LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 3 masa. 10-13
  • Zimene Baibo Imatiuza

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Baibo Imatiuza
  • Galamuka!—2021
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Maganizo Olakwika pa Zimene Baibo Imakamba
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Sayansi Imagwilizana na Baibo?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
Galamuka!—2021
g21 na. 3 masa. 10-13

Zimene Baibo Imatiuza

“Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwela.” (Genesis 2:4) Umu ni mmene Baibo imafotokozela ciyambi ca dziko lapansi. Kodi zimene Baibo imakamba zimagwilizana na mfundo zotsimikizika za sayansi? Ganizilani zitsanzo zingapo izi.

Ciyambi: Kumwamba na dziko lapansi zinalengedwa

Kodi cilengedwe cilibe ciyambi?

Genesis 1:1 imati: “Pa ciyambi Mulungu analenga kumwamba na dziko lapansi.”

Caka ca 1950 cisanafike, asayansi ambili ochuka anali kukhulupilila kuti cilengedwe cilibe ciyambi. Koma cifukwa ca zimene atulukila posacedwa, asayansi ambili tsopano amavomeleza kuti cilengedwe cili na ciyambi.

Kodi poyamba dziko lapansi linali kuoneka bwanji?

Genesis 1:2, 9 imati dziko lapansi litangolengedwa, linali “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu,” ndipo paliponse panali madzi okha-okha.

Zimenezi n’zogwilizana na zimene asayansi apeza. Katswili wa maphunzilo a zamoyo, dzina lake Patrick Shih anati, poyamba padziko lapansi “panali mpweya woipa, wopanda oxygen . . . ,” ndipo panalibe camoyo ciliconse. Magazini yochedwa Astronomy imati: “Kafukufuku waposacedwa aonetsa kuti poyamba padziko lapansi panali madzi okha-okha, ndipo mtunda unali kuonekela pang’ono kapena sunali kuoneka n’komwe.”

Kodi cifungadziko cinasintha bwanji m’kupita kwa nthawi?

Genesis 1:3-5 imaonetsa kuti pamene kuwala kunayamba kuonekela padziko lapansi, copangitsa kuwalako sicinali kuonekela padziko. Patapita nthawi, m’pamene dzuŵa na mwezi zinayamba kuonekela bwino padziko lapansi, moti munthu akanakhalapo akanatha kuziona.—Genesis 1:14-18.

Baibo siikamba kuti zamoyo zonse padziko lapansi zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24 lililonse

Koleji ina ya kafukufuku wa zacilengedwe yochedwa Smithsonian Environmental Research Center imati, poyamba cifungadziko cinali kulola kuwala kocepa cabe kufika padziko lapansi. Imakambanso kuti: “Dziko lapansi litangokhalapo kumene, paliponse panali nkhungu ya mpweya wa Methane.” Koma patapita nthawi, “nkhunguyo inacoka ndipo kumwamba kunayamba kuoneka buluu.”

Kodi zamoyo zosiyanasiyana zinakhalapo liti padziko lapansi?

1​—Tsiku Loyamba: Kuwala kuyenela kuti kunayamba kuonekela padziko lapansi.—Genesis 1:3-5

2​—Tsiku Laciŵili: Padziko lonse lapansi panali madzi na nthunzi yambili. Zinthu ziŵilizi zinalekanitsidwa n’kusiya mpata pakati pake.—Genesis 1:6-8

3​—Tsiku Lacitatu: Madzi padziko anayamba kucepa, ndipo nthaka inaonekela.—Genesis 1:9-13

4​—Tsiku Lacinayi: Dzuŵa na mwezi zinayamba kuonekela padziko lapansi.—Genesis 1:14-19

5​—Tsiku Lacisanu: Mulungu analenga zamoyo zam’madzi komanso zouluka, ndipo anazilenga kuti zizitha kubelekana monga mwa mitundu yawo.—Genesis 1:20-23

6 Tsiku la 6: Mulungu analenga nyama za kumtunda, zikulu-zikulu na zing’ono-zing’ono zomwe. Kumapeto kwa tsiku la 6, Mulungu analenga mwamuna na mkazi oyamba.—Genesis 1:24-31

Genesis 1:20-27 imati nsomba n’zimene zinali zoyamba, kenako mbalame, nyama za kumtunda, ndipo anthu ndiwo anali othela kulengedwa. Nawonso asayansi amakhulupilila kuti nsomba zinakhalapo kale-kale nyama zakumtunda zisanakhalepo, komanso kuti anthu anakhalapo patapita nthawi yaitali.

Baibo siikamba kuti zamoyo sizingasinthe m’kupita kwa nthawi

“Zimene Baibo imakamba pa Genesis caputala 1 ni zacidule. Koma n’zocititsa cidwi kwambili kuti zimene imakambazo n’zogwilizana kwambili na zimene asayansi amakono apeza.”—Anatelo katswili wasayansi Gerald L. Schroeder.

Maganizo Olakwika pa Zimene Baibo Imakamba

Anthu ena amakamba kuti zimene Baibo imakamba zimasiyana na zimene asayansi apeza. Koma nthawi zambili anthu amakamba zimenezi cifukwa cosamvetsetsa bwino zimene Baibo imakamba.

Baibo siikamba kuti cilengedwe conse kapena dziko lapansi zangokhalako kwa zaka 6,000. Koma imangokamba kuti kumwamba na dziko lapansi zinalengedwa “paciyambi.” (Genesis 1:1) Baibo siifotokoza kuti ‘paciyambipo’ ni nthawi iti makamaka.

Baibo siikamba kuti zamoyo zonse padziko lapansi zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24 lililonse. Koma imaseŵenzetsa mawu akuti “tsiku” pofotokoza za nthawi ya utali wosiyana-siyana. Mwacitsanzo, nthawi imene Mulungu analenga zinthu zonse, kuphatikizapo “masiku” 6 a kulenga ochulidwa mu Genesis caputala 1, nayonso imachedwa “tsiku” limodzi. Baibo imati linali “tsiku limene Yehovaa Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.” (Genesis 2:4) Conco, tsiku lililonse mwa “masiku” 6 akulenga amenewo, pamene Mulungu anakonza dziko lapansi kuti pakhale zamoyo na kulenga zamoyozo, lingakhale kuti limaimila nthawi yaitali kwambili.

Baibo siikamba kuti zamoyo sizingasinthe m’kupita kwa nthawi. Buku la Genesis limakamba kuti nyama zinalengedwa “monga mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:24, 25) Liwu la m’Baibo lakuti “mitundu” si liwu la zasayansi, ndipo cioneka kuti limatanthauza magulu akulu-akulu a zamoyo. Conco mu “mtundu” umodzi wa zamoyo mungakhale zamoyo zosiyanasiyana. Mawu amenewa aonetsa kuti zamoyo zosiyana-siyana za mu “mtundu” umodzi komanso zimakhala pamodzi, zingathe kusintha m’kupita kwa nthawi.

Muganiza bwanji?

Monga taonela, Baibo imakamba mosavuta komanso molondola mmene cilengedwe cinayambila, mmene dziko linalili litangopangidwa, komanso mmene moyo unayambila. Ndiye kodi n’kutheka kuti Baibo imakambanso zolondola ponena za amene analenga zinthu zonsezo? Encyclopædia Britannica imati, “Mfundo yakuti zamoyo zinakhalapo cifukwa ca mphamvu inayake yoposa ya munthu ni yogwilizana na zimene sayansi yamakono imakamba.”b

Ganizilani izi:

Ŵelengani Genesis 1:1–2:4. Zimene mavesiwa amakamba n’zosiyana kwambili na nthano zakale zokhudza cilengedwe. Mwacitsanzo, Ababulo anali kukhulupilila kuti cilengedwe conse kuphatikizapo anthu, zinapangidwa kucokela ku mtembo wa mulungu winawake wamkazi komanso magazi a mulungu winawake wamwamuna. Aiguputo akale anali kukhulupilila kuti mulungu wochedwa Ra ndiye analenga anthu pogwilitsa nchito misozi. Ku China, anthu ena anali kukhululpilila kuti makemiko a padziko lapansi anapangidwa kucokela ku mtembo wa cimunthu cinacake cacikulu, komanso kuti anthu anacokela ku nthata zimene zinali pa mtembowo. Kodi muganiza kuti nkhani ya m’buku la Genesis nayonso ni nthano monga zimenezi? Kapena ni yogwilizana na sayansi?

Onelelani vidiyo ya mphindi zinayi yakuti Kodi Kumwamba na Dziko Lapansi Zinacita Kulengedwa? Fufuzani mutu wa vidiyoyi pa jw.org.

a Yehova ni dzina la Mulungu lochulidwa m’Baibo.

b Encyclopædia Britannica siiphunzitsa kuti zamoyo zinacita kulengedwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani