UMOYO WACIKHRISTU
Kondwelani mu Ciyembekezo Canu
Ciyembekezo cili ngati nangula. (Aheb. 6:19) Cimatithandiza kuti cikhulupililo cathu cisawonongeke, ngati mmene ngalawa imawonongekela ndi cimphepo ca mkuntho panyanja. (1 Tim. 1:18, 19) Mphepo zamkuntho zingaphatikizepo kugwilitsidwa mwala, kutaikidwa cuma, matenda amgonagona [osacila msanga], imfa ya wokondedwa, kapena vuto lililonse loopseza cikhulupililo cathu.
Cikhulupililo na ciyembekezo zimatithandidza kuona bwino mphoto yathu yamtsogolo. (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 11:13, 26, 27) Conco, kaya ciyembekezo cathu n’ca kumwamba kapena padziko lapansi, tiyenela kucilimilila nthawi zonse mwa kusinkha-sinkha malonjezo ali m’Mau a Mulungu. Ndiyeno pamene mayeselo ativutitsa maganizo, tidzakhalabe acimwemwe.—1 Pet. 1:6, 7.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KONDWELANI NDI CIYEMBEKEZO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani Mose n’citsanzo cabwino cofunika kutengela?
Mitu ya mabanja ili na udindo wanji?
Ni nkhani ziti zimene mungakambilane pa Kulambila kwa Pabanja lanu?
Kodi ciyembekezo cingakuthandizeni bwanji kuyang’anizana ndi mayeselo mwacidalilo?
N’ciani cimene imwe muyembekezela mwacidwi m’tsogolo?