LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 13 nkhani 125-133
  • Mmene Mulungu Amaonela Moyo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mulungu Amaonela Moyo
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MMENE TINGALEMEKEZELE MOYO
  • MMENE TINGALEMEKEZELE MAGAZI
  • NJILA YOKHA YOYENELA YOSEŴENZETSA MAGAZI
  • Muzilemekeza Mphatso Ya Moyo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 13 nkhani 125-133

NKHANI 13

Mmene Mulungu Amaonela Moyo

  • Kodi Mulungu amauona bwanji moyo?

  • Nanga kucotsa mimba Mulungu amakuona bwanji?

  • Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza moyo?

1. Kodi analenga zamoyo zonse ndani?

MNENELI Yeremiya anakamba kuti: “Yehova ndi Mulungu woonadi. Iye ndi Mulungu wamoyo.” (Yeremiya 10:10) Ndiponso, Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa zamoyo zonse. Zolengedwa zauzimu zakumwamba zinati kwa iye: “Munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) M’nyimbo yake yotamanda Mulungu, Mfumu Davide anati: “Inu ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Conco, moyo ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.

2. Kodi Mulungu amatisamalila bwanji kuti tikhale ndi moyo?

2 Ndiponso, Yehova amatisamalila kuti tikhale ndi moyo. (Machitidwe 17:28) Amatipatsa cakudya, madzi, mpweya umene timapuma. Ndi amene anatipatsa ngakhale dziko limene tikhalapo. (Machitidwe 14:15-17) Yehova watikonzela zinthu zimenezi mwa njila yakuti tisangalale nao moyo. Koma kuti moyo tisangalale nao mofikapo, tiyenela kudziŵa malamulo a Mulungu ndi kuwatsatila.—Yesaya 48:17, 18.

MMENE TINGALEMEKEZELE MOYO

3. Kodi Mulungu anamva bwanji pamene Kaini anapha Abele?

3 Mulungu amafuna kuti tizilemekeza moyo, ponse paŵili, moyo wathu ndi wa anthu ena. Mwacitsanzo, kale kwambili m’nthawi ya Adamu ndi Hava, mwana wao Kaini anakwiya kwambili cifukwa ca mng’ono wake Abele. Yehova anacenjeza Kaini kuti mkwiyo wake ungam’pangitse kucita chimo lalikulu. Koma Kaini ananyalanyaza cenjezo limenelo. Iye “anam’kantha Abele m’bale wake n’kumupha.” (Genesis 4:3-8) Yehova anamulanga Kaini cifukwa ca kupha m’bale wake.—Genesis 4:9-11.

4. Mu Cilamulo ca Mose, kodi Mulungu anaonetsa bwanji kuti tiyenela kulemekeza moyo?

4 Patapita zaka pafupi-fupi 2,400, Yehova anapatsa Aisiraeli malamulo owathandiza kuti am’tumikile m’njila yoyenela. Cifukwa cakuti malamulo amenewa anapelekedwa kupyolela mwa mneneli Mose, nthawi zina amachedwa kuti Cilamulo ca Mose. Lamulo limodzi m’Cilamulo ca Mose linati: “Usaphe munthu.” (Deuteronomo 5:17) Zimenezi zinaonetsa Aisiraeli kuti Mulungu amaona moyo wa munthu kukhala cinthu camtengo wapatali, ndi kuti anthu ayenela kulemekeza moyo wa anthu ena.

5. Kodi nkhani yocotsa mimba tiyenela kuiona bwanji?

5 Nanga bwanji za moyo wa mwana ali m’mimba? Malinga ndi Cilamulo ca Mose, kupha mwana ali m’mimba kunali kulakwa. Inde, ngakhale moyo wa mwana ali m’mimba ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. (Ekisodo 21:22, 23; Salimo 127:3) Zimenezi zitanthauza kuti kucotsa mimba ni chimo.

6. N’cifukwa ciani sitiyenela kudana ndi munthu mnzathu?

6 Kulemekeza moyo kumaphatikizaponso kuona anthu ena kukhala ofunika. Baibo imati: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha munthu sadzalandila moyo wosatha.” (1 Yohane 3:15) Ngati tifuna kuti tikapeze moyo wosatha, tiyenela kucotselatu m’mitima yathu cidani ciliconse kwa anthu anzathu, cifukwa cidani ndiye cimayambitsa ziwawa zambili. (1 Yohane 3:11, 12) N’cinthu cofunika kwambili kuti tiphunzile kukonda anthu anzathu.

7. Kodi tingaonetse kuti sitimalemekeza moyo ngati timacita zinthu ziti?

7 Nanga bwanji za kulemekeza moyo wa ife eni? Mwacibadwa, ife anthu sitifuna kufa. Koma pali anthu ena amene amaika moyo wao pangozi cifukwa cofuna kusanguluka. Mwacitsanzo, anthu ambili pofuna kuti asanguluke amakoka fodya, camba, kapena kugwilitsila nchito mankhwala osokoneza ubongo. Zinthu zimenezi zimaononga thupi, ndipo kaŵili-kaŵili zimafika ngakhale pakupha anthu amene amazigwilitsila nchito. Munthu amene amazigwilitsila nchito saona moyo kukhala wamtengo wapatali. Zinthu zimenezi n’zonyansa kwa Mulungu. (Aroma 6:19; 12:1; 2 Akorinto 7:1) Kuti titumikile Mulungu movomelezeka, tiyenela kuleka kucita zimenezi. Ngakhale kuti kuleka kungakhale kovuta kwambili, Yehova akhoza kutithandiza kuti tileke. Ndipo iye amayamikila zonse zimene timacita zoonetsa kuti moyo wathu ndi mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa iye.

8. N’cifukwa ciani nthawi zonse tiyenela kukumbukila kupewa ngozi?

8 Ngati timalemekeza moyo, nthawi zonse tidzakumbukila kupewa ngozi. Tidzakhala osamala pocita zinthu, ndipo sitidzaika moyo wathu pangozi pofuna kuti tisanguluke cabe. Tidzapewa kuyendetsa galimoto mosasamala kapena kucita maseŵela oopsa. (Salimo 11:5) Lamulo la Mulungu kwa Aisiraeli linati: “Ukamanga nyumba yatsopano [yamtenje wotambalala] uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopela kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kucokela padengapo.” (Deuteronomo 22:8) Mogwilizana ndi lamulo limeneli, onetsetsani kuti pamasitepe oloŵela m’nyumba yanu pali bwino cakuti munthu sangagwe ndi kuvulala, ndipo phimbani maenje pakhomo kuti musagwele munthu. Ngati muli ndi galimoto kapena coyendela cina, onetsetsani kuti cili mu mkhalidwe wabwino. Tsimikizani kuti nyumba yanu kapena galimoto yanu singabweletse ngozi kwa inu kapena kwa anthu ena.

9. Ngati timalemekeza moyo, kodi tidzapewa kuzicitila ciani nyama?

9 Nanga bwanji za moyo wa nyama? Naonso ndi wamtengo wapatali kwa Mlengi. Mulungu amalola kupha nyama kuti tipeze cakudya ndi zovala, kapena pamene moyo wa anthu ungakhale pangozi ku nyamazo. (Genesis 3:21; 9:3; Ekisodo 21:28) Koma, kucitila nyama nkhanza kapena kuzipha popanda cifukwa n’kulakwa. Kumaonetsanso kuti sitiona moyo kukhala wopatulika.—Miyambo 12:10.

MMENE TINGALEMEKEZELE MAGAZI

10. Kodi Mulungu waonetsa bwanji kuti pali kugwilizana pakati pa moyo ndi magazi?

10 Kaini atapha mng’ono wake Abele, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundililila mu nthaka.” (Genesis 4:10) Pamene Mulungu anali kukamba za magazi a Abele, anali kutanthauza moyo wa Abele. Kaini anapha moyo wa Abele, conco anayenela kulangidwa. Zinali ngati kuti magazi a Abele, kapena kuti moyo wake, unali kulilila Yehova kuti acitepo kanthu. Kugwilizana kwa moyo ndi magazi kunaonekelanso pambuyo pa Cigumula ca m’nthawi ya Nowa. Cigumula cikalibe kucitika, anthu anali kudya cabe zipatso, ndiwo zamasamba, ndi zakudya zina za m’munda monga cimanga ndi nshaŵa. Pambuyo pa Cigumula, Yehova anauza Nowa ndi ana ake kuti: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga thelele laliŵisi ndakupatsani inu zonsezo.” Komabe, Mulungu anaika lamulo lakuti: “Nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” (Genesis 1:29; 9:3, 4) Izi zionetselatu kuti Yehova amagwilizanitsa kwambili moyo ndi magazi a camoyo.

11. Kucokela m’nthawi ya Nowa, kodi Mulungu waletsa kugwilitsila nchito magazi m’njila iti?

11 Timalemekeza magazi mwa kupewa kuwadya. Mu Cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli, iye anawalamula kuti: “Munthu aliyense . . . akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithila magazi ake pansi ndi kuwafocela ndi dothi. . . . Ndauza ana a Isiraeli kuti: ‘Musamadye magazi a nyama iliyonse.’” (Levitiko 17:13, 14) Lamulo la Mulungu la kusadya magazi a nyama, limene linayamba kupelekedwa kwa Nowa zaka 800 kumbuyoko, linali kugwilabe nchito kwa Aisiraeli. Maganizo a Yehova anali odziŵikilatu akuti: Atumiki ake anali kuyenela kudya nyama koma osati magazi. Magazi anayenela kuwathila pansi—kumene kunali ngati kubweza moyo wa nyama imeneyo kwa Mulungu.

12. Motsogoleledwa ndi mzimu woyela, kodi ndi lamulo liti linapelekedwa pa nkhani ya magazi kwa Akristu oyambilila, limene limagwilabe nchito mpaka lelo?

12 Lamulo limeneli limagwilanso nchito pa ife Akristu. M’nthawi ya Akristu oyambilila, atumwi pamodzi ndi amuna ena amene anali otsogolela pakati pa otsatila a Yesu anakumana kuti aone malamulo amene Akristu onse m’mipingo anayenela kumawatsatila. Motsogoleledwa ndi mzimu woyela, anaona kuti ndi bwino kuti asawanyamulitse mtolo wolema, kupatula zinthu zofunika zokhazi zimene ndi kupitiliza kupewa zinthu zopelekedwa nsembe ku mafano, magazi, zopotola, ndi dama. (Machitidwe 15:28, 29; 21:25) Mwa ici, tiyenela ‘kupewa magazi.’ Kwa Mulungu, kucita zimenezi n’kofunika monga mmene kulili kofunika kupewa kupembedza mafano ndi ciwelewele.

A bottle of an alcoholic beverage intravenously injected into a man’s arm

Ngati dokotola wanu wakuletsani kumwela moŵa kukamwa, kodi mukhoza kumauloŵetsa m’thupi mwa kudzilasa nyeleti?

13. Pelekani citsanzo coonetsa kuti kupewa magazi kumaphatikizapo kusaikidwa magazi.

13 Kodi lamulo la kupewa magazi limaphatikizapo kupewa kuikidwa magazi? Inde. Mwacitsanzo: Yelekezani kuti dokotala wakuletsani kumwa moŵa. Kodi zimenezi zingatanthauze kuti wangokuletsani kumwela kukamwa cabe, koma mukhoza kuloŵetsa moŵa m’thupi mwa kudzilasa nyeleti? Mwacionekele ayi. Mofananamo, kupewa magazi kumatanthauza kusaaloŵetsa m’thupi mwathu mwa njila ina iliyonse. Conco, lamulo la kupewa magazi limatanthauza kuti sitiyenela kulola wina aliyense kutiika magazi m’thupi.

14, 15. Ngati madokotala akamba kuti Mkristu afunikila kuikidwa magazi, kodi ayenela kucita ciani? Ndipo n’cifukwa ciani?

14 Nanga bwanji ngati Mkristu wavulala kwambili, kapena ngati afunikila opaleshoni yaikulu? Tinene kuti madokotala amuuza kuti ngati sadzaikidwa magazi adzafa. Mwacidziŵikile Mkristu ameneyo sangafune kufa. Pofuna kulemekeza mphatso yocokela kwa Mulungu ya moyo, iye angavomele njila zina zocilitsila zimene zilipo, zosaphatikizapo kugwilitsila nchito magazi molakwa.

15 Kodi n’cinthu canzelu kuti Mkristu aphwanye lamulo la Mulungu cabe kuti akhaleko ndi moyo kwakanthawi m’dziko lino? Yesu anati: “Aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza.” (Mateyu 16:25) Mwacibadwa sitimafuna kufa. Koma ngati tiphwanya lamulo la Mulungu kuti tipulumutse moyo wathu m’dziko lino, tikhoza kutaya mwai wa kupeza moyo wosatha. Conco, tingacite bwino kukhulupilila malamulo a Mulungu olungama. Tiyenela kukhala ndi cidalilo conse kuti ngati tingafe m’dziko lino, Wotipatsa Moyo adzatikumbukila pa ciukililo ndi kutipatsanso moyo.—Yohane 5:28, 29; Aheberi 11:6.

16. Kodi atumiki a Mulungu ndi otsimikiza mtima za ciani pa nkhani ya magazi?

16 Masiku ano, atumiki a Mulungu okhulupilika ali otsimikiza mtima kutsatila lamulo lake pa nkhani ya magazi. Iwo amapewa kudya magazi m’njila ina iliyonse. Ndipo amakana ngakhale kuikidwa magazi monga njila yocilitsila matenda ao.a Sakaikila ngakhale pang’ono kuti Mulungu, amene anapanga magazi, ndiye adziŵa bwino zinthu zofunikila kwa io. Kodi simukhulupilila zimenezi?

NJILA YOKHA YOYENELA YOSEŴENZETSA MAGAZI

17. M’nthawi ya Aisiraeli, kodi Yehova Mulungu analola njila imodzi yokha iti yoseŵenzetsa magazi?

17 Cilamulo ca Mose cinaonetsa njila imodzi cabe imene inali yoyenela kuseŵenzetsa magazi. Ponena za kulambila kumene Aisiraeli anayenela kucita, Yehova anawalamula kuti: “Moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikilani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbilani macimo. Zili conco popeza magazi ndiwo amaphimba macimo.” (Levitiko 17:11) Aisiraeli anali kuti akacimwa, macimo ao anali kukhululukidwa mwa kupeleka nsembe ya nyama, ndi kuika magazi ena a nyamayo paguwa la nsembe m’cihema, kapena kuwaika pakacisi wa Mulungu. Njila yokha yoyenela kuseŵenzetsa magazi inali pa nsembe zimenezi.

18. Kodi magazi a Yesu angatibweletsele mapindu ndi madalitso ati?

18 Akristu oona sanalamulidwe kuti azitsatila Cilamulo ca Mose. Conco sanali kupeleka nsembe za nyama, ndi kuika magazi ake paguwa la nsembe. (Aheberi 10:1) Komabe, m’nthawi ya Aisiraeli kugwilitsila nchito magazi paguwa la nsembe kunaimila nsembe yapadela imene inali kudzapelekedwa mtsogolo. Nsembe imeneyi inali Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. Monga mmene tinaphunzilila mu Nkhani 5 ya buku lino, Yesu anapeleka moyo wake mwa kulola kuti magazi ake akhetsedwe kaamba ka ife. Pambuyo pake anabwelela kumwamba kukapeleka kwa Mulungu mtengo wa magazi ake kamodzi kunthawi yonse. (Aheberi 9:11, 12) Zimenezi zinakhala maziko okhululukilapo macimo athu, ndipo zinatisegulila mwai wakuti tikalandile moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Kukamba zoona, kuseŵenzetsa magazi m’njila imeneyi kwabweletsa madalitso ambili. (1 Petulo 1:18, 19) Kukhulupilila magazi a Yesu amene anakhetsedwa ndiko njila yokha yopezela cipulumutso.

A Christian in a hospital explaining to her doctor what the Bible says about blood

Kodi mungalemekeze bwanji moyo ndi magazi?

19. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tikhale “oyela pa mlandu wa magazi a anthu onse”?

19 Kodi sitiyenela kumuyamikila kwambili Yehova Mulungu kaamba ka mphatso ya moyo imeneyi? Ndipo kodi zimenezi, siziyenela kutilimbikitsa kugwila nchito youzako anthu ena za mwai wopezela moyo wosatha ngati akhulupilila nsembe ya Yesu? Tikaganizila anthu ena mmene Yehova amawaganizilila, cidzatilimbikitsa kugwila nchito imeneyo mwakhama ndi mwacangu. (Ezekieli 3:17-21) Tikamagwila nchito imeneyi ndi mtima wonse, tidzanena mau amene mtumwi Paulo ananena akuti: “Ine ndine woyela pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisileni kanthu, koma ndinakuuzani cifunilo conse ca Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Kuuzako anthu ena za Mulungu ndi colinga cake ndiyo njila yabwino kwambili yoonetsela kuti mumalemekeza kwambili moyo ndi magazi.

TIMALEMEKEZA MOYO

  • Mwa kusapha mwana ali m’mimba

  • Mwa kuleka makhalidwe oipa

  • Mwa kucotselatu m’mitima yathu cidani ciliconse cimene tili naco ndi anthu anzathu

1. An unborn child; 2. A person crushing a pack of cigarettes; 3. Two friends from different ethnic backgrounds

a Kuti mudziŵe njila zina zocilitsila matenda, popanda kuikidwa magazi, onani mapeji 13 mpaka 17 m’kabuku kakuti How Can Blood Save Your Life? kolembedwa ndi Mboni za Yehova.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Moyo ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.—Salimo 36:9; Chivumbulutso 4:11.

  • Kucotsa mimba ni chimo, cifukwa ngakhale moyo wa mwana ali m’mimba uli wamtengo wapatali kwa Mulungu.—Ekisodo 21:22, 23; Salimo 127:3.

  • Timalemekeza moyo mwa kusauika paciswe ndi mwa kupewa kudya magazi.—Deuteronomo 5:17; Machitidwe 15:28, 29.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani