NKHANI 19
Khalanibe M’cikondi ca Mulungu
Kodi kukonda Mulungu kumatanthauza ciani?
Nanga tingakhalebe bwanji m’cikondi ca Mulungu?
Kodi Yehova adzawadalitsa bwanji anthu amene akhalabe m’cikondi cake?
Kodi mudzam’panga Yehova kukhala pothaŵila panu m’nthawi monga yacimphepo ino?
1, 2. N’kuti kumene tingathaŵile masiku ano kuti tipeze citetezo?
YELEKEZELANI kuti muyenda mu mseu ndipo kuli cimphepo camphamvu. Kumwamba kwacita mdima cifukwa ca mitambo. Ndiyeno, mphezi ziyamba kung’anima, mabingu akugunda, basi cimvula puu! Muthamanga kuti mupeze pobisalila mvula. Ndiyeno muona khumbi, kapena kuti kanyumba kobisalamo mvula. Khumbi limenelo ndi lolimba, ndipo mkati mwake ndi mouma bwino. Mosakaikila, mudzati ‘mwai wanga ndi umenewu!’
2 Mofananamo, ife tikhala m’nthawi imene ili monga ya cimphepo. Zinthu padziko zikungoipila-ipila. Koma pali malo acitetezo kumene tingathaŵile kuti tisungike bwino. Kodi malo amenewo n’ciani? Onani zimene Baibo imaphunzitsa: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothaŵilapo panga ndi malo anga acitetezo, Mulungu wanga amene ndimamukhulupilila.’”—Salimo 91:2.
3. Kodi tingam’pange bwanji Yehova kukhala pothaŵila pathu?
3 Ganizani cabe! Yehova, Mlengi ndi Mfumu ya cilengedwe conse, akhoza kukhala malo athu othaŵilako. Akhoza kutiteteza, cifukwa ndi wamphamvu kuposa munthu aliyense. Akhozanso kutithandiza pa vuto lililonse limene tingakumane nalo. Ngakhale anthu ena ativulaze kapena kuticitila cinthu coipa ciliconse, Yehova akhoza kukonzanso zinthu. Kodi tingam’pange bwanji Yehova kukhala pothaŵila pathu? Tingacite zimenezo mwa kum’dalila. Ndiponso, Mau a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Mudzisunge nokha m’cikondi ca Mulungu.” (Yuda 21) Inde, tiyenela kukhalabe m’cikondi ca Mulungu, posunga mgwilizano wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Tikacita zimenezi, tidzakhala otsimikiza kuti tam’panga Yehova kukhala pothaŵila pathu. Koma kodi mgwilizano umenewu tingaukhazikitse bwanji pakati pa ife ndi Mulungu?
TIKADZIŴA CIKONDI CA MULUNGU NDI KUCITAPO KANTHU TIMAONETSA KUYAMIKILA
4, 5. Kodi ndi njila zina ziti zimene Yehova waonetsela cikondi cake kwa ife?
4 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tifunikila kudziŵa mmene Yehova waonetsela cikondi cake kwa ife. Ganizilani zinthu zimene mwaphunzila m’Baibo kupitila m’buku lino. Monga Mlengi, Yehova anatipatsa dziko lapansi kukhala malo athu abwino okhalapo. Anatiikilaponso cakudya ca mwana alilenji, madzi, cuma cocokela m’zacilengedwe, nyama zokondweletsa, ndi malo okongola. Monga Mlembi wa Baibo, Mulungu watidziŵitsa dzina lake ndi makhalidwe ake. Ndiponso, Mau ake amatiuza kuti iye anatumiza Yesu, Mwana wake wokondedwa, kuti abwele padziko lapansi kudzavutika ndi kutifela. (Yohane 3:16) Kodi mphatso imeneyo itanthauzanji kwa ife? Imatipatsa ciyembekezo ca tsogolo labwino kwambili.
5 Koma ciyembekezo cathu cokhala ndi tsogolo labwino cimadalilanso cinthu cina cimene Mulungu anacita. Yehova anakhazikitsa boma lakumwamba, Ufumu Waumesiya. Posacedwa ufumuwo udzacotsa mavuto onse amene alipo, ndi kukonza dziko lonse kukhala paladaiso. Ganizilani cabe! Tikhoza kudzakhala m’dziko limenelo mwa mtendele ndi mwa cimwemwe kwamuyaya. (Salimo 37:29) Koma pali pano, Mulungu watipatsa malangizo a mmene tingakhalile ndi umoyo wabwino. Watipatsanso mphatso ya pemphelo, imene ndi njila yokamba ndi Mulungu panthawi iliyonse. Zimenezi ndi njila zocepa cabe zimene Yehova waonetsela cikondi cake kwa anthu onse, ndi kwa inu.
6. Kodi mungaonetse bwanji kuti mumayamikila cikondi cimene Yehova amaonetsa kwa inu?
6 Funso lofunika kuti mudzifunse ndi ili: Kodi ndingaonetse bwanji kuti ndimayamikila cikondi ca Mulungu? Anthu ambili angakambe kuti, “Inenso ndiyenela kumukonda Yehova.” Kodi ndi mmene inunso muganizila? Yesu anakamba kuti lamulo limeneli ndilo lalikulu pa malamulo onse. Iye anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Kunena zoona, pali zifukwa zambili zimene muyenela kumukondela Yehova Mulungu. Koma kodi kukonda Yehova ndi mtima wonse, moyo wonse, ndi maganizo anu onse, kumatanthauza kumvela cabe mu mtima mwanu kuti mumam’konda?
7. Kodi kukonda Mulungu kumatanthauza kumvela cabe mu mtima kuti mumam’konda? Fotokozani.
7 Monga mmene Baibo imakambila, kukonda Mulungu sikuyenela kukhala mu mtima cabe. N’zoona kuti cikondi ca mu mtima kwa Yehova cili cofunika. Koma cikondi cimeneco m’poyambila cabe cikondi ceni-ceni cimene mungakhale naco kwa iye. Tingayelekezele ndi cipatso. Kanjele ka cipatso n’kofunika kuti pakhale mtengo wa zipatso. Koma bwanji ngati mwapempha munthu wina kuti akupatseni cipatso kuti mudye? Kodi mungakhutile ngati angakupatseni kanjele cabe ka cipatso cimeneco? Kutali-tali! Mofananamo, cikondi ca mu mtima kwa Yehova Mulungu ndi poyambila cabe. Baibo imaphunzitsa kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Kuti cikondi kwa Mulungu cikhale ceni-ceni, ciyenela kubala zipatso. Ciyenela kuonekela m’zocita zathu.—Mateyu 7:16-20.
8, 9. Kodi tingaonetse bwanji kuti Mulungu timam’konda ndipo timayamikila zimene amaticitila?
8 Timaonetsa kuti timakonda Mulungu pamene tisunga malamulo ake, ndi kugwilitsila nchito mfundo zake za makhalidwe abwino. Kucita zimenezi sikovuta, cifukwa malamulo a Yehova amatithandiza kukhala ndi umoyo wabwino, wacimwemwe, ndi wokhutilitsa. (Yesaya 48:17, 18) Pamene titsatila malangizo a Yehova paumoyo wathu, timaonetsa Atate wathu wakumwamba kuti timayamikila kwambili zonse zimene amaticitila. N’zacisoni kuti ndi anthu ocepa cabe amene amaonetsa kuyamikila. Koma ife sitifuna kuti tikhale osayamikila, monga mmene anthu ena a m’nthawi ya Yesu analili. Panthawi ina, Yesu anacilitsa anthu odwala khate okwana 10, koma mmodzi yekha ndi amene anabwelela kukaonga zikomo. (Luka 17:12-17) Ife tifuna kukhala monga mmodzi woyamikila uja, osati aja 9 osayamikila.
9 Kodi malamulo a Yehova amene tiyenela kutsatila ndiwo ati? Ambili tinawaphunzila kale m’buku lino, koma tiyeni tikumbutsaneko ocepa cabe. Kutsatila malamulo a Mulungu kudzatithandiza kuti tikhalebe m’cikondi cake.
YANDIKILANI KWA YEHOVA NTHAWI ZONSE
10. N’cifukwa ciani kupitiliza kuphunzila za Yehova Mulungu n’kofunika? Fotokozani citsanzo.
10 Kuphunzila za Yehova kumatithandiza kwambili kuti tiyandikile kwa iye. N’cinthu cimene sitiyenela kuleka. Tiyeni tiyelekezele kuti kwazizila kwambili, ndipo inu muotha moto panja usiku. Kodi moto ukayamba kucepa, mukhoza kungouyang’ana mpaka kuzima? Iyai. Mudzapitiliza kusonkhela nkhuni kuti upitilize kuyaka kwambili. Mukapanda kucita zimenezo mungakongwe, ndipo moyo wanu ukhoza kukhala pangozi. Monga mmene nkhuni zimakolezela moto, cidziŵitso cathu conena za Mulungu cidzapitiliza kusonkhezela cikondi cathu kwa Yehova kuti cikhale colimba.—Miyambo 2:1-5.
Mofanana ndi moto, cikondi canu kwa Yehova cimafunikila kucisonkhelela nkhuni kuti moto wake usazime
11. Kodi zimene Yesu anali kuphunzitsa otsatila ake zinali kuwakhudza bwanji?
11 Yesu anafuna kuti otsatila ake asaleke kukonda Yehova, ndi kuti Mau ake a coonadi apitilize kukhala amoyo ndi amphamvu m’mitima yao. Pamene Yesu anaukitsidwa, anaphunzitsa otsatila ake aŵili za maulosi a m’Malemba a Ciheberi amene anakwanilitsika mwa iye. Kodi zinawakhudza bwanji? Iwo pambuyo pake anakamba kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumila pamene anali kulankhula nafe mumseu, ndi kutifotokozela Malemba momveka bwino?”—Luka 24:32.
12, 13. (a) Kwa anthu oculuka masiku ano, kodi cacitika n’ciani pankhani ya kukonda Mulungu ndi Baibo? (b) Nanga tingacite ciani kuti cikondi cathu cisazilale?
12 Pamene munayamba kuphunzila zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni, kodi inunso simunayambe kumva mu mtima mwanu cisangalalo, kulaka-laka kuuzako ena za coonadi, ndi cikondi kwa Mulungu? Mosakaikila ndi mmene munamvelela. Ndipo enanso ambili amamvela cimodzi-modzi. Koma nchito tsopano ili pa kusunga cikondi cimeneco kuti cikhalebe cotentha, ndi kuti cipitilize kukula. Sitifuna kutengela mzimu wa dziko lino. Yesu anakambilatu kuti: “Cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mateyu 24:12) Koma kodi mungacite ciani kuti kukonda kwanu Yehova ndi coonadi ca m’Baibo kusazilale?
13 Pitilizani kuphunzila za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Yohane 17:3) Muyenela kusinkha-sinkha, kapena kuti kuganizilapo mozama pa zimene mumaphunzila m’Mau a Mulungu. Pocita zimenezi muyenelanso kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndaŵelenga izi zimandiphunzitsa ciani ponena za Yehova Mulungu? Kodi zimandipatsa zifukwa zoonjezeleka ziti zomukondela Yehova ndi mtima wanga wonse, maganizo anga onse, ndi moyo wanga wonse?’ (1 Timoteyo 4:15) Kusinkha-sinkha kwa conco kudzathandiza kuti cikondi canu kwa Yehova cizikhala camphamvu nthawi zonse.
14. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kuti cikondi cathu kwa Yehova cikhale camphamvu nthawi zonse?
14 Njila ina imene mungasungile cikondi canu kwa Yehova kukhalabe camphamvu ndiyo kupemphela nthawi zonse. (1 Atesalonika 5:17) Mu Nkhani 17 ya buku lino, tinaphunzila kuti pemphelo ndi mphatso yapadela yocokela kwa Mulungu. Monga mmene kukambitsana momasuka nthawi zonse kumalimbikitsila ubwenzi pakati pa anthu, naonso ubwenzi wathu ndi Yehova umakhala wolimba ngati timakambitsana naye m’pemphelo nthawi zonse. Tiyeni tipewe kupeleka mapemphelo amwambo—kumangobweleza mau popanda tanthauzo, kapena popanda kuwaganizilapo kweni-kweni. Tizikamba ndi Yehova monga mmene mwana angakambile ndi atate wake amene amam’konda. N’zoona kuti tiyenela kukamba naye mwaulemu. Komabe, pokamba naye tizimuchulila zinthu momasuka ndi moona mtima. (Salimo 62:8) Inde, phunzilo laumwini la Baibo ndi pemphelo locokela pansi pa mtima ni mbali zofunika kwambili pa kulambila kwathu. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu.
PEZANI CIMWEMWE PA KULAMBILA KWANU
15, 16. N’cifukwa ciani tiyenela kuona nchito yolalikila za Ufumu kukhala mwai ndi cuma capadela?
15 Phunzilo la Baibo laumwini ndi pemphelo ndiye zinthu zimene tingacite patokha monga mbali ya kulambila kwathu. Koma tsopano tiyeni tikambilane mbali ina ya kulambila imene timaicita kwa anthu: kuuzako ena zimene timakhulupilila. Kodi inu munayamba kuuzako ena mfundo za coonadi zimene mumaphunzila m’Baibo? Ngati mumacita zimenezo, muli ndi mwai wapadela kwambili. (Luka 1:74) Pamene tiuzako ena zimene timaphunzila ponena za Yehova Mulungu, timagwila nchito yofunika kwambili imene Akristu onse anauzidwa kuti azicita. Nchito imeneyi ni yolalikila uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
16 Mtumwi Paulo anaona utumiki wake kukhala cinthu camtengo wapatali, ndipo anati unali cuma kwa iye. (2 Akorinto 4:7) Kukamba ndi anthu za Yehova Mulungu ndi zolinga zake ni nchito yabwino kwambili imene mungacite. Nchito imeneyi ndi yotumikila Bwana wabwino kupambana onse, ndipo imabweletsa madalitso osaneneka. Mwa kugwilako nchito imeneyi, mumathandiza anthu oona mtima kuti ayandikile kwa Atate wathu wakumwamba, ndi kuti apitilize kuyenda pa njila ya ku moyo wosatha. Kodi pangakhale nchito iliyonse yopambana imeneyi? Cina n’cakuti, kucitila umboni za Yehova ndi Mau ake kumaonjezela cikhulupililo canu. Kumalimbitsanso cikondi canu kwa iye. Ndipo Yehova amayamikila kwambili kuyesa-yesa kwanu. (Aheberi 6:10) Kukhala wotangwanika ndi nchito imeneyi kumakuthandizani kukhalabe m’cikondi ca Mulungu.—1 Akorinto 15:58.
17. N’cifukwa ciani utumiki wa Cikristu ufunika kucitika mofulumila masiku ano?
17 Tiyenela kukumbukila kuti nchito yolalikila za Ufumu ifunika kucitika mofulumila kwambili. N’cifukwa ciani? Cifukwa Baibo imakamba kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwela mofulumila kwambili.” (Zefaniya 1:14) Inde, nthawi ili kubwela mofulumila pamene Yehova adzaononga dongosolo lonse la zinthu. Conco, m’pofunika kuti anthu acenjezedwe! Afunika kudziŵa kuti ino ndiyo nthawi yosankha Yehova kukhala Mfumu yao. Mapeto “sadzacedwa.”—Habakuku 2:3.
18. Kodi n’cifukwa ciani tiyenela kulambila Yehova poyela pamodzi ndi Akristu oona?
18 Yehova amafuna kuti tizim’lambila poyela pamodzi ndi Akristu oona. Ndiye cifukwa cake Mau ake amakamba kuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizoloŵezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tionjezele kucita zimenezi, maka-maka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheberi 10:24, 25) Pamene tasonkhana ndi okhulupilila anzathu pamisonkhano ya Cikristu, timakhala ndi mwai wabwino kwambili wotamanda Mulungu wathu wokondedwa ndi kum’lambila. Timalimbikitsananso ndi kutsitsimulana wina ndi mnzake.
19. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tilimbikitse cikondi mu mpingo wa Cikristu?
19 Pamene tisonkhana pamodzi ndi olambila Yehova anzathu, timalimbikitsa cikondi ndi ubwenzi mu mpingo. N’cinthu cofunika kwambili kuti tiziona zabwino mwa ena, monga mmene Yehova amaonela zabwino mwa ife. Tisayembekezele ungwilo kwa okhulupilila anzathu. Kumbukilani kuti tonse timayesa-yesa kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Koma aliyense ali pamsinkhu wosiyana wa kuuzimu. (Akolose 3:13) Ngati mugwilizana ndi anthu amene amakonda Yehova kwambili, mudzayamba kukula mwa kuuzimu. Zoona, kulambila Yehova pamodzi ndi abale ndi alongo anu a kuuzimu kudzakuthandizani kukhalabe m’cikondi ca Mulungu. Kodi Yehova amawadalitsa bwanji amene amam’lambila mokhulupilika, ndi kukhalabe m’cikondi cake?
LIMBIKILANI KUTI MUPEZE “MOYO WENI-WENI”
20, 21. Kodi “moyo weni-weni” ndi uti? Ndipo n’cifukwa ciani ndi ciyembekezo cokondweletsa?
20 Yehova amapatsa atumiki ake okhulupilika mphoto ya moyo. Koma kodi ni moyo wa mtundu wanji? Cabwino, kodi inu muli ndi moyo? Ambili tingayankhe kuti n’zosacita kufunsa. Ndi iko komwe, nanga sitimapuma, sitimadya, ndipo sitimamwa? Inde tili ndi moyo. Ndipo tikakondwela, nthawi zina timacita kukamba kuti, “Koma uwu ndiwo umoyo weni-weni!” Komabe, Baibo imaonetsa kuti m’lingalilo lofunika kwambili, palibe munthu amene ali ndi moyo weni-weni.
Yehova amafuna kuti inunso mukapeze “moyo weni-weni.” Kodi mudzaupeza?
21 Mau a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuti tigwile mwamphamvu moyo weni-weni.’ (1 Timoteyo 6:19) Mau amenewa amaonetsa kuti “moyo weni-weni” ndi umene timayembekezela kudzakhala nao mtsogolo. Inde, pamene tidzakhala angwilo, tidzapeza moyo weni-weni, cifukwa tidzakhala ndi moyo umene Mulungu anali kufuna kuti tikhale nao poyamba. Potsilizila pake, tidzakhala m’paladaiso padziko lapansi mwamtendele, mwacimwemwe, ndi thanzi labwino. Panthawi imeneyo tidzakhala ndi “moyo weni-weni”—moyo wosatha. (1 Timoteyo 6:12) Kodi ciyembekezo cimeneci si cokondweletsa?
22. Kodi mungacite ciani kuti ‘mugwile moyo weni-weni’?
22 Kodi tingacite ciani kuti ‘tigwile moyo weni-weni’? Pa mfundo imeneyi, Paulo analimbikitsa Akristu “kuti azicita zabwino” ndi ‘kukhala olemela pa nchito zabwino.’ (1 Timoteyo 6:18) Conco, n’zoonekelatu kuti zimadalila kwambili mmene timatsatilila mfundo za coonadi zimene taphunzila m’Baibo. Koma kodi Paulo anatanthauza kuti tingapeze “moyo weni-weni” mwa kucita nchito zabwino? Iyai, cifukwa malonjezo amtengo wapatali amenewa, kweni-kweni timakhala nao tikalandila “cisomo ca Mulungu.” (Aroma 5:15, Buku Lopatulika) Ngakhale n’conco, Yehova amakondwela kupeleka mphoto imeneyi kwa anthu amene amamutumikila mokhulupilika. Amafuna kuti inunso mukapeze “moyo weni-weni” umenewo. Moyo wosatha umenewu, udzakhala wa cimwemwe ndi wa mtendele. Ndipo ndi umene anthu onse amene amakhalabe m’cikondi ca Mulungu adzalandila.
23. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu?
23 Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti, Kodi ndimalambila Mulungu monga mmene Baibo imakambila?’ Ngati tsiku ndi tsiku timadzifunsa funso limeneli, ndipo yankho lathu limakhala lakuti inde, ndiye kuti tili panjila yoyenela. Tingakhale ndi cidalilo cakuti Yehova ndiye pothaŵila pathu. Iye adzateteza anthu ake okhulupilika m’masiku otsiliza ano ovuta. Ndipo Yehova adzatipulumutsa kuloŵa m’dziko latsopano laulemelelo limene layandikila. Tidzakhala okondwela cotani nanga’ kukhalako panthawi imeneyo ndi kuona zimenezi! Tidzakhalanso okondwa kwambili kuti tinasankha bwino m’masiku otsiliza ano! Ngati tingacite zimenezi panthawi ino, tidzapeza “moyo weni-weni,” monga mmene Yehova Mulungu anafunila kuti ukalile poyamba, moyo wamuyaya!