UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Njila Zitatu Zoonetsela Kuti Timadalila Yehova
Davide anagonjetsa Goliyati cifukwa codalila Yehova. (1 Sam. 17:45) Yehova amafuna kuonetsa mphamvu zake pothandiza atumiki ake onse. (2 Mbiri 16:9) Tingaonetse bwanji kuti timadalila thandizo limene Yehova amapeleka m’malo modalila cidziŵitso cimene tili naco na maluso athu? Nazi njila zitatu:
Muzipemphela kaŵili-kaŵili. Osangopempha cabe cikhululukilo mukalakwitsa cinacake, koma muzipemphanso mphamvu pamene mwayang’anizana na mayeselo. (Mat. 6:12, 13) Osangopempha dalitso la Yehova pa zisankho zimene mwapanga kale, koma muzipemphanso citsogozo cake na nzelu zake musanapange zisankho.—Yak. 1:5
Khalani na cizoloŵezi coŵelenga Baibo na kuiphunzila. Muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Muzisinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo, na kugwilitsila nchito zimene mwaphunzila. (Yak. 1:23-25) Muzikonzekela ulaliki m’malo mongodalila luso lanu. Pindulani mokwanila na misonkhano ya mpingo mwa kukonzekelelatu pasadakhale.
Muziyendela limodzi na gulu la Yehova. Dziŵani malangizo atsopano a gulu, ndipo atsatileni mwamsanga. (Num. 9:17) Mvelani akulu pamene akupeleka uphungu na malangizo.—Aheb. 13:17
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PALIBE CIFUKWA COCITILA MANTHA NA CIZUNZO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
• Ni zinthu ziti zimene abale na alongo anali kuopa?
• Cinawathandiza n’ciani kuthetsa mantha awo?