LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 56
  • Sauli—mfumu Yoyamba Ya Isiraeli

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Sauli—mfumu Yoyamba Ya Isiraeli
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yesu Asankha Saulo
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Davide na Sauli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Paulendo Wa Ku Damasiko
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 56

Nkhani 56

Sauli—mfumu Yoyamba Ya Isiraeli

WAMUONA Samueli athila mafuta pamutu pa mwamuna uyu. Izi n’zimene anali kucita kwa munthu kuonetsa kuti wasankhidwa kukhala mfumu. Yehova auza Samueli kuthila mafuta pamutu wa Sauli. Ni mafuta apadela onunkhila bwino kwambili.

Sauli aganiza kuti sali woyenelela kukhala mfumu. Iye auza Samueli kuti: ‘Ine ndine wa fuko la Benjamini, fuko laling’ono kwambili pa mafuko onse a Isiraeli. Ndiye n’cifukwa ciani mwanena kuti n’dzakhala mfumu?’ Yehova akonda Sauli cifukwa sadzikudza ndi kudziona kukhala wofunika kwambili. Ndiye cifukwa cake amusankha kukhala mfumu.

Koma Sauli si munthu wosauka kapena munthu wamba. Iye acokela ku banja lolemela, ndipo ni mwamuna wokongola komanso wamtali kupambana munthu aliyense mu Isiraeli! Sauli alinso waliŵilo ndi wamphamvu kwambili. Anthu akondwela poona kuti Yehova wasankha Sauli kukhala mfumu. Ndipo onse ayamba kufuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’

Adani a Aisiraeli apitiliza kukhala amphamvu, ndipo awavutitsabe kwambili Aisiraeli. Patapita nthawi yocepa, pamene Sauli wakhala mfumu, Aamoni abwela kudzacita nkhondo ndi Aisiraeli. Koma Sauli asonkhanitsa asilikali ambili ndipo awapambana Aamoni. Zimenezi zikondweletsa anthu pokhala ndi Sauli monga mfumu yao.

Kwa zaka zambili, Sauli atsogolela Aisiraeli kupambana adani ao pankhondo zambili. Sauli alinso ndi mwana mwamuna wamphamvu, dzina lake Yonatani. Ndipo iye athandiza Aisiraeli kupambana nkhondo zambili. Afilisti akhalabe adani oipa kwambili a Aisiraeli. Tsiku lina masauzande ndi masauzande a Afilisti anabwela kudzacita nkhondo ndi Aisiraeli.

Samueli auza Sauli kuyembekezela mpaka iye abwele kuti adzapeleke nsembe kapena mphatso kwa Yehova. Koma Samueli acedwa kubwela. Sauli acita mantha kuti Afilisti adzayamba nkhondo, conco apeleka yekha nsembe. Koma pamene Samueli wabwela, auza Sauli kuti anaphwanya malangizo. Samueli akuti: ‘Yehova adzasankha munthu wina kukhala mfumu ya Aisiraeli.’

Patapita kanthawi, Sauli anaphwanyanso malangizo ena. Conco Samueli amuuza kuti: ‘Kumvela Yehova ndiko kwabwino kuposa kupeleka nsembe za nkhosa zabwino. Cifukwa cakuti simunamvele Yehova, iye sadzakulolani kupitiliza kukhala mfumu ya Isiraeli.’

Tingatengepo phunzilo labwino kwambili pamenepa. Zimenezi zimationetsa kufunika komvela Yehova nthawi zonse. Ndiponso zimationetsa kuti munthu wabwino angasinthe n’kukhala woipa, monga mmene Sauli anacitila. Sitifuna kukhala anthu oipa, si conco?

1 Samueli caputa 9 mpaka 11; 1 Sa 13:5-14; 14:47-52; 15:1-35; 2 Samueli 1:23.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani