Mawu Oyamba
Aliyense wa ife amakhudzidwa na mavuto aakulu monga matenda, ngozi, matsoka a zacilengedwe, kapena zaciwawa.
Anthu amafuna kudziŵa cifukwa cake timavutika.
Ena amakamba kuti mavuto amabwela cifukwa zinalembedwelatu, conco amaona kuti palibe kweni-kweni zimene tingacite kuti tiwapewe.
Enanso amakamba kuti timavutika cifukwa ca zina zimene tinacita kumbuyoku mu umoyo uno, kapena mu umoyo wina tisanamwalile na kubadwanso.
Tsoka likacitika, anthu amakhala na mafunso ambili.