ZIMENE MUNGACITE PA KUŴELENGA KWANU
Anthu Okhulupilika Amasunga Malonjezo Awo
Ŵelengani Oweruza 11:30-40 kuti muphunzile ku cocitika ca Yefita na mwana wake wamkazi pa nkhani yosunga malonjezo.
Mvetsani nkhani yonse. Kodi Aisiraeli okhulupilika anali kuwaona bwanji malonjezo awo kwa Yehova? (Num. 30:2) Kodi Yefita na mwana wake wamkazi, anaonetsa bwanji kuti anali na cikhulupililo mwa Yehova?—Ower. 11:9-11, 19-24, 36.
Kumbani mozamilapo. Kodi Yefita analonjeza ciyani kwa Yehova? Nanga anatanthauza ciyani pamene anapanga lonjezolo? (w16.04 7 ¶12) Ni zinthu ziti zimene Yefita na mwana wake anadzimana kuti akwanilitse lonjezo lake? (w16.04 7-8 ¶14-16) Kodi ni malonjezo otani amene Akhristu angapange masiku ano?—w17.04 5-8 ¶10-19.
Onani zimene muphunzilapo. Dzifunseni kuti:
‘N’ciyani cinganithandize kusunga lonjezo langa la kudzipatulila?’ (w20.03 13 ¶20)
‘Kodi ningadzimane zinthu ziti kuti nicite zambili potumikila Yehova?’
‘N’ciyani cinganithandize kusunga lonjezo langa lokhalabe wokhulupilika kwa mnzanga wa mu ukwati?’ (Mat. 19:5, 6; Aef. 5:28-33)