Athandizeni Kukhala ‘Okhazikika m’Cikhulupililo’
N’zosangalatsa kuona mmene Yehova amadalitsila nchito yosonkhanitsa, caka ciliconse anthu oposa 2,500 amabatizika. (Deut. 28:2) Nthawi zambili wophunzila akabatizika, wofalitsa amasiya kuphunzila naye ndi kuyamba kuphunzila ndi ena. Wophunzila nayenso angafune kusiya kuphunzila kuti azithela nthawi yoculuka mu ulaliki. Koma n’kofunika kuti ophunzila akhazikike m’cikhulupililo. Iwo ayenela ‘kuzikika’ ndi “kukhazikika m’cikhulupililo.” (Akol. 2:6, 7; 2 Tim. 3:12) Conco, wophunzila akabatizika, ayenela kupitilizabe kuphunzila mpaka kumaliza buku la Baibo Imaphunzitsa ndi lakuti Cikondi ca Mulungu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2011 patsamba 2.