CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 10-12
‘Mboni Ziŵili’ Zinaphedwa, Kenako Zinakhalanso na Moyo
11:3-11
‘Mboni Ziŵili’: Kagulu ka abale odzozedwa amene anali kutsogolela pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914
Kuphedwa: Pambuyo polalikila kwa zaka zitatu na hafu ‘atavala ziguduli,’ iwo anaphedwa pamene anamangiwa, cakuti sanathenso kugwila nchito zawo
Kukhalanso na moyo: Cakumapeto kwa zaka zitatu na hafu zophiphilitsila, iwo anakhalanso na moyo pamene anatulutsidwa m’ndende na kuyambanso kutsogolela pa nchito yolalikila