LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 22
  • Yosefe Aponyedwa M’ndende

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yosefe Aponyedwa M’ndende
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kapolo Amene Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • “Kodi Mulungu Sindiye Amamasulila Maloto?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yehova Akukuthandizani Kupambana Mayeso
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Yehova Sanamuiŵale Yosefe
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Onaninso Zina
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 22

Nkhani 22

Yosefe Aponyedwa M’ndende

YOSEFE anali ndi zaka 17 cabe pamene anatengedwa kuyenda ku Iguputo. Ali kumeneko anagulitsidwa kwa munthu wina wochedwa Potifara. Potifara aseŵenzela mfumu ya Iguputo, dzina lake Farao.

Yosefe ni wolimba panchito poseŵenzela bwana wake, Potifara. Conco, pamene Yosefe akula, Potifara amuika kukhala woyang’anila nyumba yake yonse. Nanga n’cifukwa ciani Yosefe ali mu ndende kumeneku? N’cifukwa ca mkazi wa Potifara.

Pamene Yosefe akula, akhala wokongola kwambili m’maonekedwe, ndipo mkazi wa Potifara afuna kuti agone naye. Koma Yosefe adziŵa kuti kucita zimenezi n’kulakwa, ndipo akana. Mkazi wa Potifara akalipa kwambili. Conco pamene mwamuna wake abwela kunyumba, amuuza zabodza kuti: ‘Yosefe woipa uja anafuna kugona nane!’ Potifara akhulupilila zimene mkazi wake akamba, ndipo akwiyila Yosefe kwambili. Conco, anamutumiza kundende.

Sipanapite nthawi yaitali, mwamuna amene ni mkulu wa ndende aona kuti Yosefe ni munthu wabwino. Conco amuika kukhala woyang’anila akaidi ena onse. Nthawi ina, Farao akwiyila kwambili wopelekela cikho ndi wophika mkate wake, ndipo awaponya mu ndende. Usiku wina onse aŵili alota maloto apadela, koma sanadziŵe tanthauzo la maloto ao. Tsiku lotsatila Yosefe awauza kuti: ‘Ndiuzeni maloto anu.’ Ndipo pamene amufotokozela maloto ao, Yosefe, mothandizidwa ndi Mulungu, awauza tanthauzo la maloto amenewo.

Yosefe auza wopelekela cikho kuti: ‘Pakapita masiku atatu adzakucotsa mu ndende muno, ndipo udzakhalanso wopelekela cikho wa Farao.’ Conco Yosefe aonjezela kuti: ‘Ukatuluka ukauze Farao za ine, ndipo ukandithandize kutuluka m’malo ano.’ Koma kwa wophika mkate, Yosefe akuti: ‘Pakangopita masiku atatu, Farao adzadula mutu wako.’

Patapita masiku atatu, zinacitika monga mmene Yosefe anakambila. Farao adula mutu wa wophika mkate. Koma wopelekela cikho atulutsidwa mu ndende ndipo ayamba kutumikilanso mfumu. Koma wopelekela cikho ameneyu sanakumbukile za Yosefe! Sanakambe ciliconse kwa Farao cokhudza Yosefe, ndipo Yosefe anapitiliza kukhala mu ndende.

Genesis 39:1-23; 40:1-23.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani