LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 March tsa. 15
  • Sankhani Mabwenzi Mwanzelu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Sankhani Mabwenzi Mwanzelu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Sankhani Anzanu Mwanzelu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Zocita za Munthu Mmodzi Zingapindulitse Ambili?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Sankhani Mabwenzi Okonda Mulungu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 March tsa. 15
Akazi acimoabu akunyengelela amuna aciisiraeli kuti awatsatile.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Sankhani Mabwenzi Mwanzelu

Zimene zinacitikila Aisiraeli m’cigwa ca Moabu, ni cenjezo kwa Akhristu lelolino. (1 Akor. 10:6, 8, 11) Aisiraeli amene anayamba kugwilizana na akazi aciwelewele komanso olambila mafano acimoabu, ananyengedwa mpaka kucita macimo aakulu. Izi zinabweletsa mavuto aakulu. (Num. 25:9) Nafenso timakhala pakati pa anthu osalambila Yehova, monga anzathu a kunchito, akusukulu, anansi athu, acibale athu, ndi anthu ena amene timadziŵana nawo. Kodi nkhani ya m’Baibo imeneyi itiphunzitsa ciani za kuopsa kopanga ubwenzi ndi anthu otelo?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZITSANZO ZOTICENJEZA MASIKU ANO—KAMBALI KAKE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Zitsanzo Zoticenjeza Masiku Ano—Kambali Kake.’ Zimiri akuuza Yamini na ena za akazi acimoabu.

    Ni maganizo olakwika ati amene Zimiri ndi anthu ena anauza Yamini?

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Zitsanzo Zoticenjeza Masiku Ano—Kambali Kake.’ Pinihasi akukambilana na Yamini.

    Kodi Pinihasi anamuthandiza bwanji Yamini kuona zinthu moyenela?

  • Kodi kucita zinthu mwaubwenzi na munthu wosakhulupilila n’kosiyana bwanji na kukhala naye pa ubwenzi?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kusamala posankha mabwenzi apamtima ngakhale mumpingo?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kuceza ndi anthu osawadziŵa bwino pamalo ocezela pa intaneti?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani