Yophunzila
FEBRUARY 2022
NKHANI ZOPHUNZILA: APRIL 4–MAY 1, 2022
© 2021 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika pa dziko lonse lapansi. Nchito imeneyi timaiyendetsa na zopeleka zaufulu. Kuti mupange copeleka, pitani pa donate.jw.org.
Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kusiyapo ngati taonetsa ina. Komabe, ena mwa masipeling’i a Cinyanja m’magazini ino tatsatila malamulo a m’buku lakuti A Unified Standard Orthography for South-Central African Languages.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
Akhristu a ku Yudeya anaoloka mtsinje wa Yorodano n’kuthaŵila ku Pela. Aja amene anatsogola kufika akugaŵila zakudya Akhristu anzawo amene angofika kumene (Onani nkhani yophunzila 9, ndime 13)