January 10-16
OWERUZA 17-19
Nyimbo 88 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kusamvela Malamulo a Mulungu Kumabweletsa Mavuto”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Ower. 19:18—Pa vesiyi, n’cifukwa ciani dzina lakuti Yehova linaikidwamo mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso mu 2013? (w15 12/15 11 ¶6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Ower. 17:1-13 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Wobwelelako: Mulungu Amasamala za Ife—Yer. 29:11. Nthawi iliyonse vidiyo ikaima, inunso iimitseni na kufunsa omvetsela mafunso amene aonekela mu vidiyo.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 3) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 6)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako gaŵilani kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, na kuyambitsa phunzilo la Baibo m’phunzilo 01. (th phunzilo 13)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Mvela Makolo Ako: (Mph. 10) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi munawasankhilatu. Afunseni kuti: Kodi Kalebe anacita ciani posamvela amayi ake? Kodi anacita ciani pokonza zimene analakwitsa? N’cifukwa ciani iwe uyenela kumvela makolo ako?
Zofunikila za Mpingo: (Mph. 5)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 72
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 37 na Pemphelo