UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Cikhulupililo Canu m’Malonjezo a Yehova N’colimba Bwanji?
Yoswa na Solomo onse anatsimikizila kuti palibe mau amodzi amene Yehova analonjeza amene sanakwanilitsike. (Yos. 23:14; 1 Maf. 8:56) Zimene anthu aŵili odalilika amenewa anakamba ni umboni winanso waukulu umene umaticititsa kukhala na cikhulupililo.—2 Akor. 13:1; Tito 1:2.
Kodi Yehova anakwanilitsa bwanji malonjezo ake m’nthawi ya Yoswa? Tambani vidiyo yakuti “Palibe Ngakhale Mau Amodzi Omwe Sanakwanilitsidwe” pamodzi na banja lanu. Ndiyeno kambilanani mafunso aya: (1) Mungatengele bwanji cikhulupililo ca Rahabi? (Aheb. 11:31; Yak. 2:24-26) (2) Kodi citsanzo ca Akani cionetsa bwanji kuti kusamvela mwadala kumatsogolela kuciwonongeko? (3) Olo kuti amuna a ku Gibeoni anali asilikali, n’cifukwa ciani ananamiza Yoswa ndi kukhala pamtendele ndi Isiraeli? (4) Kodi mau a Yehova anakwanilitsika bwanji pamene mafumu asanu Aamori anaopseza Aisiraeli? (Yos. 10:5-14) (5) Kodi Yehova wakudalitsani bwanji cifukwa coika Ufumu na cilungamo cake patsogolo mu umoyo wanu?—Mat. 6:33.
Pamene tiganizila zonse zimene Yehova wacita, zimene akucita, na zimene adzacita, cikhulupililo cathu m’malonjezo ake cimalimba.—Aroma 8:31, 32.
Kodi cikhulupililo canu cili monga ca Yoswa?