Maulaliki Acitsanzo
Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo Paciŵelu Coyamba mu August
“Pafupi-fupi munthu aliyense amapeza nthawi yopemphela. Ngakhale anthu amene sakhulupilila Mulungu amapemphela akakhala pa mavuto. Kodi muganiza kuti Mulungu amamvela mapemphelo onse?” Yembekezani ayankhe. Ndiyeno muonetseni nkhani ili patsamba lothela kucikuto kwa Nsanja ya Mlonda ya August 1, ndi kukambilana naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndipo ŵelengani naye lemba ngakhale limodzi pa malembawo. Kenako m’gaŵileni magazini ndi kupangana kuti mukabwelenso kudzakambilana naye funso lotsatila.
Cidziŵitso: Citsanzo ici ciyenela kucitika pa kukumana kokonzekela ulaliki pa August 3.
Nsanja ya Olonda August 1
“Tikucezela anthu mwacidule kaamba ka vuto limene ladetsa nkhawa anthu ambili, vuto limeneli ndi kuonelela zamalisece. Ambili amaona kuti kuonelela zamalisece kulibe vuto lililonse. Kodi inu muona bwanji? [Yembekezani yankho.] Yesu anakamba kuti tingadziŵe ngati cinthu n’cabwino mwa kuona zipatso zake. [Ŵelengani Mateyu 7:17.] Magazini iyi ionetsa cipatso cimene kuonelela zamalisece kumatulutsa. Ipelekanso njila zothandiza kuti munthu amasuke ku zamalisece.”
Galamukani! August
“Ambili a ife timafuna kukhala moyo wautali kwambili. Kodi muganiza kuti kupita patsogolo kwa sayansi kudzacititsa kuti tsiku lina tikakhale ndi moyo wosatha? [Yembekezani yankho.] Onani lonjezo locititsa cidwi ili. [Ŵelengani 1 Akorinto 15:26.] Koma kodi Mulungu adzakwanilitsa bwanji izi? Kodi adzagwilitsila nchito sayansi kapena njila ina? Ndipo n’cifukwa ciani timakalamba ndi kufa? Magazini iyi ionetsa mmene Baibo imayankhila mafunso awa.”