LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 18 nkhani 174-183
  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CIDZIŴITSO NDI CIKHULUPILILO N’ZOFUNIKA
  • KUUZAKO ENA COONADI CA M’BAIBO
  • KULAPA NDI KUTEMBENUKA
  • KUDZIPELEKA WEKHA
  • KUCOTSA MANTHA AKUTI MUNGALEPHELE
  • UBATIZO NI UMBONI WAKUTI MUNTHU ADZIPELEKA
  • TANTHAUZO LA UBATIZO WANU
  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi N’dzipeleke Kwa Mulungu Kuti N’kabatizike?
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 18 nkhani 174-183

NKHANI 18

Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenela kucita coyamba kuti mukhale woyenela kubatizika?

  • Kodi muyenela kucita ciani kuti mudzipeleke kwa Mulungu?

  • Kodi tiyenela kubatizika pa cifukwa capadela citi?

1. N’cifukwa ciani nduna ya ku Itiyopiya inapempha kuti ibatizike?

M’ZAKA za zana loyamba, nduna ya ku Itiyopiya inafunsa funso lakuti: “Taonani! Si awa madzi ambili. Cikundiletsa kubatizidwa n’ciani?” Mkristu wina dzina lake Filipo, anatsimikizila nduna imeneyi kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa. Atakhudzidwa ndi zimene anaphunzila m’Malemba, Mwaitiyopiya uja anacitapo kanthu. Anaonetsa kuti anali kufuna kubatizika.—Machitidwe 8:26-36.

Philip and the Ethiopian court official talking about baptism

2. N’cifukwa ciani muyenela kuganizila zakuti mubatizike tsopano?

2 Ngati munaphunzila ndi mmodzi wa Mboni za Yehova nkhani zoyambilila za buku lino, mwina inunso mungadzifunse kuti, ‘Kodi cindiletsa ine kubatizika n’ciani?’ Kufika pano, mwaphunzila za lonjezo la Baibo lonena za moyo wosatha m’Paladaiso. (Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Mwaphunzilanso za mmene akufa alili kweni-kweni ndi ciyembekezo cakuti adzaukitsidwa. (Mlaliki 9:5; Yohane 5:28, 29) Mwina mwakhala mukupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo mwadzionela nokha mmene zocita zao zimaonetsela kuti ndi olambila oona. (Yohane 13:35) N’kutheka kuti, mwayamba kale kukhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu, ndipo cimeneci ndico cinthu cofunika kwambili.

3. (a) Kodi ndi lamulo liti limene Yesu anapeleka kwa otsatila ake? (b) Kodi ubatizo wa m’madzi uyenela kucitika bwanji?

3 Kodi mungaonetse bwanji kuti mufuna kutumikila Mulungu? Yesu anauza otsatila ake kuti: ‘Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila. Muziwabatiza.’ (Mateyu 28:19) Yesu iye mwini anapeleka citsanzo mwa kubatizika m’madzi. Iye sanangowazidwa kapena kungothilidwa madzi pamphumi iyai. (Mateyu 3:16) Mau acigiriki otembenuzidwa kuti “kubatiza” amatanthauza “kuviika m’madzi.” Conco, ubatizo wacikristu umatanthauza kumiza kapena kuti kuviika thupi lonse m’madzi.

4. Kodi ubatizo wa m’madzi umaonetsa ciani?

4 Ubatizo wa m’madzi ndi wofunika kwa anthu onse amene afuna kukhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu. Ubatizo umaonetsa poyela kuti mufuna kutumikila Mulungu. Umaonetsa kuti mumakondwela kucita cifunilo ca Yehova. (Salimo 40:7, 8) Koma kuti mukhale woyenela kubatizika, pali zinthu zingapo zofunika zimene muyenela kucita coyamba.

CIDZIŴITSO NDI CIKHULUPILILO N’ZOFUNIKA

5. (a) Kodi cinthu cofunika coyamba cimene muyenela kucita kuti mubatizike n’ciani? (b) Nanga n’cifukwa ciani misonkhano ya mpingo ndi yofunika kwambili?

5 Mwayamba kale kucita cinthu cofunika coyamba. M’njila iti? Mwa kuphunzila za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Mwina mumacita zimenezi mwa kukhala ndi munthu wina amene amakuphunzitsani Baibo nthawi zonse. (Yohane 17:3) Koma palinso zina zambili zimene mufunika kuphunzila. Akristu amafuna kukhala ndi cidziŵitso colongosoka ponena za cifunilo ca Mulungu. (Akolose 1:9) Kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova kudzakuthandizani kwambili pambali imeneyi. N’kofunika kwambili kupezeka pamisonkhano imeneyi. (Aheberi 10:24, 25) Kupezeka pamisonkhano nthawi zonse kudzakuthandizani kuonjezela cidziŵitso canu ponena za Mulungu.

Two of Jehovah’s Witnesses studying the Bible with a man

Kupeza cidziŵitso colongosoka ca Mau a Mulungu n’kofunika kwambili kuti munthu abatizike

6. Kodi muyenela kudziŵa zonse za m’Baibo kuti mubatizike?

6 Koma sikuti muyenela kudziŵa zonse za m’Baibo kuti mubatizike. Nduna ya ku Itiyopiya inaliko ndi cidziŵitso cinacake, koma inafunikilabe wina woithandiza kumvetsetsa mbali zina za m’Malemba. (Machitidwe 8:30, 31) Ngakhale inu, pakali zambili zimene mufunika kudziŵa. Ndipo kuphunzila za Mulungu sikumatha. (Mlaliki 3:11) Koma mukalibe kubatizika, mufunika kudziŵa ndi kukhulupilila ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. (Aheberi 5:12) Ziphunzitso zimenezo zimaphatikizapo kudziŵa zoona pa nkhani ya mmene akufa alili, ndi kudziŵanso kufunika kwa dzina la Mulungu ndi Ufumu wake.

7. Kodi kuphunzila Baibo kudzakuthandizani kucita ciani?

7 Komabe, cidziŵitso cokha si cokwanila. Mufunikanso cikhulupililo, monga mmene Baibo imakambila pa Aheberi 11:6 kuti: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” Malemba amatiuza kuti pamene anthu ena mu mzinda wa Akorinto anamva uthenga umene Akristu anali kulalikila, “anayamba kukhulupilila ndi kubatizidwa.” (Machitidwe 18:8) N’cimodzi-modzinso ndi inu. Kuphunzila Baibo kudzakuthandizani kukhulupilila kuti Baibo ndi Mau ouzilidwa a Mulungu. Kudzakuthandizaninso kukhulupilila malonjezo a Mulungu, ndi kukhulupililanso nsembe ya Yesu yopulumutsa anthu.—Yoswa 23:14; Machitidwe 4:12; 2 Timoteyo 3:16, 17.

KUUZAKO ENA COONADI CA M’BAIBO

8. Kodi n’ciani cingakulimbikitseni kuuzako ena zimene mumaphunzila?

8 Pamene cikhulupililo canu cikula, mudzaona kuti kudzakhala kovuta kungosunga mu mtima mwanu zimene mumaphunzila. (Yeremiya 20:9)Mudzakhala wosonkhezeleka kuuzako ena za Mulungu ndi zolinga zake.—2 Akorinto 4:13.

A Bible student along with his teacher in the public ministry, sharing the good news with a man

Cikhulupililo ciyenela kukusonkhezelani kuuzako ena zimene mumakhulupilila

9, 10. (a) Kodi mungayambe kuuzako ndani coonadi ca m’Baibo? (b) Nanga muyenela kucita ciani mukafuna kuyamba kulalikila ndi mpingo wa Mboni za Yehova?

9 Mungayambe kuuzako ena coonadi ca m’Baibo mwa kukambitsilana ndi acibanja anu, mabwenzi, anansi, ndi anzanu a kunchito. M’kupita kwa nthawi, mungavomelezedwe kuyamba kuyenda ndi mpingo m’nchito yolalikila. Mukafuna kuyamba kulalikila ndi mpingo, kambilanani nkhaniyo ndi Mboni imene imakuphunzitsani Baibo. Iye akaona kuti muoneka kukhala woyenelela kuyamba kupita mu ulaliki, makonzedwe adzapangidwa akuti inu ndi mphunzitsi wanu mukakumane ndi akulu aŵili a mpingo.

10 Zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa akulu pampingo, amene amasamalila nkhosa za Mulungu. (Machitidwe 20:28; 1 Petulo 5:2, 3) Akulu akaona kuti mumamvetsetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo ndi kuzikhulupilila, mumatsatila mfundo za m’Baibo paumoyo wanu, ndipo muli wofunitsitsa kukhala Mboni ya Yehova, adzakuuzani kuti ndinu woyenelela kuyamba kulalikila uthenga wabwino ndi mpingo, monga wofalitsa wosabatizika

11. Kodi anthu ena angafunikile kucita ciani kuti awavomeleze kuyamba kulalikila ndi mpingo?

11 Koma nthawi zina akulu angaone kuti pali zina zimene mufunikila kukonza paumoyo wanu mukalibe kuyamba kulalikila ndi mpingo. Zimenezi zingakhale zinthu zimene mwakhala mukucita kumbali. Mwa ici, mukalibe kupempha kuti mukhale wofalitsa wosabatizika, muyenela kulekelatu kucita macimo aakulu, monga ciwelewele, kuledzela, ndi mankhwala osokoneza ubongo.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21.

KULAPA NDI KUTEMBENUKA

12. N’cifukwa ciani kulapa n’kofunika?

12 Palinso zinthu zina zimene mufunika kucita kuti mubatizike. Mtumwi Petulo anakamba kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe.” (Machitidwe 3:19) Kulapa kumatanthauza kumvela cisoni cocokela pansi pa mtima pa cinthu coipa cimene wacita. Conco, kulapa n’kofunika ngati munthu anali ndi umoyo wocita zaciwelewele. Koma ngakhale munthu amene sanali kucita zoipa kweni-kweni, nayenso afunikilabe kulapa. Cifukwa ciani? Cifukwa anthu onse ndi ocimwa ndipo afunikila cikhululukilo ca Mulungu. (Aroma 3:23; 5:12) Mukalibe kuphunzila Baibo, simunali kudziŵa cifunilo ca Mulungu. Conco, m’pomveka kuti umoyo wanu sunali wogwilizana kweni-kweni ndi cifunilo ca Mulungu. Ndiye cifukwa cake kulapa n’kofunika kwambili.

13. Kodi kulapa n’ciani?

13 Pambuyo pa kulapa munthu afunikila kutembenuka. Si nkhani ya kumvela cisoni cabe iyai. Mufunikila kusiilatu umoyo wanu wakumbuyo, ndi kutsimikiza mu mtima mwanu kuti kucokela panthawi imeneyo mudzayamba kucita zinthu zoyenela. Kuti mubatizike, mufunikila kulapa ndi kutembenuka.

KUDZIPELEKA WEKHA

14. Kodi mufunikanso kucita cinthu cofunika citi kuti mubatizike?

14 Koma palinso cinthu cina cofunika kwambili kuti munthu abatizike. Mufunikila kudzipeleka nokha kwa Yehova Mulungu.

A Bible student dedicating himself to God in prayer

Kodi munadzipeleka kwa Mulungu m’pemphelo?

15, 16. Kodi munthu amadzipeleka bwanji kwa Mulungu? Ndipo n’ciani cimalimbikitsa munthu kuti adzipeleke?

15 Pamene mwadzipeleka kwa Yehova Mulungu, kupitila m’pemphelo locokela pansi pa mtima, mumamulonjeza kuti mwapeleka moyo wanu wonse kwa iye ku nthawi zonse. (Deuteronomo 6:15) Koma n’cifukwa ciani munthu afunikila kudzipeleka? Tiyeni tiyelekezele kuti mwamuna waona mbeta. Coyamba amafunsila kuti adziŵe zambili za mkaziyo. Akamva kuti ndi wakhalidwe labwino amakopeka naye. Mwacibadwa, m’kupita kwa nthawi amamufunsila. N’zoona kuti cikwati cimabweletsa udindo waukulu pa iye. Koma cikondi cimam’pangitsa kukwatilabe.

16 Mukafika pomudziŵa bwino Yehova ndi kumukonda, mumayamba kumutumikila ndi mtima wonse, kapena kuti modzikhuthula. Munthu aliyense wofuna kutsatila Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ayenela ‘kudzikana yekha.’ (Maliko 8:34) Timadzikana tokha mwa kutsimikiza kuti zofuna za mtima wathu sizitilepheletsa kumvela Mulungu m’zinthu zonse. Zimenezi zitanthauza kuti, mukalibe kubatizika, kucita cifunilo ca Yehova Mulungu kuyenela kukhala cinthu cofunika kwambili paumoyo wanu.—1 Petulo 4:2.

KUCOTSA MANTHA AKUTI MUNGALEPHELE

17. N’cifukwa ciani anthu ena amaopa kuti adzipeleke kwa Mulungu?

17 Anthu ena amaopa kuti adzipeleke kwa Yehova. Amaganiza kuti akakhala Mkristu wodzipeleka, Mulungu angawaimbe mlandu akalakwa. Conco, poopa kuti angalephele ndi kukhumudwitsa Yehova, amaona kuti cingakhale cabe bwino kusadzipeleka.

18. Kodi n’ciani cingakusonkhezeleni kuti mudzipeleke kwa Yehova?

18 Pamene muyamba kukonda Yehova, mudzakhala wofunitsitsa kudzipeleka kwa iye ndi kucita zimene amafuna paumoyo wanu. (Mlaliki 5:4) Ndipo mukabatizika, mudzafuna kuti “muziyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, “kuti muzimukondweretsa pa chilichonse.” (Akolose 1:10) Cifukwa ca kukonda kwanu Mulungu, simudzavutika kucita cifunilo cake. Mosakaikila, ngakhale inu mudzavomeleza zimene mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” —1 Yohane 5:3.

19. N’cifukwa ciani simuyenela kuopa kudzipeleka kwa Mulungu?

19 Sikuti mufunikila kukhala wangwilo kuti mudzipeleke kwa Mulungu iyai. Yehova amadziŵa zolephela zanu, ndipo sayembekezela kuti mucite zimene simungakwanitse. (Salimo 103:14) Cimene iye amafuna n’cakuti mupambane, ndipo adzakucilikizani ndi kukuthandizani. (Yesaya 41:10) Musakaikile ngakhale pang’ono. Ngati mudalila Yehova ndi mtima wonse, ‘adzaongola njila zanu.’—Miyambo 3:5, 6.

UBATIZO NI UMBONI WAKUTI MUNTHU ADZIPELEKA

20. Kodi munthu akadzipeleka kwa Yehova, n’cifukwa ciani siiyenela kungokhala nkhani yodziŵa yekha cabe?

20 Kuganizila pa zinthu zimene tafotokoza kungakuthandizeni kudzipeleka kwa Yehova m’pemphelo. Munthu aliyense amene amakonda Mulungu afunikilanso ‘kulengeza poyela kuti akapulumuke.’ (Aroma 10:10) Kodi mungacite bwanji zimenezi?

A Christian man baptizing a new disciple, raising him up from being fully immersed in water

Ubatizo umatanthauza kufa ku umoyo wakale ndi kukhalanso ndi umoyo watsopano wocita cifunilo ca Mulungu

21, 22. Kodi mungalengeze bwanji poyela cikhulupililo canu?

21 Dziŵitsani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu pampingo wanu kuti mufuna kubatizika. Iye adzakonza zakuti akulu ena akakambilane ndi inu mafunso okhudza ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Akulu amenewo akaona kuti ndinu woyenelela, adzakuuzani kuti mudzabatizika pamsonkhano wotsatila.a Pa misonkhano imeneyi pamakambidwa nkhani yofotokoza tanthauzo la ubatizo. Ndiyeno pambuyo pake, mkambi amapempha onse opita ku ubatizo kuyankha mafunso aŵili osavuta, monga njila imodzi imene ‘amalengezela poyela’ cikhulupililo cao.

22 Ubatizo ndi umene umaonetsa poyela kuti munadzipeleka kwa Mulungu, ndi kuti tsopano ndinu Mboni ya Yehova. Anthu opita ku ubatizo amamizidwa thupi lonse m’madzi kuonetsa poyela kuti anadzipeleka kwa Yehova.

TANTHAUZO LA UBATIZO WANU

23. Kodi kubatizika “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela” kumatanthauza ciani?

23 Yesu anakamba kuti ophunzila ake adzabatizika “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela.” (Mateyu 28:19) Zimenezi zimatanthauza kuti munthu wopita ku ubatizo amazindikila ulamulilo wa Yehova Mulungu ndi wa Yesu Kristu. (Salimo 83:18; Mateyu 28:18) Amazindikilanso nchito ya mzimu woyela wa Mulungu, kapena mphamvu yake yogwila nchito.—Agalatiya 5:22, 23; 2 Petulo 1:21.

24, 25. (a) Kodi ubatizo umaimila ciani? (b) Nanga nkhani yotsatila idzayankha funso liti?

24 Komabe, ubatizo si mwambo cabe womiza munthu m’madzi iyai. Umaimila cinthu cina cofunika kwambili. Kumizidwa m’madzi kumatanthauza kuti mwafa ku umoyo wanu wakale. Kuvuuka m’madzi kumatanthauza kuti tsopano mwakhalanso ndi moyo kuti mucite cifunilo ca Mulungu. Kumbukilaninso kuti munadzipeleka kwa Yehova Mulungu iye mwini, osati ku nchito, kwa anthu ena, kapena ku bungwe lililonse. Kudzipeleka kwanu ndi ubatizo ndico ciyambi ca ubwenzi wanu ndi Mulungu—mgwilizano wanu wolimba ndi iye.—Salimo 25:14.

25 Pamene mwabatizika sindiye kuti mwapulumuka kale iyai. Yesu Kristu anati ‘amene adzapilila mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuka.’ (Mateyu 24:13) Ubatizo ndi ciyambi cabe ca njila ya ku cipulumutso. Conco, funso n’lakuti, Kodi muyenela kucita ciani kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu? Nkhani yathu yotsilizila idzayankha funso limeneli.

a Ubatizo umacitika pamisonkhano ikulu-ikulu ya Mboni za Yehova caka ciliconse.

ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA

  • Ubatizo wa Cikristu umacitika mwa kumiza thupi lonse m’madzi, osati kuwaza cabe madzi.—Mateyu 3:16.

  • Kuti munthu abatizike, coyamba ayenela kuphunzila kuti akhale ndi cidziŵitso, ndiyeno aonetse cikhulupililo, alape, atembenuke, ndipo cotsilizila adzipeleke yekha kwa Mulungu.—Yohane 17:3; Machitidwe 3:19; 18:8.

  • Kuti mudzipeleke kwa Yehova, muyenela kudzikana nokha, monga mmene anthu ena anadzikanila okha kuti atsatile Yesu.—Maliko 8:34.

  • Ubatizo umatanthauza kufa ku umoyo wakale ndi kukhalanso ndi umoyo watsopano wocita cifunilo ca Mulungu.—1 Petulo 4:2.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani