July 17-23
EZEKIELI 18-20
Nyimbo 21 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kodi Yehova Akatikhululukila Macimo, Amawakumbukilanso?”: (10 min.)
Ezek. 18:19, 20—Munthu aliyense adzadziyankhila mlandu kwa Yehova pa zocita zake (w12 7/1 peji 18 pala. 2)
Ezek. 18:21, 22—Yehova ni wokonzeka kukhululukila olapa ndipo sawasungilanso cifukwa (w12 7/1 peji 18 pala. 3-7)
Ezek. 18:23, 32—Yehova amawononga oipa kokha akaona kuti salapa (w08 4/1 peji 8 pala. 4; w06 12/1 peji 27 pala. 11)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 18:29—N’cifukwa ciani Aisiraeli anayamba kuona Yehova molakwika? Nanga ise tingapewe bwanji kutengela zimenezo? (w13 8/15 peji 11 pala. 9)
Ezek. 20:49—N’cifukwa ciani anthu anaganiza kuti Ezekieli anali ‘kunena miyambi’? Pali cenjezo lanji kwa ise? (w07 7/1 peji 14 pala. 3)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 20:1-12
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) 1 Yoh. 5:19—Phunzitsani Coonadi. Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Gen. 3:2-5—Phunzitsani Coonadi. Yalani maziko a ulendo wotsatila. (Onani mwb16.08 peji 8 pala. 2.)
Nkhani: (6 mineti kapena kucepelapo) w16.05 32-CN—Mutu Wake: Kodi Mpingo Ungaonetse Bwanji Kukondwela pa Cilengezo Cakuti Cite Wabwezedwa?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Mumadziimbabe Mlandu?”: (10 min.) Kukambilana. Yambani ndi kutambitsa vidiyo yakuti Muzicilikiza Malamulo a Yehova—Muzikhululuka.
Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake (5 min.) Kukambilana nkhani yakuti: Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake? Yambani mwa kuliza mbali yakuti “Kodi inuyo mungatani?”
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 15 mapa. 9-17
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 38 na Pemphelo