LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g18 na. 2 tsa. 10
  • 7 Makhalidwe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 7 Makhalidwe
  • Galamuka!—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE AMATANTHAUZA
  • CIFUKWA CAKE NI OFUNIKA
  • ZIMENE MUNGACITE
  • Kufunika kwa Makhalidwe Abwino
    Galamuka!—2019
  • Mmene Ambili Amasankhila Zocita
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
Galamuka!—2018
g18 na. 2 tsa. 10
Tate na mwana aseŵenzetsa kampasi kuti adziŵe kopita

Makhalidwe abwino ali monga kampasi yodalilika, angathandize mwana wanu kuyenda panjila yoyenela

KWA MAKOLO

7 Makhalidwe

ZIMENE AMATANTHAUZA

Makhalidwe amaphatikizapo mfundo zimene munthu amasankha kuyendela mu umoyo. Mwacitsanzo, kodi mumayesetsa kukhala oona mtima m’zinthu zonse? Ngati n’conco, ndiye kuti mwacionekele mukufuna kukhomeleza khalidwe limeneli mwa ana anu.

Makhalidwe abwino angaphatikizeponso kugwila nchito mwakhama, kukhala acilungamo na kuganizila ena. Nthawi yabwino imene munthu angakhale na makhalidwe amenewa ni pamene ali wamng’ono.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.

CIFUKWA CAKE NI OFUNIKA

Makhalidwe abwino ni ofunika m’nthawi ino imene zipangizo zamakono zili paliponse. “Mwana angaphunzile makhalidwe oipa panthawi iliyonse, kaya ni pa foni kapena pa tabuleti. Nthawi zina ana athu angakhoza kumatamba zinthu zosayenela ali pafupi na ise!” Anakamba conco mayi wina dzina lake Karyn.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Anthu okhwima mwauzimu . . . amene pogwilitsa nchito mphamvu zawo za kuzindikila, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.”—Aheberi 5:14.

Makhalidwe ena abwino ofunika. Amenewa angaphatikizepo kupatsa ena ulemu m’zinthu zing’ono-zing’ono monga kukamba kuti “conde,” na “zikomo,” komanso kuganizila ena. Masiku ano ambili alibe khalidwe limeneli, ndipo amaona zipangizo kukhala zofunika kuposa anthu.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inuyo muwacitile zomwezo.”—Luka 6:31.

ZIMENE MUNGACITE

Muziwauza mfundo zanu za makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, kafuku-fuku aonetsa kuti kaŵili-kaŵili acicepele amapewa kugonana asanaloŵe m’cikwati ngati aphunzitsidwa momveka bwino kuipa kwa khalidwe limeneli.

CINANSO CIMENE MUNGACITE: Mukamvela nkhani ina yake imene yangocitika kumene, pezelamponi mwayi wophunzitsa ana anu mfundo za makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, ngati pa nyuzi pali nkhani za kuphana, mungakambe kuti: “Koma anthu ni ankhanza kwambili. Kodi uganiza kuti n’cifukwa ciani anthu ni ankhanza conco?”

“N’zovuta kwambili kuti ana acite coyenela ngati sadziŵa kusiyanitsa cabwino na coipa.”—Brandon.

Muziwaphunzitsa makhalidwe abwino. Olo ana ang’ono-ang’ono angaphunzile kukamba kuti “conde” na “zikomo.” Angaphunzilenso kukhala woganizila ena. “Ngati ana aphunzitsidwa kuganizila ena m’banja, ku sukulu, komanso m’dela lawo, amakhala ofunitsitsa kucitila ena zinthu mokoma mtima.” Imakamba conco buku yakuti, Parenting Without Borders.

CINANSO CIMENE MUNGACITE: Muzipatsa ana anu nchito za pakhomo kuti aphunzile kutumikila ena.

“Ngati ana athu ajaila kugwila nchito za pakhomo akali pa nyumba pathu, sadzavutika akadzayamba kudzikhalila. Cifukwa adzakhala atazoloŵela kale kugwila nchito.”—Tara.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani