LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g18 na. 1 tsa. 3
  • Mmene Mungaipezele

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungaipezele
  • Galamuka!—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Acimwemwe ni Anthu Amene Amatumikila “Mulungu Wacimwemwe”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Zamkati
    Galamuka!—2018
Galamuka!—2018
g18 na. 1 tsa. 3
Mwamuna ayenda pa njila

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Mmene Mungaipezele

KODI MUMAONA KUTI NDIMWE MUNTHU WACIMWEMWE? Ngati n’conco, n’ciani cimakucititsani kukhala wacimwemwe? Kodi ni banja lanu, nchito yanu, kapena cipembedzo canu? Mwina muyembekezela cinthu cina cimene cingakupatseni cimwemwe, monga kutsiliza sukulu, kupeza nchito yabwino, kapena kugula motoka yanyowani.

Anthu ambili amapeza cimwemwe akakwanilitsa colinga cawo, kapena akagula cinthu cimene anali kufuna. Koma kodi cimwemwe cimene amapeza cimakhala cokhalitsa? Nthawi zambili cimakhala ca kanthawi kocepa, zimene zingakhale zokhumudwitsa.

Cimwemwe cimatanthauza kukhala na mtendele wamumtima umene umakhalapo nthaŵi zonse. Munthu wacimwemwe amakhala wokhutila mumtima, komanso wosangalala, ndipo mwacibadwa amalaka-laka kuti mtendele wamumtima upitilize.

Ndiponso, popeza kuti cimwemwe ni mkhalidwe wofunika kupitilizabe, uli ngati ulendo, osati kumene ukupita. Conco, m’malo mokamba kuti, “n’zakhala na cimwemwe . . . ” tifunika kukamba kuti nili na cimwemwe.

Kuti mucimvesetse cimwemwe, ganizilani za thanzi labwino. Kodi n’ciani cimatithandiza kukhala na thanzi labwino? Ni kudya vakudya vopatsa thanzi, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kukhala na makhalidwe abwino. Mofananamo, kuti tikhale na cimwemwe tiyenela kukhala na makhalidwe abwino, na kutsatila mfundo zabwino mu umoyo wathu.

Kodi ni mfundo ziti kapena makhalidwe ati amene tiyenela kukhala nawo kuti tipeze cimwemwe? Pali makhalidwe ambili ofunika, koma otsatilawa ni othandiza kwambili:

  • KUKHUTILA KOMANSO KUPATSA

  • THANZI LABWINO NA KUPILILA

  • CIKONDI

  • KUKHULULUKA

  • COLINGA CA MOYO

  • CIYEMBEKEZO

Buku lodalilika kwambili la malangizo anzelu limati: “Odala [acimwemwe] ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njila zawo.” (Salimo 119:1) Manje tiyeni tikambilane mmene tingapezele njila yotithandiza kupeza cimwemwe.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani