti ya Nthambi ya Australasia?

Inde, kwanithandiza m’njila zingapo. Coyamba, kwanithandiza cifukwa nthambi ya Australia inauzidwa kuti iziyang’anilanso nchito yathu ku zisumbu za American Samoa komanso Samoa. Cina, nthambi ya New Zealand anaiphatikiza na nthambi ya Australia. Tsopano gawo la nthambi ya Australasia liphatikizapo Australia, American Samoa, Samoa, Cook Islands, New Zealand, Niue, Timor-Leste, Tokelau, komanso Tonga. Ndipo nakhala na mwayi wokacezela abale na alongo athu m’zisumbu zimenezi monga woimila nthambi. Kutumikila pa zisumbu zimenezi limodzi na abale na alongo okhulupilika a kumeneko kwanithandiza kwambili pa utumiki wanga wa pano pa nthambi.

M’bale Winston na mlongo Pam Payne pa nthambi ya Australasia

M’bale Winston na mlongo Pam pa nthambi ya Australasia

Malinga na mmene zinthu zinayendela muumoyo wathu, ine na mkazi wanga Pam, tazindikila kuti si anthu acikulile cabe amene amafuna-funa Mulungu. Acicepele nawonso amafuna-funa “ngale . . . yamtengo wapatali” ya coonadi. Iwo amacita izi olo kuti ena m’banja lawo sacita cidwi na zinthu zauzimu. (2 Maf. 5:2, 3; 2 Mbiri 34:1-3) Kukamba zoona, Yehova ni Mulungu wacikondi amene amafuna kuti anthu onse, acikulile komanso acicepele akapeze moyo wosatha.

Pamene ine na mkazi wanga Pam tinayamba kufuna-funa Mulungu zaka zoposa 50 zapitazo, sitinadziŵe kuti kufuna-funa kumeneko kudzakhala na zotulukapo zanji. Ndithudi! Coonadi ca Ufumu, ni ngale ya mtengo wapatali kwambili! Ndipo ine na mkazi wanga, ndife otsimikiza mtima kugwilabe mwamphamvu ngale ya mtengo wapatali ya coonadi imeneyi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani