LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsa. 15
  • Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Anu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Anu?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Athu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kodi Yehova Adzayankha Mapemphelo Anga?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 July tsa. 15
Mlongo akupemphela, ndipo Baibo ili patebulo patsogolo pake.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Anu?

M’Baibo muli zitsanzo zambili za mapemphelo amene Yehova anayankha. Pamene atumiki a Mulungu anaona kuti iye wamva nkhawa zawo na kuwathandiza, mosakayikila cikhulupililo cawo cinalimba. Cotelo, ni bwino kuti popeleka mapemphelo athu, tizichula zinthu mosapita m’mbali na kuyesetsa kuona mmene Yehova watiyankhila. Komabe, tiyenela kukumbukila kuti yankho la Yehova lingakhale losiyana na zimene tinapempha, kapena angaticitile zambili kuposa zimene tinapempha. (2 Akor. 12:7-9; Aef. 3:20) Kodi Yehova angacite ciyani poyankha mapemphelo athu?

  • Angatipatse mphamvu, kutitonthoza, na kulimbitsa cikhulupililo cathu kuti tikwanitse kupilila mavuto amene takumana nawo. —Afil. 4:13

  • Angatipatse nzelu kuti tikwanitse kupanga zisankho zabwino.—Yak. 1:5

  • Angalimbitse zokhumba zathu na kutipatsa mphamvu kuti ticitepo kanthu.—Afil. 2:13

  • Angatithandize kukhala osatekeseka pamene tili na nkhawa.—Afil. 4:6, 7

  • Angasonkhezele ena kuti atithandize pa zosowa zathu kapena kutilimbikitsa.—1 Yoh. 3:17, 18

  • Angapeleke thandizo kwa anthu amene timawapemphelela.—Mac. 12:5, 11

ONELELANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA NI “WAKUMVA PEMPHELO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi nkhani ya M’bale Shimizu ingatilimbikitse bwanji ngati timalephela kucita zambili cifukwa ca matenda?

  • Tingatengele bwanji citsanzo ca M’bale Shimizu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani