LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 30
  • Citsamba Coyaka Moto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Citsamba Coyaka Moto
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Citsamba Coyaka Moto
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Cimene Mose Anathaŵila
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 30

Nkhani 30

Citsamba Coyaka Moto

MOSE anayenda mpaka ku phili la Horebe kuti akapezeko maudzu a nkhosa. Pamene anali kumeneko anaona citsamba cikuyaka moto, koma sicinali kupsa.

Pamene anaona zimenezi, Mose anaganiza kuti: ‘Izi ni zodabwitsa kwambili, niyenda pafupi kuti nionetsetse.’ Pamene anafika pafupi, panamveka mau kucokela mu citsamba onena kuti: ‘Usafike pafupi kwambili. Vula nsapato zako, cifukwa malo amene waimapo ni malo oyela.’ Mose anaphimba nkhope yake cifukwa ndi Mulungu amene anali kukamba naye kupitila mwa mngelo.

Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ndaona kuvutika kwa anthu anga ku Iguputo. Conco, ndipita ndikawalanditse, ndipo ndidzatumiza iwe kuti ukawatsogolele pocoka ku Iguputo.’ Yehova anali ndi colinga cobweletsa anthu ake ku dziko lokongola la Kanani.

Koma Mose anati: ‘Ndine ndani ine. Kodi ningakwanitse bwanji kucita zimenezo? Nanga bwanji ndikapita, ndiyeno Aisiraeli n’kundifunsa kuti, “Kodi ndani amene wakutuma?” Kodi ndikanene ciani?’

Mulungu anamuyankha kuti: ‘Izi n’zimene udzanena, “Yehova Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo ndi amene wandituma kwa inu.” Ndipo Yehova anapitiliza kuti: ‘Ili ndilo dzina langa kosatha.’

Mose anayankha Mulungu kuti: ‘Koma bwanji ngati io sadzandikhulupilila ndikawauza kuti mwandituma?’

Mulungu anamufunsa kuti: ‘N’ciani ico cili mu dzanja lako?

Mose anayankha kuti: ‘Ni ndodo

Ndiyeno Mulungu anati: ‘Iponye pansi. Pamene Mose anaiponya pansi, ndodo ija inasanduka njoka. Ndiyeno Yehova anaonetsa Mose cozizwitsa cina. Iye anati: ‘Loŵetsa dzanja lako m’malaya ako.’ Mose anacita zimenezo, ndipo pamene anatulutsa dzanja lake, linayela mbuu ngati cipale cofeŵa. Dzanja lake linaoneka monga ngati linali ndi nthenda yoopsa yakhate. Ndiyeno, Yehova anapatsa Mose mphamvu zocita cozizwitsa cacitatu. Potsilizila pake anati: ‘Ukacita zozizwitsa zimenezi, Aisiraeli adzakhulupilila kuti ndine ndakutuma.’

Pambuyo pake Mose anapita kunyumba, ndipo anauza Yetero kuti: ‘Conde ndiloleni ndibwelele ku Iguputo kuti ndikaone mmene acibanja anga alili.’ Cotelo, Yetero analailana ndi Mose, ndipo Mose ananyamuka ulendo wobwelela ku Iguputo.

Ekisodo 3:1-22; 4:1-20.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani