ZIMENE MUNGACITE PA PHUNZILO LA INU MWINI
Khalanibe Maso mwa Kuŵelenga Baibo Mwakhama
Ŵelengani Danieli 9:1-19 kuti mudziŵe kufunika koŵelenga Baibo mwakhama.
Mvetsani nkhani yonse. Ni zinthu ziti zimene zinali zitangocitika kumene? Nanga zinamukhudza bwanji Danieli? (Dan. 5:29–6:5) Mukanamva bwanji mukanakhala Danieli?
Kumbani mozamilapo. Ni “mabuku opatulika” ati amene Danieli ayenela kuti anali kuŵelenga? (Dan. 9:2, mawu a m’munsi; w11 1/1 22 ¶2) N’cifukwa ciyani Danieli anavomeleza macimo ake komanso a mtundu wa Isiraeli? (Lev. 26:39-42; 1 Maf. 8:46-50; dp 182-184) Kodi pemphelo la Danieli lionetsa bwanji kuti anali kukonda kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama?—Dan. 9:11-13.
Onani maphunzilo amene mutengapo. Dzifunseni kuti:
‘Ningapewe bwanji kuceutsidwa na zocitika za m’dzikoli?’ (Mika 7:7)
‘Ningapindule bwanji nikamaŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama mmene Danieli anali kucitila?’ (w04 8/1 12 ¶17)
‘Ni nkhani ziti zimene ningaŵelenge pa phunzilo la ine mwini zimene zinganithandize ‘kukhalabe maso’?’ (Mat. 24:42, 44; w12 8/15 5 ¶7-8)