LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 2 masa. 10-12
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Cikwati Canu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Cikwati Canu?
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA
  • ZIMENE MUNGACITE
  • ‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • 3 Kulemekezana
    Galamuka!—2018
  • 1 Kukhulupilika
    Galamuka!—2018
Galamuka!—2021
g21 na. 2 masa. 10-12
Mwamuna amene ali ku eyapoti akukambilana pa foni na mkazi wake amene ali kunyumba, ndipo akuonana pokambilanapo.

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Cikwati Canu?

Ngati mwamuna na mkazi wake amaseŵenzetsa bwino zipangizo zamakono, zingawathandize kulimbitsa mgwilizano wawo. Mwacitsanzo, zingawathandize kuti azikwanitsa kukambilana nthawi iliyonse pa tsiku.

Komabe, anthu ena amene ali pabanja amalola zipangizo zamakono . . .

  • kuwawonongela nthawi yoceza kapena yocitila zinthu pamodzi.

  • kuwapangitsa kuseŵenza pa nthawi imene safunikila kutelo.

  • kuwapangitsa kuyamba kukayikilana, ngakhalenso kukhala osakhulupilika kwa wina na mnzake.

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

Mwamuna na mkazi wake ali gone pabedi usiku, ndipo aliyense wa iwo akuseŵenzetsa foni yokhala na intaneti.

PAMENE MULI LIMODZI

Mwamuna wina dzina lake Michael anati: “Nthawi zina ngati ine na mkazi wanga tili pamodzi, iye amangokhala monga kuti ‘palibe.’ Amatangwanika kuyang’ana zinthu pa foni yake, n’kumakamba kuti ‘Sin’napeze nthawi yoziona izi.’” Mwamuna winanso dzina lake Jonathan anakamba kuti “zinthu zikakhala conco, mwamuna na mkazi amene ali pamodzi angaone kuti ni otalikilana kwambili.”

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi nimakonda kukamba pa foni kapena kutumila anthu mameseji pa nthawi yoyenela kuceza na mkazi kapena mwamuna wanga?—AEFESO 5:33.

NCHITO

Anthu ena amagwila nchito zimene zimafuna kuti aziyankha mafoni kapena mameseji nthawi iliyonse, ngakhale usiku. Koma ngakhale anthu amene nchito yawo si yopanikiza kwambili conco, nthawi zina zingawavute kuleka kucita zinthu za kunchito akakhala panyumba. Mwamuna wina, dzina lake Lee anati: “Kunchito akanitumila foni kapena meseji pa nthawi imene n’napatula kuti niziceza na mkazi wanga, zimanivuta kungoinyalanyaza.” Komanso mkazi wina, dzina lake Joy anati: “Nimaseŵenzela panyumba. Conco, nthawi zonse nchito imakhala pafupi. Nimafunika kudziletsa kuti nizikwanitsa kugaŵa bwino nthawi yoseŵenza na kucita zinthu zina.”

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumamvetsela mwachelu pamene mnzanu wa m’cikwati akukamba nanu?—LUKA 8:18.

KUKHULUPILIKA

Pa kufufuza kwina kumene kunacitika, anthu ambili amene anafunsidwa anakamba kuti anakanganapo na mnzawo wa m’cikwati cifukwa ca zimene wina wa iwo anali kuika pa masamba a mcezo a pa intaneti. 10 pelesenti ya amene anafunsidwa anavomeleza kuti anaikako zinthu pa intaneti, zimene sanafune kuti mnzawo azidziŵe kapena kuziona.

Mpake kuti anthu ena amakamba kuti masamba a mcezo a pa intaneti ni “bwalo lochelapo mabomba owonongela mabanja” kapenanso kuti ni “nthumwi ya cigololo.” Conco n’zosadabwitsa kuti maloya a nkhani za cisudzulo amakamba kuti, masamba a mcezo a pa intaneti amapangitsa mabanja ambili kutha.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi mumabisa kwa mnzanu wa m’cikwati zimene mumakambilana na munthu wina amene si mkazi kapena mwamuna wanu?—MIYAMBO 4:23.

ZIMENE MUNGACITE

DZIIKILENI MALILE

Munthu amene amanyalanyaza kudya sangakhale na thanzi labwino. Mofananamo, munthu amene amanyalanyaza kupatula nthawi yoceza kapena kucitila zinthu pamodzi na mnzake wa m’cikwati, sangakhale na cikwati colimba.—Aefeso 5:28, 29.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”—AFILIPI 1:10.

Pa malingalilo ali m’munsimu, kambilanani amene mufuna kuwaseŵenzetsa, kapena lembani malingalilo anu amene angathandize kuti zipangizo zamakono zisasokoneze cikwati canu.

  • Kudyela pamodzi cakudya, ngakhale kamodzi cabe pa tsiku

  • Kuika nthawi imene simuziseŵenzetsa zipangizo zanu

  • Kupanga nthawi yakuti mukaciteko zinthu zinazake zosangalatsa pamodzi

  • Ngati ni usiku, kuika mafoni na matabuleti anu patali na kumene mumagona

  • Kupatula mphindi 15 tsiku lililonse kuti muziceza popanda kukhala na foni kapena cipangizo cina pafupi

  • Kuika nthawi yoleka kuseŵenzetsa intaneti tsiku lililonse

ZIMENE MWAMUNA NA MKAZI WAKE ANGAKAMBILANE

Ganizilani mafunso otsatilawa aliyense payekha-payekha. Pambuyo pake, kambilanani mayankho ake na mnzanu.

  • Kodi zipangizo zamakono mungaziseŵenzetse bwanji kuti mulimbitse cikwati canu?

  • Kodi muona kuti zipangizo zamakono zimakuwonongelani nthawi yoceza na kucitila zinthu pamodzi?

  • Muona kuti ni zinthu ziti zimene imwe na mnzanu muyenela kuwongolela?

  • Kodi mumakonda kucitabe zinthu za kunchito mukabwela kunyumba? Kodi mnzanu angavomeleze yankho lanu?

  • Kodi mungaonetse bwanji kulolela pa nkhani ya nthawi imene mumafuna kuti mnzanu wa m’cikwati aziceza nanu?

    MFUNDO YA M’BAIBO: “Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 AKORINTO 10:24.

Jason na Alexandra.

“Nimaseŵenzela panyumba. Conco nimayesetsa kudziikila malile a nthawi yoseŵenza. Komanso ikafika nthawi inayake, nimaseting’a foni yanga kuti isamaonetse mameseji a kunchito amene abwela. Nimacita izi n’colinga cakuti nizikwanitsa kuiseŵenzetsa pa zinthu zina, monga kuyang’ana pa nthawi popanda kuceutsidwa na zinthu za kunchito.”​—JASON, NA MKAZI WAKE, ALEXANDRA.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani