NKHANI 7
Ciyembekezo Cotsimikizilika Cakuti Okondedwa Athu Amene Anamwalila Adzauka
Kodi timadziŵa bwanji kuti ciukililo cidzacitika zoona?
N’ciani cimaonetsa kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa akufa?
Nanga ndani adzaukitsidwa?
1-3. Kodi ndi mdani uti amene atithamangitsa ife tonse? Ndipo n’cifukwa ciani kudziŵa zimene Baibo imaphunzitsa n’kolimbikitsa?
GANIZILANI kuti cigaŵenga coopsa cikuthamangitsani. N’camphamvu kwambili, ndipo n’caliŵilo kuposa inu. Mumadziŵa kuti n’cimunthu copanda cifundo cifukwa munaonapo mmene cinaphela anzanu ena. Ngakhale muthamange bwanji, m’pamene cifika pafupi kuti cikugwileni. Ndipo zaonekelatu kuti basi cidzakugwilani. Ndiyeno mwadzidzidzi, munthu wina atulukila. Iye ndi wamphamvu kwambili kuposa cigaŵengaco, ndipo akuuzani kuti adzakuthandizani.
2 Mofananamo, pali mdani amene ali kukuthamangitsani. Ndipo tonse atithamangitsa. Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Baibo imachula mdani ameneyo kuti ndi imfa. Palibe aliyense wa ife amene angathaŵe kwa mdani ameneyu kapena kumugonjetsa. Ambili taona mmene mdani ameneyu watengela miyoyo ya anthu amene timawakonda. Koma Yehova ndi wamphamvu kwambili kuposa imfa. Iye ndi Mpulumutsi wacikondi amene waonetsa kale kuti akhoza kugonjetsa mdani ameneyu. Ndipo analonjeza kuti adzagonjetsa ndi kumalizilatu mdani ameneyu, imfa. Baibo imaphunzitsa kuti: “Imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Ha, ni nkhani yosangalatsa cotani nanga!
3 Tsopano tiyeni tione mwacidule mmene mdani ameneyu amativutitsila pamene watitengela wokondedwa wathu mu imfa. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kumvetsetsa lonjezo limene lidzatikondweletsa kwambili. Yehova analonjeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. (Yesaya 26:19) Iwo adzaukitsidwa. Ili ndi lonjezo la Mulungu limene limatipatsa ciyembekezo.
MUNTHU AMENE TIMAKONDA AKAMWALILA
4. (a) Kodi citsanzo ca Yesu cimationetsa ciani za mmene Yehova amaonela imfa? (b) Kodi Yesu anakhala ndi mabwenzi a pamtima ati?
4 Kodi munatayapo wokondedwa wanu mu imfa? Panthawi imeneyi, timakhala ndi cisoni kwambili cakuti timasoŵelatu cocita, ndipo zimenezi zimaoneka ngati n’zosapililika. Zimenezi zikacitika, tiyenela kuŵelenga Mau a Mulungu kuti tipeze citonthozo. (2 Akorinto 1:3, 4) Baibo imatithandiza kudziŵa mmene Yehova ndi Yesu amamvelela munthu akamwalila. Yesu amene anaonetsa mtima weni-weni wa Atate wake, anadziŵa mmene kumamvekela kutaya wokondedwa wathu mu imfa. (Yohane 14:9) Nthawi zonse Yesu akapita ku Yerusalemu, anali kukaonanso Lazaro limodzi ndi azilongosi ake, Mariya ndi Marita, amene anali kukhala mu tauni yapafupi ya Betaniya. Iwo anakhala mabwenzi a Yesu a pamtima. Baibo imati: “Yesu anali kukonda Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” (Yohane 11:5) Koma monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, Lazaro anafa.
5, 6. (a) Kodi Yesu anacita bwanji pamene anali pamalilo pamodzi ndi banja la Lazaro ndi mabwenzi ao? (b) N’cifukwa ciani kumva cisoni kwa Yesu kuli kolimbikitsa kwa ife?
5 Kodi Yesu anamva bwanji pamene bwenzi lake linamwalila? Nkhani ya m’Baibo imatiuza kuti Yesu anapita kumalilo kukakhala pamodzi ndi banja la Lazaro ndi mabwenzi ao. Poona mmene io anali kulilila, zinam’khudza kwambili. Ndiyeno nkhaniyo imakamba kuti iye ‘anadzuma povutika mumtima, ndipo analila.’ (Yohane 11:33, 35) Kodi pamene Yesu analila zitanthauza kuti analibe ciyembekezo? Iyai. Iye anadziŵa kuti adzacita cinthu cina codabwitsa. (Yohane 11:3, 4) Ngakhale ndi conco, Yesu anamva kuŵaŵa ndi cisoni cimene imfa imabweletsa.
6 Kumbali ina, mmene Yesu anamvelela cisoni n’zolimbikitsa kwa ife. Zimatiphunzitsa kuti Yesu ndi Atate wake Yehova amadana ndi imfa. Koma Yehova Mulungu adzakwanitsa kulimbana ndi mdani ameneyu mpaka kum’gonjetsa kothelatu. Tsopano tiyeni tione zimene Mulungu anathandiza Yesu kucita.
“LAZARO, TULUKA!”
7, 8. N’cifukwa ciani zinaoneka ngati panalibenso cimene cikanacitika kwa Lazaro? Koma Yesu anacita ciani?
7 Lazaro anali ataikidwa m’manda a m’phanga, ndipo Yesu anapempha anthu kuti acotse mwala wotsekela pakhomo la mandawo. Marita anakana zimenezo cifukwa panali patapita masiku anai, ndipo thupi la Lazaro linali litayamba kuonongeka. (Yohane 11:39) Mwa kuona kwa umunthu, panalibe ciliconse cimene akanacita.
Kuukitsidwa kwa Lazaro kunabweletsa cimwemwe cacikulu.—Yohane 11:38-44
8 Mwala uja anaukunkhuluza, ndipo Yesu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Pamenepo cinacitika n’ciani? “Amene anali wakufa uja anatuluka.” (Yohane 11:43, 44) Ganizani cabe mmene anthuwo anakondwelela! Kaya Lazaro anali mng’ono wao, wacibanja, bwenzi, kapena mnansi wao, anadziŵa kuti iye anamwalila ndithu. Koma anangoona uyu watuluka!—ali bwino-bwino ngati poyamba. Zinali ngati kulota cabe. Mosakaikila, ambili anam’kumbatila Lazaro mwacisangalalo. Kodi umenewu sunali umboni woonetsela kuti Yehova ali ndi mphamvu zogonjetsa imfa?
Eliya anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye.—1 Mafumu 17:17-24
9, 10. (a) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kumene anacotsa mphamvu zimene anaukitsila Lazaro? (b) Kodi timapindula bwanji tikamaŵelenga nkhani za kuuka kwa akufa za m’Baibo?
9 Yesu sanakambe kuti anacita cozizwitsa cimeneci mwa mphamvu zake iyai. Akalibe kuitana Lazaro kuti atuluke m’manda, anayamba wapeleka pemphelo. M’pemphelo lake anaonetsa poyela kuti Yehova ndiye adzapeleka mphamvu zoukitsila Lazaro. (Yohane 11:41, 42) Si apa pokha pamene Yehova anagwilitsila nchito mphamvu zake kuukitsa munthu. Kuonjezela pa cozizwitsa coukitsa Lazaro, Mau a Mulungu amatiuzanso za anthu ena 8 amene anaukitsidwa mozizwitsa.a Nkhani zimenezi n’zokondweletsa kwambili kuziŵelenga. Zimatiphunzitsa kuti Mulungu alibe tsankho, cifukwa anthu amene anaukitsidwa amaphatikizapo acicepele ndi acikulile, amuna ndi akazi, Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina. Nkhani zimenezi zimaonetsa kuti anthu anakondwela kwambili pamene anthuwo anaukitsidwa. Mwacitsanzo, pamene Yesu anaukitsa mtsikana wina, makolo ake “anasangalala kwambili.” (Maliko 5:42) Zoona, Yehova anawacitila cinthu cokondweletsa kwambili cimene sakanaiŵala.
Mtumwi Petulo anaukitsa Dorika mkazi wacikristu.—Machitidwe 9:36-42
10 N’zoona kuti anthu amene Yesu anaukitsa anafanso. Kodi ndiye kuti kuwaukitsa kunali kopanda tanthauzo? Ndithudi ayi. Zocitika zimenezi zimatsimikizila mfundo zofunika za m’Baibo, ndipo zimatipatsa ciyembekezo.
ZIMENE TIMAPHUNZILA PA NKHANI ZA AKUFA AMENE ANAUKITSIDWA
11. Kodi nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro imatsimikizila bwanji mfundo ya pa Mlaliki 9:5?
11 Baibo imaphunzitsa kuti “akufa sadziŵa ciliconse.” Iwo sali ndi moyo kwina kulikonse. Nkhani ya Lazaro imatsimikizila mfundo imeneyi. Pamene Lazaro anakhalanso ndi moyo, kodi anasimbila anthu za mmene moyo wakumwamba ulili wokondweletsa? Kapena kodi anawafotokozela zoopsa za ku helo wamoto? Iyai. Baibo siionetsa kuti Lazaro anakambako zimenezo. Pa masiku anai amene iye anali wakufa, ‘anali wosadziŵa ciliconse.’ (Mlaliki 9:5) Lazaro sanapite kulikonse, koma anali cigonele mu imfa.—Yohane 11:11.
12. Kodi pali umboni wanji wotitsimikizila kuti Lazaro anaukitsidwa zoona?
12 Nkhani ya Lazaro imatiphunzitsanso kuti kuukitsa anthu akufa n’kothekadi, si zongoganizila cabe iyai. Yesu anaukitsa Lazaro pamaso pa anthu amene anaona ndi maso ao. Ngakhale atsogoleli acipembedzo amene anali kudana ndi Yesu sanatsutse zimenezi. M’malo mwake, io anati: “Kodi ticite ciani pamenepa, cifukwa munthu uyu [Yesu] akucita zizindikilo zoculuka?” (Yohane 11:47) Anthu ambili anapita kukaona munthu amene anaukitsidwayo. Mwa ici, anthu ambili anakhulupilila mwa Yesu. Lazaro anakhala umboni weni-weni kwa io wakuti Yesu anatumidwadi ndi Mulungu. Umboni umenewu unali wosatsutsika cakuti ena mwa atsogoleli acipembedzo aciyuda ouma mtima anakonza ciwembu cakuti tsopano aphe onse aŵili, Yesu ndi Lazaro.—Yohane 11:53; 12:9-11.
13. Kodi tili ndi zifukwa zanji zokhulupililila kuti Yehova akhozadi kuukitsa akufa?
13 Kodi kukhulupilila za ciukililo n’kukhulupilila zinthu zosatheka? Iyai, cifukwa Yesu anaphunzitsa kuti tsiku lina “onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake.” (Yohane 5:28) Yehova ndiye analenga camoyo ciliconse. Kodi ingakhale nkhani yovuta kuti iye alengenso moyo umene unataika? Zingadalile kwambili cikumbukilo ca Yehova. Koma kodi iye angawakumbukile okondedwa athu onse amene anafa? Dziŵani izi: Kumwamba kuli nyenyezi mabiliyoni osaŵelengeka. Koma Mulungu amadziŵa dzina la nyenyezi iliyonse. (Yesaya 40:26) Conco, n’zosacita kufuna ngati Yehova Mulungu amakumbukila ciliconse cokhudza okondedwa anthu amene anamwalila, ndipo amalaka-laka kuti akawaukitse.
14, 15. Mogwilizana ndi zimene Yobu anakamba, kodi n’ciani cimaonetsa kuti Yehova amalaka-laka kuukitsa akufa?
14 Kodi n’ciani cimaonetsa kuti Yehova amalaka-laka kuukitsa akufa mogwilizana ndi zimene Yobu anakamba? Baibo imaphunzitsa kuti Iye amafunitsitsa kuukitsa akufa. Munthu wokhulupilika Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Yobu anali kukamba za kuyembekezela m’manda mpaka pamene nthawi idzafika imene Mulungu adzam’kumbukila. Iye anati kwa Yehova: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalaka-laka nchito ya manja anu.”—Yobu 14:13-15.
15 Ganizani cabe! Yehova amacita kulaka-laka kuti aukitse anthu akufa. Kodi si zolimbikitsa zimenezi? Nanga bwanji za ciukililo ca kutsogolo? Kodi ndani adzaukitsidwa, ndipo adzaukitsidwila kuti?
“ONSE ALI M’MANDA ACIKUMBUTSO”
16. Kodi akufa adzaukitsidwila m’dziko labwanji?
16 Nkhani za m’Baibo za ciukililo zimatiphunzitsa zambili ponena za ciukililo ca mtsogolo. Anthu amene kale anaukitsidwa pano padziko lapansi anakhalanso pamodzi ndi okondedwa ao. Ciukililo cimene cidzacitika mtsogolo cidzafananako ndi cimene cinacitika kale, koma cidzakhala cabwino kuposapo. Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 3, colinga ca Mulungu n’cakuti dziko lonse lapansi likhale paladaiso. Conco akufa sadzaukitsidwila m’dziko lodzala ndi nkhondo, upandu, ndi matenda. Iwo adzakhala ndi mwai wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi mwacimwemwe.
17. Kodi ciukililo cidzakhala cacikulu bwanji? Ndipo ndi anthu ati amene adzaukitsidwa?
17 Kodi ndani adzaukitsidwa? Yesu anakamba kuti “onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Mofananamo, lemba la Chivumbulutso 20:13 limati: “Nyanja inapeleka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda [kapena kuti Hade] zinapeleka akufa amene anali mmenemo.” Mau akuti “Hade” amatanthauza manda acikumbutso. (Onani Zakumapeto, pamapeji 212 mpaka 213.) M’manda amenewa simudzakhalanso anthu. Anthu mabiliyoni onse amene ali cigonele mmenemo adzakhalanso ndi moyo. Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Kodi zimenezi zitanthauza ciani?
Mu Paladaiso, akufa adzaukitsidwa ndipo adzakhalanso pamodzi ndi okondedwa ao
18. Kodi anthu “olungama” amene adzaukitsidwa amaphatikizapo anthu ati? Ndipo kodi inu panokha ciyembekezo cimeneci cimakukhudzani bwanji?
18 “Olungama” amaphatikizapo anthu ambili amene timaŵelenga m’Baibo amene anakhalako ndi moyo Yesu akalibe kubwela padziko lapansi. Mungaganizile za Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Esitere, ndi ena ambili. Ena mwa amuna ndi akazi okhulupilika amenewa amafotokozedwa mu caputala 11 ca Aheberi. “Olungama” amaphatikizaponso atumiki a Yehova amene amafa masiku ano. Cifukwa cokhala ndi ciyembekezo ca ciukililo, sitiopa kufa.—Aheberi 2:15.
19. Kodi anthu “osalungama” ndani? Ndipo ndi mwai wanji umene Yehova wawapatsa mokoma mtima?
19 Nanga bwanji za anthu amene sanatumikile Yehova kapena kumvela malamulo ake cifukwa cakuti sanali kum’dziŵa? Mabiliyoni a anthu “osalungama” amenewa sadzaiŵalika. Naonso adzaukitsidwa ndi kupatsidwa nthawi yophunzila za Mulungu woona ndi kum’tumikila. M’zaka 1,000, akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwai wotumikila Yehova pamodzi ndi anthu okhulupilika padziko lapansi. Nthawi imeneyi idzakhala yokondweletsa kwambili. Nyengo imeneyi ndi imene Baibo imacha Tsiku la Ciweluzo.b
20. Kodi Gehena n’ciani? Nanga ndani amapita kumeneko?
20 Kodi zimenezi zitanthauza kuti munthu aliyense amene anakhalako ndi moyo adzaukitsidwa? Iyai. Baibo imakamba kuti anthu ena akufa ali “mu Gehena.” (Luka 12:5) Mau akuti Gehena anacokela kumalo otailako zinyalala amene anali kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Kumeneko anali kuochako matupi a anthu akufa ndi zinyalala. Matupi a anthu amene anali zigaŵenga anali kuwataila kumeneko, cifukwa anali kuwaona kuti sanali kuyenelela ciukililo. Conco, mau akuti Gehena amaimila cionongeko cosatha. Ngakhale kuti Yesu ali ndi mbali yoweluza anthu amoyo ndi akufa, Yehova ndiye Woweluza wamkulu. (Machitidwe 10:42) Iye sadzaukitsa anthu amene amawaweluza kuti ndi oipa ndi osafuna kusintha.
CIUKILILO COPITA KUMWAMBA
21, 22. (a) Kodi Baibo imachulanso ciukililo cina citi? (b) Nanga ndani anali woyamba kuukitsidwa ndi moyo wauzimu?
21 Baibo imachulanso kuukitsidwa kwa mtundu wina, kokakhala ndi moyo kumwamba monga zolengedwa zauzimu. Pali citsanzo cimodzi cokha ca ciukililo ca mtundu umenewu colembedwa m’Baibo, ndico ca Yesu Kristu.
22 Pambuyo pakuti Yesu waphedwa monga munthu, Yehova sanalole kuti Mwana Wake wokhulupilika ameneyu akhale m’manda. (Salimo 16:10; Machitidwe 13:34, 35) Mulungu anaukitsa Yesu, koma osati monga munthu weni-weni. Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Kristu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” (1 Petulo 3:18) Zoona, ici cinali cozizwitsa codabwitsa kwambili. Yesu anakhalanso ndi moyo monga munthu wauzimu. (1 Akorinto 15:3-6) Iye anakhala woyamba kuukitsidwa m’njila yaulemelelo imeneyi. (Yohane 3:13) Koma sanali wotsilizila.
23, 24. Kodi ndani amapanga “kagulu ka nkhosa” ka Yesu? Ndipo ndi angati?
23 Pamene Yesu anatsala pang’ono kufa, anauza otsatila ake okhulupilika kuti adzabwelela kumwamba ‘kukawakonzela malo.’ (Yohane 14:2) Yesu anacha anthu amene adzapita kumwamba kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Kodi ndi angati amene ali m’kagulu kameneko ka Akristu okhulupilika? Malinga ndi Chivumbulutso 14:1, mtumwi Yohane anati: “Nditayang’ana, ndinaona Mwanawankhosa [Yesu Kristu] ataimilila paphili la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pao.”
24 Akristu amenewa a 144,000, amene akuphatikizapo atumwi okhulupilika a Yesu, amaukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba. Kodi ciukililo cao cimacitika liti? Mtumwi Paulo analemba kuti cidzacitika panthawi ya kukhalapo kwa Kristu. (1 Akorinto 15:23) Monga mmene tidzaphunzilila mu Nkhani 9, tikukhala m’nthawi imeneyi. Conco otsalila ocepa a 144,000 amene amamwalila masiku ano amaukitsidwa nthawi imeneyo kukakhala ndi moyo kumwamba. (1 Akorinto 15:51-55) Koma anthu oculuka ali ndi ciyembekezo coukitsidwa mtsogolo kudzakhala ndi moyo m’Paladaiso padziko lapansi.
25. Kodi m’nkhani yotsatila tidzaphunzila ciani?
25 Inde, Yehova adzagonjetsadi mdani wathu imfa, ndipo adzaicotsapo kothelatu! (Yesaya 25:8) Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi anthu amene adzaukitsidwila moyo wa kumwamba azikacita ciani kumeneko?’ Adzakhala mbali ya boma la Ufumu wabwino wa kumwamba. M’nkhani yotsatila tidzaphunzila zambili za boma limeneli.
a Nkhani zina zimapezeka pa 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Mateyu 28:5-7; Luka 7:11-17; 8:40-56; Machitidwe 9:36-42; ndi Machitidwe 20:7-12.
b Kuti mudziŵe zambili ponena za Tsiku la Ciweluzo ndi maziko a ciweluzo, mungaone Zakumapeto, pamapeji 213 mpaka 215.