LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 195-nkhani 197 pala. 3
  • Kugwilitsila Nchito Dzina la Mulungu ndi Kudziŵa Tanthauzo Lake

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kugwilitsila Nchito Dzina la Mulungu ndi Kudziŵa Tanthauzo Lake
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Dzina la Mulungu N’ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Kodi Yehova N’ndani?
    Kuyankha Mafunso Okhudza Baibo
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 195-nkhani 197 pala. 3

ZAKUMAPETO

Kugwilitsila Nchito Dzina la Mulungu ndi Kudziŵa Tanthauzo Lake

KODI lemba la Masalimo 83:18 analitembenuza bwanji, m’Baibo yanu? Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika analitembenuza kuti: “Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” Mabaibo angapo naonso amatembenuza vesi limeneli mofanana ndi Baibo imeneyi. Komabe, m’Mabaibo ambili mulibe dzina lakuti Yehova, m’malo mwake muli maina audindo monga “Ambuye” kapena “Wamuyaya.” Kodi pa vesi limeneli payenela kulembedwa dzina liti, laudindo kapena lakuti Yehova?

[Cithunzi papeji 195]

Dzina la Mulungu m’zilembo za Ciheberi

Vesi limeneli limakamba za dzina linalake. Mu Ciheberi coyambilila cimene mbali yaikulu ya Baibo inalembedwamo, pa vesi limeneli pali dzina leni-leni la Mulungu. Dzinali linalembedwa m’zilembo za Ciheberi zakuti (YHWH). M’Cinyanja, kalembedwe kodziŵika kwambili ka dzinali ndi “Yehova.” Kodi dzina limeneli limapezeka cabe pa vesi imodzi m’Baibo? Iyai. Limapezeka m’zilembo zoyambilila za Malemba Aciheberi nthawi zokwana 7,000.

Kodi dzina la Mulungu ndi lofunika motani? Ganizilani pemphelo la citsanzo limene Yesu Kristu anapeleka. Limayamba conco: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9) Panthawi ina, Yesu anapemphela kwa Mulungu kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Mulungu anayankha kucokela kumwamba mwakunena kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.” (Yohane 12:28) Mwacionekele, dzina la Mulungu ndi lofunika kwambili. Nanga n’cifukwa ciani otembenuza ena sanalembe dzina limeneli m’Mabaibo amene io anatembenuza koma m’malo mwake analembamo maina audindo?

Cioneka kuti pali zifukwa ziŵili zazikulu zimene anacitila conco. Coyamba, ambili amanena kuti dzinali siliyenela kugwilitsidwa nchito cifukwa kachulidwe kake koyambilila sikadziŵika masiku ano. Ciheberi cakale cinali kulembedwa popanda mavawelo. Conco, masiku ano palibe munthu amene angatiuze motsimikiza mmene anthu m’nthawi za m’Baibo anali kuchulila kalembedwe ka YHWH. Komabe, kodi zimenezi ziyenela kutilepheletsa kugwilitsila nchito dzina la Mulungu? M’nthawi ya m’Baibo, dzina lakuti Yesu anali kulichula kuti Yeshuwa kapena mwina kuti Yehoshuwa. Palibe amene anganene kachulidwe kake keni-keni. Komabe, anthu padziko lonse amalemba dzina lakuti Yesu m’njila zosiyana-siyana, ndipo amalichula malinga ndi cinenelo cao. Iwo salephela kuligwilitsila nchito cabe cifukwa cakuti sadziŵa mmene kachulidwe kake kanali m’zaka za zana loyamba. Mofananamo, ngati mungapite ku dziko lina, n’kutheka kuti mungapeze kuti dzina lanu limachulidwa mosiyana m’cinenelo cina. Conco, anthu sangasiye kugwilitsila nchito dzina la Mulungu cabe cifukwa cakuti sadziŵa mmene kale anali kulichulila.

Cifukwa caciŵili cimene samalembela dzina la Mulungu m’Baibo n’cokhudza cikhalidwe ca Ayuda cakale kwambili cimene amatsatila. Ambili amakhulupilila kuti dzina la Mulungu siliyenela kuchulidwa. Cikhulupililo cimeneci n’cozikidwa pa kamvedwe kao kolakwa ka lamulo la m’Baibo limene limati: “Usagwilitse nchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala, pakuti Yehova sadzalekelela aliyense wogwilitsa nchito dzina lake mosasamala osam’langa.”—Ekisodo 20:7.

Lamulo limeneli limaletsa kugwilitsila nchito dzina la Mulungu mosasamala. Koma kodi limaletsa kugwilitsila nchito dzina lake moyenela? Iyai. Onse amene analemba Malemba Aciheberi (Cipangano Cakale) anali anthu okhulupilika amene anali kutsatila Cilamulo cimene Mulungu anapeleka kwa Aisiraeli. Koma anali kugwilitsila nchito dzina la Mulungu kaŵili-kaŵili. Mwacitsanzo, analigwilitsila nchito m’masalimo ambili amene anali kuimbidwa mofuula ndi gulu la olambila. Yehova Mulungu nayenso analangiza olambila ake kuti aziitanila pa dzina lake, ndipo amene anali okhulupilika anamvela. (Yoweli 2:32; Machitidwe 2:21) Conco, masiku ano, Akristu naonso amagwilitsila nchito dzina la Mulungu moyenela, monga mmene Yesu anacitila.—Yohane 17:26.

Otembenuza Baibo akamasiya dzina la Mulungu n’kumaikamo maina audindo amalakwa kwambili. Iwo amacititsa Mulungu kuoneka monga ali kutali kwambili ndi anthu, ngati kuti samafuna kuyandikana nao. Koma Baibo imalimbikitsa anthu kukhala ndi “ubwenzi wolimba ndi Yehova.” (Salimo 25:14) Ganizilani mnzanu amene mumakondana naye kwambili. Kodi mukanakondana naye kwambili ngati simunafune kudziŵa dzina la mnzanuyo? Mofananamo, ngati anthu sadziŵa dzina la Mulungu, lakuti Yehova, kodi angamuyandikile bwanji? Komanso, ngati anthu sagwilitsila nchito dzina la Mulungu, sangadziŵenso tanthauzo lake lofunika kwambili. Kodi dzina la Mulungu limatanthauza ciani?

Mulungu iye mwini anafotokoza tanthauzo la dzina lake kwa mtumiki wake wokhulupilika Mose. Pamene Mose anafunsa za dzina la Mulungu, Yehova anayankha kuti: “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” (Ekisodo 3:14) Conco, Yehova angakhale aliyense amene afunikila kukhala kuti akwanilitse zolinga zake.

Tinene kuti mukhoza kukhala munthu aliyense amene mufuna kukhala. Kodi anzanu mungawacitile ciani? Ngati mnzanu wina angadwale kwambili, kodi simungakhale dokotala waluso kwambili ndi kum’cilitsa? Ndipo ngati wina angakhale ndi vuto la zacuma, kodi simungakhale munthu wacuma ndi kum’thandiza. Koma zoona n’zakuti simungathe kukhala aliyense amene mungafune. Ndipo ndi mmene ife tonse tilili. Koma pamene muphunzila Baibo, mudzadabwa kwambili kuona mmene Yehova amakhalila aliyense amene akufunikila kuti akwanilitse zolinga zake. Ndipo zimam’kondweletsa kwambili kugwilitsila nchito mphamvu zake kuthandiza anthu amene amam’konda. (2 Mbiri 16:9) Anthu amene sadziŵa dzina lake sangazindikile makhalidwe a Yehova ocititsa cidwi amenewa.

Mwacionekele, dzina lakuti Yehova limafunika kugwilitsidwa nchito m’Baibo. Conco, kudziŵa tanthauzo la dzina limeneli ndi kuligwilitsila nchito pom’lambila, zingatithandize kwambili kuti tiyandikile Atate wathu wakumwamba Yehova.a

a Kuti mudziŵe zambili ponena za dzina la Mulungu, tanthauzo lake, ndi cifukwa cimene tiyenela kuligwilitsila nchito polambila, onani kabuku kakuti, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, kolembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani