Zilengezo
February: Gaŵilani kalikonse ka tumabuku ta masamba 32 utu: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kapena kakuti Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu. Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo, m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yambitsani phunzilo la Baibo. March ndi April: Gaŵilani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo, m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yambitsani phunzilo la Baibo. May: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kweni-kweni Akulamulila Dziko? kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.
◼ Autilaini yatsopano ya nkhani ya Cikumbutso yakonzedwa ndipo caka cino ili ndi mutu wakuti “Yamikilani Zimene Kristu Wakucitilani!” Okamba nkhani ya Cikumbutso onse ayenela kugwilitsila nchito autilaini imeneyi kuyambila mu 2013.
◼ Nkhani yapadela ya panyengo ya Cikumbutso ca 2013 idzakhala ndi mutu wakuti “Kodi Imfa Ndiye Mapeto a Zonse?”