LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsa. 13
  • Mayeso Onse Ali na Mapeto Ake

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mayeso Onse Ali na Mapeto Ake
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Khalanibe Oleza Mtima
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kodi Mudzayembekezela Moleza Mtima?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Yembekezelani Yehova Moleza Mtima
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 March tsa. 13
Zithunzi: Cithunzi coonetsa zocitika za m’vidiyo yakuti “Anthu Ogwilizana M’dziko Logaŵikana.” 1. Gulu la abale na alongo acikuda lili pa msonkhano wadela. 2. Kagulu ka akulu aciyela komanso acikuda pamodzi na azikazi awo akujambulitsa cithunzi. 3. Alongo aŵili osiyana misinkhu komanso mtundu akucitila pamodzi ulaliki wapoyela.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mayeso Onse Ali na Mapeto Ake

Mayeso angatilefule mosavuta maka-maka ngati akhalitsa. Davide anadziŵa kuti ciyeso cake cocokela kwa Mfumu Sauli cidzatha m’kupita kwa nthawi, ndipo adzakhala mfumu monga mmene Yehova analonjezela. (1 Sam. 16:13) Cikhulupililo cake Davide cinam’thandiza kukhala woleza mtima na kuyembekezela Yehova.

Tikamayesedwa, mwina tingakwanitse kuthetsa vuto lathu cifukwa ca kucita zinthu mocenjela, kudziŵa zinthu, kapena cifukwa cokhala woganiza bwino. (1 Sam. 21:12-14; Miy. 1:4) Komabe, mavuto ena sangathe ngakhale kuti tacita zonse zotheka mogwilizana na mfundo za m’Baibo. Zikatelo, tiyenela kukhala oleza mtima na kuyembekezela Yehova. Posacedwa, iye adzathetsa mavuto athu onse, ndipo “adzapukuta misozi yonse” m’maso mwathu. (Chiv. 21:4) Kaya mavuto athu athe cifukwa cakuti Yehova waloŵelelapo kapena kaamba ka zifukwa zina, cimene sitikayikila n’cakuti: Mayeso onse ali na mapeto ake. Mfundo imeneyi ingatitonthoze.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OGWILIZANA M’DZIKO LOGAŴIKANA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Ni zopinga zotani zimene Akhristu ena anakumana nazo kum’mwela kwa dziko la America?

  • Kodi anaonetsa bwanji kuleza mtima na cikondi?

  • Kodi anacita ciani kuti apitilize kuika maganizo awo pa “zinthu zofunika kwambili”?—Afil. 1:10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani