LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 16 nkhani 154-163
  • Onetsani Kuti Mumacilikiza Kulambila Koona

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Kuti Mumacilikiza Kulambila Koona
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ZIFANIZILO NDI KULAMBILA MIZIMU YA MAKOLO
  • AKRISTU OYAMBILILA SANALI KUKONDWELELA KIRISIMASI
  • MMENE KIRISIMASI INAYAMBILA
  • KODI CIYAMBI CAKE CILIBE KANTHU?
  • KHALANI WOZINDIKILA POCITA ZINTHU NDI ENA
  • NANGA BWANJI AKAKHALA ACIBANJA?
  • CITANI ZINTHU ZOGWILIZANA NDI KULAMBILA KOONA
  • Sankhani Kulambila Mulungu
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kodi Zikondwelelo Zonse Zimam’sangalatsa Mulungu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Zikondwelelo Zonse Zimakondweletsa Mulungu?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Zikondwelelo Zimene Mulungu Amadana Nazo
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Onaninso Zina
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 16 nkhani 154-163

NKHANI 16

Onetsani Kuti Mumacilikiza Kulambila Koona

  • Kodi Baibo imaphunzitsa ciani pa nkhani yogwilitsila nchito zifanizilo polambila?

  • Nanga Akristu amawaona bwanji maholide a zipembedzo?

  • Kodi anthu ena mungawafotokozele bwanji zimene mumakhulupilila popanda kuwakhumudwitsa?

1, 2. Pambuyo pa kucoka m’cipembedzo conama, kodi muyenela kudzifunsa funso liti? Ndipo n’cifukwa ciani kudzifunsa funso limeneli n’kofunika?

TINENE kuti ndi nthawi yamvula ndipo dela lonse limene mumakhala lasefukila ndi madzi oipitsidwa ndi matenda oopsa monga kolela. Miyoyo ya anthu onse ili pangozi cifukwa madzi onse, kaya ndi a kupompi kapena a pacitsime ali ndi matendawo. Kodi mungacite ciani? Mwacionekele mungacoke m’dela limenelo. Koma ngakhale mutacita zimenezo mungakhalebe ndi nkhawa yakuti, ‘Kodi matenda sanaloŵe kale m’thupi mwanga?’

2 N’cimodzi-modzi ndi cipembedzo conama. Baibo imaphunzitsa kuti kulambila kumeneko n’kodetsedwa ndi ziphunzitso ndi miyambo yoipa. (2 Akorinto 6:17) Ndiye cifukwa cake n’cinthu cofunika kuti mucoke mu “Babulo Wamkulu,” amene ndi ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conama. (Chivumbulutso 18:2, 4) Kodi mwacita kale zimenezi? Ngati yankho lanu ndi inde, tikuyamikilani kwambili. Koma pali zina zofunikila kucita kuonjezela pa kudzilekanitsa ndi cipembedzo conama. Muyenelanso kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikali kucitako zinthu zina zokhudza kulambila konama? Tiyeni tione zina.

ZIFANIZILO NDI KULAMBILA MIZIMU YA MAKOLO

3. (a) Pa nkhani ya kugwilitsila nchito zifanizilo, kodi Baibo imakamba ciani? Ndipo n’cifukwa ciani maganizo a Mulungu amenewa angakhale ovuta kuti ena awavomeleze? (b) Ngati mungakhale ndi zinthu zilizonse zokhudza kulambila konama, kodi muyenela kucita ciani?

3 Anthu ena akhala ndi zifanizilo kapena malo olambililapo mizimu ya makolo m’nyumba zao kapena ku malo ena kwa zaka zambili. Kodi inu muli ndi zimenezi? Ngati muli nazo, mungacione kukhala cinthu cosayenela kapena colakwika kupemphela kwa Mulungu popanda kugwilitsila nchito zinthuzo. Ndipo mwina munafika pozikonda kwambili zinthu zimenezo. Koma Mulungu ndi amene ayenela kutiuza mmene tiyenela kum’lambilila, ndipo Baibo imaphunzitsa kuti iye safuna kuti tizigwilitsila nchito zifanizilo. (Ekisodo 20:4, 5; Salimo 115:4-8; Yesaya 42:8; 1 Yohane 5:21) Conco, mungaonetse kuti mumacilikiza kulambila koona mwa kuononga cinthu cina ciliconse cokhudza kulambila konama cimene mungakhale naco. Muyenela kuona zinthu zimenezi monga mmene Yehova amazionela, kuti ndi zinthu ‘zonyansa.’—Deuteronomo 27:15.

4. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti kulambila mizimu ya makolo kulibe phindu lililonse? (b) N’cifukwa ciani Yehova analetsa anthu ake kutengako mbali m’zocitika zilizonse zokhulupilila mizimu?

4 Kulambila mizimu ya makolo kulinso kofala kwambili m’zipembedzo zambili zonama. Akalibe kuphunzila coonadi ca m’Baibo, anthu ena anali kukhulupilila kuti akufa ali ndi moyo ku malo a mizimu, ndi kuti akhoza kuthandiza anthu amoyo kapena kuwavulaza. Mwina munali kucita zinthu zambili kuti mukondweletse mizimu ya makolo anu amene anamwalila. Koma monga mmene munaphunzilila mu Nkhani 6 ya buku lino, akufa samakhala ndi moyo kumalo alionse. Conco, ngati wina ayesa kukamba nao, palibe phindu lililonse limene angapeze. Mauthenga alionse amene angaoneke ngati ocokela kwa wokondedwa wathu amene anamwalila, m’ceni-ceni amacokela ku ziŵanda. Conco, Yehova analetsa Aisiraeli kuti asamakambe ndi anthu akufa, kapena kutengako mbali m’zocitika zilizonse zokhulupilila mizimu.—Deuteronomo 18:10-12.

Forms of image and ancestor worship practiced around the world

5. Ngati kale munali kugwilitsila nchito zifanizilo, kapena munali kulambila mizimu ya makolo, kodi tsopano muyenela kucita ciani?

5 Ngati kale munali kugwilitsila nchito zifanizilo kapena kulambila mizimu ya makolo, kodi tsopano muyenela kucita ciani? Muyenela kumaŵelenga ndi kusinkha-sinkha nkhani za m’Baibo zimene zidzakuonetsani mmene Mulungu amaonela zinthu zimenezi. Muzipemphela kwa Yehova tsiku lililonse ndi kumuuza kuti mumafunitsitsa kucilikiza kulambila koona. Ndiponso muzimupempha kuti muziona zinthu mmene iye amazionela.—Yesaya 55:9.

AKRISTU OYAMBILILA SANALI KUKONDWELELA KIRISIMASI

6. Kodi anthu amati Kirisimasi ndi tsiku lokumbukila ciani? Nanga ophunzila a Yesu oyambilila anali kukondwelela tsiku limeneli?

6 Kulambila kwa munthu kungadetsedwe ndi cipembedzo conama pamene akondwelela maholide ofala. Tiyeni tione citsanzo ca Kirisimasi. Anthu ena amati Kirisimasi ndi kukumbukila kubadwa kwa Yesu Kristu, ndipo pafupi-fupi cipembedzo ciliconse cimene amati ndi Cacikristu cimakondwelela tsiku limenelo. Komabe, palibe umboni woonetsa kuti ophunzila a Yesu oyambilila anali kukondwelela tsiku limenelo. Buku lina linati: “Patapita zaka 200 kucokela pamene Kristu anabadwa, palibe munthu amene anali kudziŵa za tsiku limenelo, ndipo ndi anthu ocepa cabe amene anali ndi cidwi ndi tsiku leni-leni limene Yesu anabadwa.”

7. Panthawi ya ophunzila a Yesu oyambilila, kodi zikondwelelo za tsiku la kubadwa zinali kudziŵika ndi ciani?

7 Ngakhale ngati ophunzila a Yesu akanadziŵa tsiku leni-leni limene iye anabadwa, sakanalikondwelela. Cifukwa ciani? Cifukwa buku lina linati, Akristu oyambilila “anali kuona kukondwelela tsiku la kubadwa kwa munthu aliyense ngati mwambo wacikunja.” (The World Book Encyclopedia) Baibo imangochula zikondwelelo ziŵili cabe za tsiku la kubadwa kwa mafumu aŵili amene sanali kulambila Yehova. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Anthu anali kucita zikondwelelo za tsiku la kubadwa polemekeza milungu yacikunja. Mwacitsanzo, pa tsiku la May 24 Aroma anali kukondwelela tsiku la kubadwa kwa mulungu wao wamkazi Dayana. Patsiku lotsatila, anali kukondwelela tsiku la kubadwa kwa mulungu wao dzuŵa, wochedwa kuti Apollo. Conco, kukondwelela tsiku la kubadwa kunali kudziŵika ndi miyambo yacikunja osati Cikristu.

8. Fotokozani mmene zikondwelelo za tsiku la kubadwa zimagwilizanilana ndi kukhulupilila mizimu.

8 Pali cifukwa cina cimene Akristu oyambilila sakanakondwelela tsiku la kubadwa kwa Yesu. Ophunzila ake ayenela kuti anali kudziŵa kuti tsiku la kubadwa linali kuloŵetsamo kukhulupilila mizimu. Mwacitsanzo, Agiriki ambili ndi Aroma a m’nthawi zakale, anali kukhulupilila kuti pa kubadwa kwa munthu aliyense pamakhala mzimu umene umateteza munthu ameneyo kwa umoyo wake wonse. Buku lina limati: “Anthu amene sanali Akristu m’nthawi imeneyo anali kukondwelela tsiku la kubadwa cifukwa anali kuganiza kuti kucita zimenezo kungacititse milungu yao kuti iteteze munthu amene anabadwa patsiku limenelo.” (The Lore of Birthdays) Mwacidziŵikile, Yehova sangasangalale ndi cikondwelelo ciliconse cimene cingagwilizanitse Yesu ndi kukhulupilila mizimu. (Yesaya 65:11, 12) Nanga n’cifukwa ciani anthu ambili amakondwelela Kirisimasi?

MMENE KIRISIMASI INAYAMBILA

9. Kodi tsiku la December 25 linakhala bwanji tsiku lokondwelela kubadwa kwa Yesu?

9 Anthu anayamba kukumbukila tsiku la kubadwa kwa Yesu pa December 25, patapita zaka pafupi-fupi 300 kucokela pamene iye anali padziko lapansi. Koma tsiku limeneli si limene Yesu anabadwa. Malinga ndi umboni umene ulipo, iye ayenela kuti anabadwa mu October.a Nanga n’cifukwa ciani anthu anasankha December 25? Malinga n’kunena kwa buku lina, zioneka kuti m’kupita kwa nthawi Akristu a dziko “anafuna kuti tsiku la kubadwa kwa Yesu likhale patsiku limene Aroma anali kukondwelela kubadwa kwa ‘dzuŵa losagonjetseka.’” (The New Encyclopædia Britannica) M’nyengo yozizila, pamene dzuŵa linali kucepa mphamvu, anthu akunja anali kukhala ndi mapwando kuti dzuŵa libweletsenso kutentha ndi kuwala kwake. Tsiku la December 25 linaonedwa kukhala tsiku limene dzuŵa linayamba ulendo wake wobwelela. Pofuna kutembenuza anthu akunja, atsogoleli a cipembedzo anatengela phwando limeneli ndi kulipanga kukhala la “Cikristu.”b

10. N’cifukwa ciani anthu sanali kukondwelela Kirisimasi m’nthawi yakale?

10 Kwa nthawi yaitali anthu avomeleza kuti Kirisimasi inayambila kucikunja. Cifukwa cakuti ciyambi cake si ca m’malemba, Kirisimasi inaletsedwa ku England ndi ku maiko ena a ku America m’zaka za m’ma 1600. Munthu aliyense amene anali kupezeka kuti wangokhala panyumba tsiku la Kirisimasi anali kulipilitsidwa faindi. Komabe, pasanapite nthawi yaitali, anthu anayambanso kutsatila miyambo yakale, ndi kukhazikitsanso miyambo ina yatsopano. Kirisimasi inakhalanso holide yofala kwambili, ndipo mpaka masiku ano ikali yofala m’maiko ambili. Koma cifukwa ca mgwilizano umene ulipo pakati pa Kirisimasi ndi cipembedzo conama, anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu samakondwelela tsiku limeneli, kapena maholide ena amene anacokela ku cikunja.c

KODI CIYAMBI CAKE CILIBE KANTHU?

11. N’cifukwa ciani anthu ena amakondwelela maholide? Ndipo n’ciani cimene ciyenela kukhala cofunika kwambili kwa ife?

11 Ngakhale kuti anthu ena amavomeleza kuti maholide amenewa monga Kirisimasi anacokela ku cikunja, amaonabe kuti sikulakwa kuwakondwelela. Ndi iko komwe, anthu ambili samaganiza za kulambila konama pamene amakondwelela maholide. Ndipo amaona kuti maholide amenewa amapeleka mpata wakuti mabanja akhale ndi maceza capamodzi. Kodi ndi mmene inu mumaganizila? Ngati mumaganiza conco, ndiye kuti kukonda banja lanu n’kumene kumacititsa kuti muziona ngati kucilikiza kulambila koona n’kovuta, osati kukonda cipembedzo conama. Dziŵani kuti Yehova, amene anayambitsa banja, amafuna kuti inu mukhale paubale wabwino ndi acibanja anu. (Aefeso 3:14, 15) Koma mungalimbitse ubale umenewo m’njila zimene Mulungu amakondwela nazo. Pa cinthu ciliconse cimene mumaciona kuti n’cofunika kwambili, Mtumwi Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti covomelezeka kwa Ambuye n’citi.”—Aefeso 5:10.

A dirty piece of candy in a gutter

Kodi mungadye switi imene mwatola m’madzi onyansa a mu mfolo?

12. Pelekani citsanzo coonetsa cifukwa cimene tiyenela kupewela miyambo ndi zikondwelelo zimene ciyambi cake n’coipa.

12 Mwina mumaganiza kuti masiku ano anthu angakondwelele maholide mosasamala kanthu za mmene anayambila. Kodi ciyambi cake cili ndi kanthu? Inde! Mwacitsanzo: Tinene kuti mwaona switi m’madzi onyansa mu mfolo. Kodi mungaitole ndi kudya? Kutali-tali! Cifukwa switi imeneyo ni yonyansa. Monga switi imeneyo, maholide angaoneke abwino kwambili, koma anacokela ku miyambo yodetsedwa. Kuti tionetse kuti timacilikiza kulambila koona, tiyenela kukhala ndi maganizo amene mneneli Yesaya anali nao, pamene anauza olambila oona kuti: “Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa.”—Yesaya 52:11.

KHALANI WOZINDIKILA POCITA ZINTHU NDI ENA

13. Kodi ndi mavuto ati amene angakhalepo mukaleka kukondwelela maholide?

13 N’zoona kuti mukaleka kukondwelela maholide, zinthu zina zingayambe kukhala zovuta kwa inu. Mwacitsanzo, anzanu a kunchito angadabwe cimene simukondwelela nao pamodzi maholide kunchito kwanu. Ndiye mungacite bwanji ngati munthu wina wakupatsani mphatso ya Kirisimasi? Kodi n’kulakwa kuilandila? Nanga bwanji ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wa cipembedzo cina? Kodi mungacite ciani kuti ana anu asaone kuti akumanidwa zinthu zabwino cifukwa cakuti simukondwelela maholide?

14, 15. Kodi mungacite ciani ngati wina wakuuzani mau okufunilani cikondwelelo cabwino, kapena ngati afuna kukupatsani mphatso?

14 Kuzindikila bwino n’kofunika kuti mudziŵe mocitila ndi vuto lililonse. Pamene wina wakuuzani mau okufunilani cikondwelelo cabwino, onani mmene mungayankhile mosamala. Koma bwanji ngati ndi munthu amene mumadziŵa, kapena mnzanu amene mumagwila naye nchito nthawi zonse? Kodi muyenela kucita ciani? Pamenepo, mungafunikile kufotokoza bwino-bwino. Koma pa zocitika zonse, muyenela kukhala wozindikila. Baibo imati: “Nthawi zonse mau anu azikhala acisomo, okoma ngati kuti mwawathila mcele, kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.” (Akolose 4:6) Samalani kuti muonetse ulemu kwa ena. Afotokozeleni bwino-bwino zimene mumakhulupilila. Auzeni kuti simukana kupatsana mphatso kapena kukhala ndi maceza capamodzi, kungoti mumafuna kucita zimenezo panthawi ina.

15 Koma bwanji ngati munthu wina afuna kukupatsani mphatso? Zimadalila ndi mmene mkhalidwe ulili. Wopeleka mphatsoyo angakambe kuti: “Ndidziŵa kuti simutengako mbali pa cikondwelelo cimeneci. Komabe, ndingofuna cabe kukupatsankoni mphatso iyi.” Malinga ndi mkhalidwe umene ulipo, mungaone kuti kulandila mphatso imeneyo sikungakhale kukondwelela holide imeneyo. Koma ngati wopeleka mphatsoyo sadziŵa zimene mumakhulupilila, musanalandile mufotokozeleni kuti sim’makondwelela tsiku limenelo. Zimenezi zingamuthandize kumvetsa cifukwa cake mudzalandila mphatso imeneyo pamene inu simupatsa ena mphatso patsiku limenelo. Koma musalandile mphatso imeneyo ngati yapelekedwa ndi colinga cokuyesani, kuona ngati mumatsatila zimene mumakhulupilila, kapena ngati mudzalephela pofuna cabe zinthu zakuthupi.

NANGA BWANJI AKAKHALA ACIBANJA?

16. Kodi mungacite bwanji zinthu mosamala pa nkhani zokhudza zikondwelelo za maholide?

16 Koma bwanji ngati acibanja anu sakhulupilila zimene inu mumakhulupilila? Apanso muyenela kucita mosamala. Palibe cifukwa coyambila mkangano pa mwambo ulionse kapena cikondwelelo cimene io afuna kucita. M’malo mwake, lemekezani zimene io amakhulupilila, monga mmene inunso mumafunila kuti alemekeze zimene mumakhulupilila. (Mateyu 7:12) Pewani kucita zilizonse zimene zingakupangitseni kutengako mbali pa kukondwelela tsiku limenelo. Komanso, muyenela kukhala ololela pa zinthu zimene sizikupangitsani kutengako mbali kweni-kweni pa cikondwelelo cimeneco. Ngakhale ndi conco, nthawi zonse citani zinthu m’njila imene sidzavutitsa cikumbumtima canu.—1 Timoteyo 1:18, 19.

17. Kodi mungacite ciani kuti ana anu asamaone kuti akumanidwa zinthu zabwino pamene aona anthu ena akukondwelela maholide?

17 Kodi mungacite ciani kuti ana anu asaone monga kuti akumanidwa zinthu zabwino cifukwa cakuti simucitako zikondwelelo zosemphana ndi malemba? Kweni-kweni zimadalila zimene mumawacitila panthawi zina mkati mwa caka. Makolo ena amapatula nthawi yakuti apatse ana ao mphatso. Zina mwa mphatso zabwino kwambili zimene mungapatse ana anu ndizo nthawi yanu ndi cisamalilo canu cacikondi.

CITANI ZINTHU ZOGWILIZANA NDI KULAMBILA KOONA

Scenes of a family preaching the good news, worshipping together at a Christian meeting, and exchanging gifts at a picnic

Kucita zinthu zogwilizana ndi kulambila koona kumabweletsa cimwemwe ceni-ceni

18. Kodi misonkhano yacikristu imakupatsani bwanji mpata woonetsa kuti mumacilikiza kulambila koona?

18 Kuti mukondweletse Mulungu, muyenela kupewa kulambila konama pocilikiza kulambila koona. Kodi kucita zimenezi kumaphatikizapo ciani? Baibo imati: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena a cizoloŵezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tionjezele kucita zimenezi, maka-maka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheberi 10:24, 25) Misonkhano yacikristu imakupatsani mipata yabwino yolambilila Mulungu m’njila imene amavomeleza. (Salimo 22:22; 122:1) Pa misonkhano imeneyo, pamakhala ‘kulimbikitsana’ pakati pa Akristu okhulupilika.—Aroma 1:12.

19. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti muziuzako anthu ena zinthu zimene mumaphunzila m’Baibo?

19 Njila ina imene mungaonetsele kuti mumacilikiza kulambila koona ndiyo kuuzako ena zinthu zimene mwaphunzila m’Baibo ndi Mboni za Yehova. Zoona, anthu ambili “akuusa moyo ndi kubuula” cifukwa ca zinthu zoipa zimene zimacitika m’dziko masiku ano. (Ezekieli 9:4) Mwina mumadziŵa anthu ena amene amamva conco. Bwanji osawauzako za ciyembekezo ca zamtsogolo cimene cimapezeka m’Baibo? Pamene mugwilizana ndi Akristu oona ndi kumauzako anthu ena mfundo zabwino za coonadi zimene mwaphunzila m’Baibo, mudzapeza kuti maganizo ofuna kucitako miyambo ya kulambila konama adzayamba kutha pang’ono-pang’ono. Dziŵani ndithu kuti mudzakhala acimwemwe, ndipo mudzalandila madalitso ambili ngati mucilikiza kulambila koona.—Malaki 3:10.

a Onani Zakumapeto, pamapeji 221 mpaka 222.

b Phwando lochedwa Satanaliya linali cifukwa cinanso cosankhila December 25. Phwando limeneli lolemekeza mulungu waciroma wa zaulimi linali kucitika pa December 17 mpaka 24. Pa phwando la Satanaliya panali kukhala madyelelo, kusangalala, ndi kupatsana mphatso.

c Kuti mudziŵe zambili za mmene Akristu oona amaonela maholide ena ofala, onani Zakumapeto, pamapeji 222 mpaka 223.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Zifanizilo kapena kulambila mizimu ya makolo siziyenela kugwilitsilidwa nchito pa kulambila koona.—Ekisodo 20:4, 5; Deuteronomo 18:10-12.

  • N’kulakwa kutengako mbali pa zikondwelelo zimene zinayambila ku cikunja.—Aefeso 5:10.

  • Akristu oona ayenela kukhala osamala pamene afotokozela ena zimene amakhulupilila.—Akolose 4:6.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani