September 18-24
DANIELI 1-3
Nyimbo 131 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Kukhala Wokhulupilika kwa Yehova Kumabweletsa Madalitso” (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Danieli.]
Dan. 3:16-20—Anzake a Danieli anacilimikabe poyesedwa kuti ataye cikhulupilililo cawo kwa Yehova (w15 7/15 peji 25 mapa. 15-16)
Dan. 3:26-29—Kukhulupilika kwawo kunatamanditsa Yehova ndipo kunawabweletsela madalitso w13 1/15 peji 10 pala. 13
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Dan. 1:5, 8—N’cifukwa ciani Danieli na anzake atatu anaona kuti kudya zakudya zabwino za mfumu kungawadetse? (it-2 peji 382)
Dan. 2:44—N’cifukwa ciani Ufumu wa Mulungu udzaphwanya maulamulilo a padziko, oimilidwa na fano? (w12 6/15 peji 17, bokosi; w01 10/15 peji 6 pala. 4)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Dan. 2: 31-43
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) Yes. 40:22— Phunzitsani Coonadi—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) Aroma 15:4—Phunzitsani Coonadi—Musiileni kakhadi kongenela pa JW. ORG.
Nkhani: (6 mineti kapena kucepelapo) w17.02 peji 29-30—Mutu Wake: Kodi Yehova Amapendelatu Mayeselo Amene Tingakwanitse Kuwapilila, Kenako N’kuwasankha Kuti Tikakumane Nawo?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Khalani Okhulupilika Pamene Mukuyesedwa”: (8 min.) Kukambilana.
“Khalanibe Okhulupilika Pamene M’bululu Wanu Wacotsedwa”: (7 min.) Kukambilana.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr “Cigawo 6-Kucilikiza Ufumu—Kumanga Malo Olambilila ndi Kupeleka Thandizo Pakacitika Ngozi,” nkhani 18, mapa. 1-8
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 101 na Pemphelo