Zamkati
January 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MLUNGU WA FEBRUARY 29, 2016–MARCH 6, 2016
Kodi lemba la caka ca 2016 ndi liti? Nanga tifunika kuganizila ciani tikamaona lembali caka cino? Nkhani iyi itithandiza kudziŵa zimene tingacite kuti tipindule ndi lemba la caka cino.
MLUNGU WA MARCH 7-13, 2016
9 Muzilimbikitsidwa ndi Mphatso ya Mulungu Yosatheka Kuifotokoza
Yehova watipatsa “mphatso yake yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) Kodi mphatso imeneyi n’ciani? Nanga imatilimbikitsa bwanji kutengela Kristu Yesu, kukonda abale athu, ndi kuwakhululukila ndi mtima wonse? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa. Ifotokozanso zinthu zina zimene tingacite pa nyengo ya Cikumbutso.
MLUNGU WA MARCH 14-20, 2016
14 Mzimu Umacitila Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu
MLUNGU WA MARCH 21-27, 2016
Nkhani ziŵilizi zifotokoza mmene munthu amadziŵila kuti wasankhidwa kuti akakhale kumwamba ndiponso cimene cimacitika munthuyo akadzozedwa. Tikambilananso mmene odzozedwa ayenela kudzionela ndi mmene ife tiyenela kumvela tikaona kuti ciŵelengelo ca anthu amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso cikukwela.
MLUNGU WA MARCH 28, 2016–APRIL 3, 2016
27 Kugwila Nchito ndi Mulungu—Kumabweletsa Cimwemwe
Nthawi zonse, Yehova wakhala akupatsa ena mwai wogwila naye nchito pokwanilitsa colinga cake. Iye amafuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi, ndipo watipatsa mwai wogwila naye nchitoyi. Nkhani imeneyi ikufotokoza cifukwa cake kugwila nchito ndi Mulungu kumatibweletsela cimwemwe cacikulu.
CITHUNZI CA PACIKUTO:
MADAGASCAR
Mpainiya akuŵelengela Baibulo munthu amene akuyendetsa ngolo mumsewu wa pakati pa mitengo ya Baobab ku Morondava, m’dziko la Madagascar
OFALITSA
29,963
MAPHUNZILO A BAIBULO
77,984
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO