LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w22 June tsa. 29
  • Kodi Mudziŵa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudziŵa?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
w22 June tsa. 29

Kodi Mudziŵa?

Kodi Aroma anali kulola munthu wopacikidwa pa mtengo, monga Yesu, kuti mtembo wake uikidwe m’manda?

Ophunzila a Yesu akutsitsa mtembo wake pa mtengo wozunzikilapo, na kuukulunga na nsalu.

AMBILI amadziŵa kuti Yesu anapacikidwa pakati pa apandu aŵili. (Mat. 27:35-38) Koma anthu ena amaona kuti zimene Baibo imakamba zakuti mtembo wa Yesu unakonzedwa na kuikidwa m’manda acikumbutso, si zolondola.—Maliko 15:42-46.

Ena otsutsa Mauthenga Abwino, amakayikila zakuti zinali zololeka kuti munthu wopacikidwa pa mtengo mtembo wake uikidwe m’manda olemekezeka. Iwo amati n’kutheka kuti anthu opacikidwa amene anali kucita zaupandu sanali kucitilidwa ulemu woika mtembo wawo m’manda. Katswili wina dzina lake Ariel Sabar, polemba m’magazini yochedwa Smithsonian, anafotokoza cifukwa cake anthu ena anali na maganizo aconco. Anati: “Kupacikidwa pa mtanda cinali cilango ca anthu ocita zaupandu, ndipo akatswili amakamba kuti n’kulakwa kuganiza kuti Aroma anali kulemekeza anthuwo mwa kuika mitembo yawo m’manda.” Aroma anali na colinga conyazitsa munthu amene wapezeka na mlandu wocita zaupandu. Conco, nthawi zambili mitembo ya anthu otelo anali kuisiya pa mtengo kuti idyedwe na nyama zakuchile. Pambuyo pake, mafupawo anali kungowaponya m’dzenje la manda a anthu wamba.

Ngakhale n’telo, ofukula za m’matongwe, anapeza zosiyana zokhudza mafupa a Ayuda ena amene anaphedwa. Mu 1968, anapeza mafupa a munthu wina amene anapacikidwa pa mtengo m’zaka za zana loyamba. Mafupawo anawapeza m’bokosi m’manda acikumbutso a banja la Ciyuda pafupi na mzinda wa Yerusalemu. Pamafupawo panali fupa la kadendene. Fupalo linali lokhomedwa pa thabwa na msomali wotalika masentimita 11.5. Sabar anati: “Fupa la kadendenelo linali la munthu wochedwa Yehochanan, ndipo linapeleka umboni woonetsa kuti nkhani ya m’Mauthenga Abwino yonena za kuikidwa m’manda acikumbutso kwa Yesu ingakhale yoona.” N’zoonekelatu kuti “fupa la kadendene la Yehochanan ni citsanzo ca munthu wa m’nthawi ya Yesu amene anapacikidwa pa mtengo. Koma Aroma analola kuti iye aikidwe m’manda motsatila mwambo wa Ayuda.”

Anthu akali na maganizo osiyana-siyana za mmene Yesu anam’pacikila, malinga na zimene fupa la kadendene la Yehochanan linaonetsa. Koma mfundo yoonekelatu ni yakuti, apandu ena amene anali kuphedwa mocita kupacikidwa pa mtengo, mitembo yawo inali kuikidwa m’manda, osati mafupa awo okha ayi. Mwacionekele, zimene Baibo imakamba zakuti mtembo wa Yesu unaikidwa m’manda acikumbutso n’zolondola. Umboni umene unapezeka utsimikizila zimene Baibo imakamba.

Koma cofunika kwambili n’cakuti, Yehova anali atanenelatu kuti Yesu adzaikidwa m’manda a munthu wolemela, ndipo palibe cikanalepheletsa mawu a Mulungu kukwanilitsidwa.—Yes. 53:9; 55:11.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani