CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 6-7
Pitilizani Kufuna-funa Ufumu Coyamba
M’pemphelo lake la citsanzo, Yesu anaonetsa kuti zinthu zokhudzana na colinga ca Yehova na Ufumu wake, tifunika kuziika patsogolo mu umoyo wathu.
Dzina la Mulungu
Ufumu wa Mulungu
Cifunilo ca Mulungu
Cakudya ca lelo
Kukhululuka macimo
Kutilanditsa m’mayeselo
Zinthu zina zokhudzana ndi Ufumu zimene ningazipemphelele ni:
Kupita patsogolo kwa nchito yolalikila
Mzimu woyela wa Mulungu kuti uthandize amene akuzunzidwa
Dalitso la Mulungu pa nchito zomanga-manga kapena makampeni a ulaliki
Nzelu za Mulungu na mphamvu zake kuti zitsogolele amene amatitsogolela
Zina