LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • my nkhani 93
  • Yesu Adyetsa Anthu Ambili

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Adyetsa Anthu Ambili
  • Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yesu Adyetsa Khamu la Anthu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Yesu Anayenda pa Madzi
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Kuculukitsa Mikate Mozizwitsa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
my nkhani 93

Nkhani 93

Yesu Adyetsa Anthu Ambili

CINTHU coipa kwambili cacitika. Yohane Mbatizi waphedwa. Mkazi wa mfumu Herodiya samukonda Yohane. Conco asonkhezela mfumu kulamula kuti Yohane adulidwe mutu.

Pamene Yesu akumva zimenezi, amvela cisoni kwambili. Ndipo ayenda kumalo kwayekha kumene kulibe anthu. Koma anthu amutsatila. Pamene Yesu aona gulu la anthu, alimvelela cifundo. Awauza za ufumu wa Mulungu, ndipo acilitsa odwala ao.

Cakumadzulo ophunzila ake abwela kwa iye ndi kumuuza kuti: ‘Nthawi yatha ndipo kumalo kuno kulibe anthu, auzeni anthu ayende mu midzi kuti akadzigulile cakudya.’

Yesu awayankha kuti: ‘Iwo safunikila kupita, inu muwapatse cakudya.’ Yesu atembenukila kwa Filipo ndipo afunsa kuti: ‘Kodi tingagule kuti cakudya codyetsa anthu onse awa?’

Filipo ayankha kuti: ‘Padzafunika ndalama zambili kuti tigule cakudya cokwanila kuti aliyense adye.’ Andireya nayenso akuti: ‘Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda isanu ya mkate ndi tunsomba tuŵili. Koma tumenetu situngakwanile cikhamu conse ca anthu ici.’

Yesu akuti: ‘Auzeni anthu akhale pansi pamaudzu.’ Ndiyeno Yesu ayamikila Mulungu kaamba ka cakudyaco, ndi kuyamba kucinyema-nyema. Ndipo ophunzila apatsa anthu onse mkate ndi tunsomba. Pali amuna okwanila 5,000, ndi masauzande ambili a akazi ndi ana. Onse anadya mpaka kukhuta. Pamene ophunzila asonkhanitsa zakudya zotsala, zidzala mabasiketi 12!

Yesu tsopano auza ophunzila ake kukwela boti kuti aoloke Nyanja ya Galileya. Nthawi ya usiku kuyamba cimphepo cacikulu, ndipo mafunde akankhila boti uku ndi uku. Ophunzila ake acita mantha kwambili. Ndiyeno pakati pa usiku, io aona munthu ayenda pamadzi kubwela kumene io ali. Afuula mwamantha, cifukwa sadziŵa cimene aona.

Koma Yesu akuti: ‘Musacite mantha, ndine!’ Iwo sakhulupilila zimene iye akamba. Conco Petulo akuti: ‘Ambuye, ngati zoona ndinu, niuzeni niyende pamadzi apa kuti nibwele kumene inu muli.’ Ndipo Yesu ayankha kuti: ‘Bwela!’ Ndipo Petulo aseluka m’boti muja ndi kuyamba kuyenda pamadzi! Koma acita mantha, ndipo ayamba kumbila, koma Yesu amupulumutsa.

Panthawi ina, Yesu apatsanso masauzande a anthu cakudya. Koma nthawi ino, awadyetsa ndi mikate 7 ndi tunsomba tocepa. Ndipo ngakhale tsopano, onse akwanila cakudya. Kodi si cokondweletsa kuti Yesu amasamalila anthu? Pamene adzayamba kulamulila monga mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, sikudzakhala mavuto alionse!

Mateyu 14:1-32; 15:29-38; Yohane 6:1-21.

Mafunso Ophunzilila

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani