LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 February tsa. 7
  • Kodi Mumapindula na Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumapindula na Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 February tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumapindula na Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku?

Kodi pulogilamu yanu yauzimu imaphatikizapo kuŵelenga lemba la tsiku na ndemanga yake m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku? Ngati si conco, kodi mungaiphatikize pa pulogilamu yanu yocita zauzimu? Ambili amasanthula lemba la tsiku m’maŵa kuti aziliganizilapo pamene akugwila nchito za tsikulo. (Yos. 1:8; Sal. 119:97) Koma kodi mungacite ciani kuti muzipindula moŵilikiza na Lemba la tsiku? Muziŵelenga nkhani pamene pacokela vesilo m’Baibo kuti mudziŵe nkhani yonse. Yesani kuganizila nkhani ya m’Baibo imene igwilizana na mfundo imene yafotokozedwa m’lemba la tsiku. Ndiyeno, ganizilani mmene mungaseŵenzetsele mfundoyo mu umoyo wanu. Mukamalola Mawu a Mulungu kukutsogolelani popanga zosankha, mudzapindula kwambili.—Sal. 119:105.

Mabanja a Beteli pa dziko lonse, amasanthula Lemba la Tsiku pa nthawi ya cakudya ca m’maŵa. Ndipo m’zaka zaposacedwa, zambili mwa nkhani zimene timakambilana pokambilana lemba la tsiku zaikidwa pa JW Broadcasting® pa mbali yakuti MAPULOGILAMU NA ZOCITIKA ZINA. Kodi ni liti pamene munamvetselako nkhani zimenezi? Mwina nkhani zina zinakuthandizani kwambili. Mwacitsanzo, kodi citsanzo ca Loti cingakuthandizeni bwanji popanga zosankha?

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MUSAMAKONDE DZIKO (1Jo 2:15), PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi Kulambila kwa M’maŵa kumeneku kunazikidwa pa mfundo iti ya m’Baibo?

  • Pa nkhani ya Loti, kodi kukonda dziko kapena zinthu za m’dziko kuli na ngozi yanji?—Gen. 13:12; 14:12; 19:3, 12, 13, 24-26

  • Tingaonetse bwanji kuti timakonda Yehova osati dziko kapena zinthu za m’dziko?

Zithunzi: M’bale akuganizila lemba la tsiku na ndemanga yake tsiku lonse. 1. Pamene akuŵelenga, iye akuyelekezela m’maganizo mwake kuti akuona angelo akutulutsa Loti na banja lake mu mzinda wa Sodomu atamugwila dzanja. 2. Pamene akudya cakudya ca masana ku nchito, akupitiliza kuganizila zimene waŵelenga m’maŵa. 3. Ku nyumba madzulo popeteka vovala, iye akupitiliza kusinkha-sinkha pa zimene waŵelenga m’maŵa.

Kodi ningaonetse bwanji tsiku lonse kuti Mawu a Yehova ni ofunika kwa ine?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani