LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • gf phunzilo 5 masa. 8-9
  • Anzake A Mulungu Adzakhala mu Paladaiso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Anzake A Mulungu Adzakhala mu Paladaiso
  • Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Nkhani Zofanana
  • “Tidzaonana M’Paradaiso!”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?
    Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
gf phunzilo 5 masa. 8-9

Phunzilo 5

Anzake A Mulungu Adzakhala mu Paladaiso

Paladaiso idzakhala malo osiyana na dziko limene tikhalamo panthawi ino. Mulungu sanafune ngakhale pang’ono kuti padziko lapansi pakhale mavuto alionse na zinthu zocititsa cisoni. Mtsogolo, Mulungu adzasintha dziko lapansi kukhala Paladaiso. Kodi Paladaiso idzakhala malo abwanji? Tiyeni tione zimene Baibo ikamba:

Anthu abwino. Mu Paladaiso mudzakhala cabe anzake a Mulungu. Adzayamba kucitilana zinthu zabwino wina na mnzake. Pamoyo wawo adzatsatila njila za Mulungu zolungama.—Miyambo 2:21.

Zakudya za mwana alilenji. Mu Paladaiso simudzakhala njala. Baibo imakamba kuti: ‘M’dzikomo mudzakhala zinthu [kapena, zakudya] zoculuka.’—Salmo 72:16.

Manyumba abwino na nchito zokondweletsa. Mu Paladaiso padziko lapansi, banja lililonse lidzakhala na nyumba yawoyawo. Munthu aliyense adzacita nchito imene idzamukondweletsa.—Yesaya 65:21-23.

Kudzakhala mtendele padziko lonse. Nkhondo na kuphana kudzakhala kulibe. Mau a Mulungu amakamba kuti: ‘[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezelo a dziko lapansi.’—Salmo 46:8, 9.

Umoyo wabwino. Baibo imalonjeza kuti: “Ndipo wokhalamo [mu Paladaiso] sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndiponso, sipadzakhala munthu wolemala kapena wosaona kapena wosamva kapena wosakamba.—Yesaya 35:5, 6.

Zoŵaŵa, cisoni na imfa zidzacoka. Mau a Mulungu amakamba kuti: ‘Ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso malilo, kapena kulila, kapena coŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’—Cibvumbulutso 21:4.

Anthu oipa sadzakhalamo. Yehova analonjeza kuti: “Oipa . . . adzalikhidwa [kucotsedwa] m’dziko, aciwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.

Anthu adzakondana na kulemekezana. Sikudzakhala kucitilana zosalungama, kupondelezana, dyela, na kuzondana. Anthu adzakhala ogwilizana, ndipo adzatsatila njila za Mulungu zolungama.—Yesaya 26:9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani