NKHANI 11
N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?
Kodi Mulungu ndiye amacititsa mavuto?
Kodi ndi nkhani iti imene inayambika m’munda wa Edeni?
Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto a anthu?
1, 2. Kodi anthu amakumana ndi mavuto anji masiku ano? Ndipo mavutowo amapangitsa anthu ambili kufunsa mafunso ati?
PAMBUYO pa nkhondo yoopsa imene inacitika m’dziko lina, azimai ndi ana masauzande ambili amene anaphedwa anaikidwa m’manda amodzi (m’dzenje limodzi), ndipo pamwamba pake anazikapo tumitanda tung’ono-tung’ono. Pa kamtanda kalikonse analembapo funso lakuti: “N’cifukwa ciani?” Limeneli ndi funso limene limaonetsa kuŵaŵidwa mtima ndi cisoni cacikulu. Anthu amafunsa funso limeneli pamene nkhondo, ngozi, matenda, kapena upandu zapha okondedwa ao, kuononga nyumba zao, kapenanso kucititsa mavuto ena osaneneka. Amafuna kudziŵa cifukwa cake masoka amenewa amawacitikila.
2 N’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika? Ngati Yehova Mulungu ndi wamphamvu zonse, wacikondi, wanzelu, ndi wacilungamo, n’cifukwa ciani cidani ndi kupanda cilugamo zili kulikonse padziko? Kodi munayamba mwadzifunsapo mafunso amenewa?
3, 4. (a) Kodi n’cocitika citi cimene cimaonetsa kuti sikulakwa kufunsa kuti, N’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika? (b) Kodi Yehova amamva bwanji akamaona zoipa ndi mavuto amene anthu amakumana nao?
3 Kodi n’kulakwa kufunsa kuti n’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika? Ena amaganiza kuti kufunsa funso limeneli kungaonetse ngati kuti alibe cikhulupililo kweni-kweni mwa Mulungu, kapena kuti sam’lemekeza. Komabe, pamene muŵelenga Baibo, mudzapeza kuti anthu okhulupilika ndi oopa Mulungu akale naonso anali ndi mafunso ngati amenewa. Mwacitsanzo, mneneli Habakuku anafunsa Yehova kuti: “N’cifukwa ciani mukundicititsa kuona zinthu zopweteka? N’cifukwa ciani mukupitiliza kuyang’ana khalidwe loipa? N’cifukwa ciani kufunkha ndi ciwawa zikucitika pamaso panga? Ndipo n’cifukwa ciani pali mikangano ndi kumenyana?”—Habakuku 1:3.
Yehova adzacotsapo mavuto onse
4 Kodi Yehova anam’kalipila mneneli wokhulupilika Habakuku cifukwa cofunsa mafunso amenewa? Iyai. M’malo mwake, Mulungu analola kuti mau amene Habakuku anakamba moona mtima alembedwe m’Baibo. Mulungu anathandizanso mneneli ameneyu, kuti amvetse bwino zinthu ndi kuti akhale ndi cikhulupililo colimba. Yehova amafuna kucita cimodzi-modzi kwa inu. Kumbukilani kuti Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu “amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Kuposa munthu wina aliyense, Mulungu sakondwela kuona zoipa ndi mavuto onse amene anthu amakumana nao. (Yesaya 55:8, 9) Nanga n’cifukwa ciani anthu amavutika kwambili?
N’CIFUKWA CIANI PALI MAVUTO ONSEWA?
5. Kodi ena amapeleka zifukwa ziti pofotokoza cifukwa cimene anthu amavutikila? Koma kodi Baibo imaphunzitsa ciani?
5 Anthu a zipembedzo zosiyana-siyana amapita kwa atsogoleli ndi abusa ao kukafunsa funso limeneli. Nthawi zambili amawayankha kuti mavuto amene anthu amakumana nao ndi cifunilo ca Mulungu. Amakamba kuti Mulungu anakonzelatu cocitika ciliconse, ngakhale ngozi zonse zimene zimacitika. Ambili amauzidwa kuti zocita za Mulungu palibe munthu amene angazimvetsetse. Kapena amawauza kuti iye ndiye amacititsa imfa—ngakhale imfa za ana—n’colinga cakuti akakhale nao kumwamba. Koma malinga ndi mmene tinaphunzilila, Yehova Mulungu sacititsa coipa ciliconse. Baibo imati: “Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, Ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.
6. N’cifukwa ciani anthu ambili amaimba Mulungu mlandu wakuti ndiye amacititsa mavuto?
6 Kodi mudziŵa cimene anthu amaimbila Mulungu mlandu wakuti ndiye amacititsa mavuto? Nthawi zambili, amaimba Mulungu Wamphamvuyonse mlandu cifukwa amaganiza kuti iye ndi amene amalamulila dziko. Iwo sadziŵa coonadi cosavuta kumva koma cofunika cimene Baibo imaphunzitsa. Coonadi cimeneci munaciphunzila mu Nkhani 3 ya m’buku lino. Wolamulila weni-weni wa dziko lino ndi Satana Mdyelekezi.
7, 8. (a) Kodi dziko limaonetsa bwanji makhalidwe a wolamulila wake? (b) Kodi kupanda ungwilo kwa anthu ndi zinthu zakugwa mosayembekezeka zaonjezela bwanji mavuto a anthu?
7 Baibo imakamba momveka bwino kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mutaganizila, kodi zimenezi si zomveka? Dzikoli limaonetsa makhalidwe a colengedwa cauzimu cimene ‘cikusoceletsa dziko lonse lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9) Satana ndi wacidani, wacinyengo ndiponso wankhanza. Conco, dziko limene iye alamulila nalonso n’lodzala ndi cidani, cinyengo ndi nkhanza. Ici n’cifukwa cimodzi cimene padziko lapansi pakhalila mavuto ambili.
8 Cifukwa caciŵili n’cakuti, mtundu wa anthu wakhala wopanda ungwilo ndi wocimwa kungocokela pacipanduko ca m’munda wa Edeni. Izi n’zimene munaphunzila mu Nkhani 3. Anthu ocimwa amakonda kwambili kulamulila anthu anzao, ndipo zimenezi zimacititsa kuti pakhale nkhondo, kupondelezana ndi mavuto ambili. (Mlaliki 4:1; 8:9) Cifukwa cacitatu ndi ‘nthawi yatsoka ndi zinthu zakugwa mosayembekezeka.’ (Mlaliki 9:11) Popeza kuti Yehova sindiye Wolamulila dziko lino ndipo samateteza anthu mwakuthupi, anthu angamavutike cifukwa ca tsoka ndi zinthu zakugwa mosayembekezeka.
9. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala otsimikiza kuti Yehova ali ndi cifukwa cabwino cololela kuti anthu apitilize kuvutika?
9 N’zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti Mulungu si amene amacititsa kuti anthu azivutika. Sindiye amene amacititsa nkhondo, upandu, kupondelezana ngakhale ngozi zacilengedwe zimene zimapangitsa anthu kuvutika. Koma ngakhale ndi conco, tifunikabe kudziŵa cifukwa cimene Yehova walolela kuti anthu azivutika. Popeza iye ndi wamphamvuyonse, ndiye kuti ali ndi mphamvu zocotsapo mavuto onse. Nanga n’cifukwa ciani iye sacitapo kanthu? Pokhala kuti Mulungu ndi wacikondi, ayenela kuti ali ndi cifukwa cabwino cololela zimenezi.—1 Yohane 4:8.
SATANA AYAMBITSA NKHANI YAIKULU
10. Kodi Satana anatsutsa ciani? Ndipo anacita bwanji zimenezi?
10 Kuti tidziŵe cifukwa cimene Mulungu walolela anthu kuti azivutika, tiyenela kukumbukila mmene mavuto anayambila. Pamene Satana anacititsa Adamu ndi Hava kupandukila Yehova, anayambitsa nkhani yaikulu. Satana sanatsutse zakuti Yehova ali ndi mphamvu zomuposa. Iye amadziŵa kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malile. Conco, zimene Satana anatsutsa kweni-kweni n’zakuti Yehova ndiye woyenela kulamulila. Mwa kuonetsa ngati kuti Mulungu ndi wabodza ndipo amamana anthu ake zabwino, Satana ananeneza Yehova kuti ndi wolamulila woipa. (Genesis 3:2-5) Mwa ici, Satana anatanthauza kuti mtundu wa anthu ukanakhala ndi umoyo wabwino kwambili popanda ulamulilo wa Mulungu. Kumeneku kunali kuukila Yehova, amene ndiye woyenela kulamulila.
11. N’cifukwa ciani Yehova sanangowaononga apandu a mu Edeni aja?
11 Adamu ndi Hava anapandukila Yehova. Mwa kucita zimenezi, zili ngati io anakamba kuti: ‘Sitifunikila Yehova kuti azitilamulila. Tikhoza kumasankha tokha zoyenela ndi zosayenela.’ Kodi Yehova akanathetsa bwanji nkhani imeneyi? Kodi akanathandiza bwanji anthu ndi angelo kuona kuti opandukawo anali olakwa, ndi kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino koposa? Koma anthu ena angakambe kuti, n’cifukwa ciani Mulungu sanangowaononga opandukawo ndi kulenganso anthu ena? Lingalilo limeneli lingaoneke ngati labwino. Koma Yehova anali atakamba kale colinga cake cofuna kudzaza dziko lapansi ndi ana a Adamu ndi Hava. Ndipo iye anafuna kuti io akhale m’paladaiso padziko lapansi. (Genesis 1:28) Yehova nthawi zonse amakwanilitsa colinga cake. (Yesaya 55:10, 11) Cinanso n’cakuti, Yehova akanaononga apandu a mu Edeni aja, sakanapeleka umboni wotsimikizila kuti Satana ndi wabodza pa zimene ananena kuti Yehova si woyenela kulamulila.
12, 13. Mwa kugwilitsila nchito citsanzo, fotokozani cifukwa cimene Yehova walolela Satana kukhala wolamulila wa dziko lino. Nanga n’cifukwa ciani Mulungu analola anthu kuti ayambe kudzilamulila okha?
12 Tiyeni tione citsanzo. Ganizilani kuti mphunzitsi afotokozela ana a m’kalasi lake mmene angapezele samu inayake. Ndiyeno mwana wina wa m’kalasimo, wanzelu koma wosamvela, akamba kuti njila imene mphunzitsi akuwafotokozela yopezela samuyo ndi yolakwika. Mwana wosamvela ameneyu aumilila kuti njila imene iye adziŵa yopezela samuyo ndiyo yolongosoka. Pocita zimenezi iye atanthauza kuti mphunzitsi wake sangakwanitse kuipeza samuyo. Ana ena naonso aganiza kuti mnzaoyo akamba zoona, ndipo agwilizana naye kutsutsa mphunzitsi wao. Kodi mphunzitsi ameneyu ayenela kucita ciani? Kodi akapitikitsa ana osamvelawo m’kalasi, ana ena adzaganiza ciani? Kodi io sadzakhulupilila kuti mwana wosamvelayo pamodzi ndi ena amene agwilizana naye akamba zoona? Ngati zimenezi zingacitike, ana onse m’kalasimo angayambe kusuliza mphunzitsi wao. Iwo angayambe kuganiza kuti mphunzitsi wao akuopa kuti angadziŵike kuti sadziŵa masamu. Koma bwanji ngati mphunzitsiyo angalole mwana wosamvelayo kuti aonetse anzake mmene angapezele samuyo?
Kodi mwana wa sukulu angakhale woyenela kuphunzitsa kuposa mphunzitsi wake?
13 Yehova wacita zofanana ndi zimene mphunzitsi wa m’citsanzo cimeneci akanayenela kucita. Kumbukilani kuti nkhani ya mu Edeni ija sinakhudze opanduka okhawo. Angelo mamiliyoni ambili anali kupenyelela zocitika zimenezo. (Yobu 38:7; Danieli 7:10) Mmene Yehova anacitila ndi opandukawo zinakhudza angelo onsewo, ndipo zinakhudzanso anthu onse amene anali kudzakhala padziko lapansi. Conco, kodi Yehova wacita ciani? Iye walola kuti Satana aonetse mmene angalamulilile mtundu wa anthu. Mulungu walolanso kuti anthu adzilamulile okha moyang’anilidwa ndi Satana.
14. Kodi pamene Yehova walola anthu kudzilamulila okha, zathandiza angelo ndi anthu kudziŵa ciani?
14 Mphunzitsi wa m’citsanzo cathu cija adziŵa kuti zimene mwana wosamvelayo pamodzi ndi anzake akamba si zoona. Koma adziŵanso kuti kuwapatsa mpata wakuti aonetse njila yao kudzathandiza kalasi lonse kudziŵa kuti io ndi abodza. Ana osamvelawo akalephela kupeza samu imeneyo, ana ena omvela adzadziŵa kuti mphunzitsiyo ndiye woyenelela kuphunzitsa kalasiyo. Iwo tsopano angamvetse cifukwa cimene mphunzitsi angacotsele ana onse osamvela m’kalasimo. Mofananamo, Yehova amadziŵa kuti anthu onse oona mtima pamodzi ndi angelo adzadziŵa kuti Satana ndi opanduka anzake alephela, ndi kuti anthu sangathe kudzilamulila okha. Mofanana ndi Yeremiya, anthu oona mtima ndi angelo adzaphunzila mfundo yofunika yakuti: “Ine ndikudziŵa bwino, inu Yehova, kuti munthu wocokela kufumbi alibe ulamulilo woongolela njila ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo woongolela mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
N’CIFUKWA CIANI WATENGA NTHAWI YAITALI OSACITAPO KANTHU?
15, 16. (a) N’cifukwa ciani Yehova walola kuti anthu avutike kwa nthawi yaitali conco? (b) N’cifukwa ciani sachingiliza zoipa zimenezi kuti zisamacitike?
15 Koma n’cifukwa ciani Yehova walolela kuti anthu avutike kwa nthawi yaitali conco? Ndipo n’cifukwa ciani sachingiliza zoipa kuti zisamacitike? Cabwino, ganizilani zinthu ziŵili zimene mphunzitsi wa m’citsanzo cathu cija sayenela kucita. Coyamba, iye sayenela kuletsa mwana wosamvelayo kuti aonetse njila yake yopezela samuyo. Caciŵili, mphunzitsiyo sayenela kum’thandiza mwana wosamvelayo kupeza samuyo. Mofananamo, ganizilani zinthu ziŵili zimene Yehova anatsimikiza kuti sadzacita. Iye sanaletse Satana ndi onse amene ali kumbali yake kuti aonetse ngati akamba zoona. Conco, kwakhala kofunikila kuti awapatse nthawi yokwanila. Pazaka zonse zimene anthu akhala akudzilamulila, ayesapo mtundu uliwonse wa boma. Pamene mtundu wa anthu wapita patsogolo kwambili mu zasayansi ndi zinthu zina, m’pamenenso kupanda cilungamo, umphawi, upandu ndi nkhondo zikuonjezeleka-onjezeleka. Tsopano ulamulilo wa anthu wacita kuonekelatu kuti walephela!
16 Caciŵili, Yehova sanathandize Satana kulamulila dziko. Mwacitsanzo, ngati Mulungu angachingilize zoipa kuti zisamasacitike, kodi sangakhale akucilikiza ulamulilo wa Satana? Kodi sakanapangitsa anthu kuganiza kuti mwina anthu akhoza kudzilamulila okha popanda vuto lililonse? Yehova akanacita zimenezo, akanacilikiza bodza la Mdyelekezi. Komabe, “n’zosatheka kuti Mulungu aname.”—Aheberi 6:18.
17, 18. Kodi Yehova adzacitapo ciani pa zinthu zonse zimene zaonongeka cifukwa ca ulamulilo wa anthu ndi mphamvu za Satana?
17 Nanga bwanji zinthu zonse zimene zaonongeka panthawi yonse imene anthu akhala opandukila Mulungu? Musaiŵale kuti Yehova ndi wamphamvuyonse. Conco, iye adzathetsa mavuto onse a anthu. Monga mmene taphunzilila kale, dziko lapansi likadzakhala Paladaiso zinthu zonse zimene zinaonongeka zidzakonzedwanso. Kupyolela m’nsembe ya dipo la Yesu, ucimo udzacotsedwa pamodzi ndi zoipa zonse zimene umabweletsa. Ndiponso imfa idzacotsedwa mwa kuukitsa akufa. Conco, Yehova adzagwilitsila nchito Yesu ‘kuononga nchito za Mdyelekezi.’ (1 Yohane 3:8) Yehova adzacita zimenezi panthawi yake yoyenela. Tiyenela kuyamikila kuti Iye sanacitepo kanthu mwamsanga, cifukwa kuleza mtima kwake kwatipatsa mwai wakuti tiphunzile coonadi ndi kuti timutumikile. (2 Petulo 3:9, 10) Koma palipano, Mulungu amafuna anthu amene angam’lambile moona mtima, ndipo amawathandiza kupilila mavuto alionse amene angakumane nao.—Yohane 4:23; 1 Akorinto 10:13.
18 Anthu ena angafunse kuti, Kodi mavuto amenewa sakanapewedwa ngati Mulungu akanalenga Adamu ndi Hava m’njila yakuti n’kosatheka kuti apanduke? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenela kukumbukila mphatso ina yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa.
KODI MUYENELA KUGWILITSILA NCHITO BWANJI MPHATSO IMENE MUNALANDILA KWA MULUNGU?
Mulungu adzakuthandizani kupilila mavuto
19. Kodi Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali iti? Ndipo n’cifukwa ninji tiyenela kuiona kukhala yofunika?
19 Monga mmene tinaonela mu Nkhani 5, anthu analengedwa ndi ufulu wodzisankhila zocita. Kodi mudziŵa kuti imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali? Mulungu anapanga nyama zambili-mbili, ndipo nyama zimenezi zilibe nzelu zopanga cosankha. (Miyambo 30:24) Anthu amakwanitsa kupanga makina amene amangocita ciliconse cimene io afuna kuti acite. Kodi tikanakondwela Mulungu akanatipanga mwa njila imeneyo? Iyai. Ndife okondwa kuti tili ndi ufulu wodzisankhila mtundu wa munthu amene tifuna kukhala, umoyo umene tifuna, anthu amene tifuna kuti akhale mabwenzi athu, ndi zina za conco. Timakondwela kukhala ndi ufulu pa zinthu zina zake, ndipo n’zimene Mulungu amafuna.
20, 21. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tigwilitsile nchito bwino kwambili ufulu wodzisankhila zocita? Ndipo n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?
20 Yehova safuna kuti tizimutumikila mokakamizika. (2 Akorinto 9:7) Mwacitsanzo: Kodi n’ciani cimene cingakondweletse kwambili makolo—pamene mwana wakamba kuti “ndimakukondani” cifukwa wauzidwa ndi munthu wina kukamba zimenezo, kapena pamene wadzikambila yekha kucokela pansi pamtima? Conco, funso n’lakuti, Kodi inu mudzagwilitsila nchito bwanji ufulu wodzisankhila zocita umene Yehova anakupatsani? Satana, Adamu ndi Hava anagwilitsila nchito ufulu wodzisankhila zocita m’njila yoipa kwambili. Iwo anakana Yehova Mulungu. Nanga inu mudzacita ciani?
21 Muli ndi mwai wogwilitsila nchito bwino kwambili ufulu wodzisankhila zocita umenewu. Mwa kucita zimenezi, mungacite mofanana ndi anthu ofika m’mamiliyoni amene asankha kukhala kumbali ya Yehova. Iwo amakondweletsa Mulungu cifukwa amalimbikila kucita zinthu zimene zimatsimikizila Satana kuti ndi wabodza, ndi kuti iye walephela kulamulila anthu. (Miyambo 27:11) Inunso mungakondweletse Mulungu ngati mukhala ndi umoyo umene iye afuna. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimenezi.