Mawu Oyamba
Anthu ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya mmene cilengedwe na moyo padziko zinayambila. Magazini ino ya Galamuka! ikuthandizani kudziŵa mfundo zina zocititsa cidwi pankhaniyi, zimene zidzakuthandizani kusankha nokha zoyenela kukhulupilila. Kodi zam’cilengedwe zinangokhalako zokha kapena zinacita kulengedwa na Mulungu? Kudziŵa yankho pa funso limeneli kungakupindulitseni kwambili.