November 27–December 3
NAHUMU 1–HABAKUKU 3
Nyimbo 129 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khalanibe Achelu ndi Okangalika Kuuzimu”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Nahumu.]
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Habakuku.]
Hab. 2:1-4—Kuti tikapulumuke tsiku la ciweluzo ca Yehova, tifunika ‘kuliyembekezela’ (w07 11/15 peji 10 mapa. 3-5
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Nah. 1:8; 2:6—Kodi Ninive anawonongedwa kothelatu motani? (w07 11/15 peji 9 pala. 2)
Hab. 3:17-19—Olo kuti tikumane na mavuto pali pano, kapena panthawi ya Aramagedo, ni cidalilo cotani cimene tiyenela kukhala naco? (w07 11/15 peji 10 pala. 10)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Hab. 2:15–3:6
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) hf—Yalani maziko a ulendo wobwelelako.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) hf—Kabukuka kanagaŵilidwa pa ulendo woyamba. Onetsani ulendo wobwelelako.
Nkhani: (6 mineti kapena kucepelapo)w16.03 peji 3-5—Mutu Wake: Kodi Mungathandize Ena mu Mpingo Wanu?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Khalanibe Achelu ndi Okangalika Zinthu Zikasintha mu Umoyo Wanu”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khalanibe Olimba Mwauzimu Pamene Mwasamuka.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 22 mapa. 1-7
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.) Dziŵitsani mpingo kuti m’mwezi wa December tidzagaŵila Galamukani! yakuti: “Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri?” Vidiyo ya ulaliki wake imene tidzakambilana pa msonkhano wotsatila idzaikidwa pa JW Library pa November 30. Ofalitsa afunika akayesetse kuigaŵila kwambili Galamukani! imeneyi.
Nyimbo 142 na Pemphelo