Yophunzila
JANUARY 2022
NKHANI ZOPHUNZILA: FEBRUARY 28–APRIL 3, 2022
© 2021 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
LEMBA LA CAKA CA 2022:
“Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.”—SAL. 34:10
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika pa dziko lonse lapansi. Nchito imeneyi timaiyendetsa na zopeleka zaufulu. Kuti mupange copeleka, pitani pa donate.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
Pa cisautso cacikulu, gulu la nkhondo la Gogi wa Magogi lidzatiukila m’nyumba zathu. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yesu na angelo ake adzaona zimenezo, ndipo adzatithandiza (Onani nkhani yophunzila 1, ndime 13)