LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • gf phunzilo 12 tsa. 20
  • Kodi Munthu Akafa Cimacitika Kwa Iye ni Ciyani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Munthu Akafa Cimacitika Kwa Iye ni Ciyani?
  • Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Munthu Akamwalila, Cimacitikano N’ciyani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Makolo Athu Anapita Kuti?
    Njila ya Kumoyo Wamuyaya—Kodi Mwaipeza?
  • Kodi Akufa Ali Kuti?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Cilikizani Coonadi Pankhani ya Akufa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Onaninso Zina
Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
gf phunzilo 12 tsa. 20

Phunzilo 12

Kodi Munthu Akafa Cimacitika Kwa Iye ni Ciyani?

Munthu akafa ndiye kuti alibe moyo. Imfa ili monga tulo tukulu, kapena kuti tulo tofa nato. (Yohane 11:11-14) Anthu akufa sangamve, sangaone, sangakambe, kapena kuganiza ciliconse. (Mlaliki 9:5, 10) Cipembedzo conama cimaphunzitsa kuti anthu akafa amayenda ku dziko la mizimu kukakhala pamodzi na mizimu ya makolo awo. Koma Baibo siiphunzitsa zimenezi.

Anthu amene anafa sangatithandize pa ciliconse, ndipo sangatiukile ciŵanda. Anthu ambili amakonda kucita miyambo na kupeleka nsembe zimene amakhulupilila kuti zimakondweletsa anthu amene anafa. Zimenezi Mulungu sakondwela nazo cifukwa ni mabodza a Satana Mdyelekezi. Sizingakondweletse ngakhale akufa cifukwa alibe moyo. Sitiyenela kuopa kapena kulambila anthu amene anafa. Tifunikila kulambila Mulungu yekha cabe.—Mateyu 4:10.

Anthu amene anafa adzauka. Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kuti akakhale na moyo mu paladaiso padziko lapansi. Zimenezi zidzacitika mtsogolo. (Yohane 5:28, 29; Macitidwe 24:15) Kwa Mulungu, ni cosavuta kuukitsa anthu akufa, monga mmene cilili cosavuta kwa imwe kuutsa munthu amene ali mu tulo.—Marko 5:22, 23, 41, 42.

Maganizo akuti anthu ife sitimafelatu ni mabodza amene Satana Mdyelekezi amafalitsa. Satana na viŵanda vake amapangitsa anthu kuganiza kuti mizimu ya anthu amene anafa ili na moyo. Amakamba kuti mizimu imeneyo ni imene imadwalitsa anthu na kubweletsa mavuto ena. Nthawi zina Satana amanama anthu kupitila m’maloto na masomphenya oona vinthu. Yehova amawazonda anthu amene amayesa kukamba na anthu amene anafa.—Deuteronomo 18:10-12.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani