ZAKUMAPETO
Yesu Kristu—Mesiya Wolonjezedwa
KUTI atithandize kuzindikila Mesiya, Yehova Mulungu anauzila aneneli ambili kuti alosele za kubadwa kwa mpulumutsi wolonjezedwa ameneyu, utumiki wake, ndi imfa yake. Maulosi onse a m’Baibo amenewo anakwanilitsika mwa Yesu Kristu. Kulondola kwake ndi tsatane-tsatane wa maulosi amenewa n’kocititsa cidwi. Mwacitsanzo, tiyeni tione maulosi ocepa cabe amene anakambilatu za zinthu zokhudza kubadwa kwa Mesiya ndi mmene umoyo wake unalili pamene anali mwana.
Mneneli Yesaya anakambilatu kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. (Yesaya 9:7) Ndipo Yesu anabadwiladi mu mzela wa Davide.—Mateyu 1:1, 6-17.
Mneneli wina wa Mulungu, Mika, nayenso anakambilatu kuti mwana ameneyu adzabadwila mu “Betelehemu Efurata,” ndi kuti m’kupita kwa nthawi adzakhala wolamulila. (Mika 5:2) Panthawi ya kubadwa kwa Yesu, mu Isiraeli munali matauni aŵili ochedwa Betelehemu. Tauni imodzi inali kumpoto kwa dzikolo, ndipo ina inali pafupi ndi Yerusalemu m’dziko la Yuda. Tauni ya Betelehemu imene inali pafupi ndi Yerusalemu poyamba inali kuchedwa Efurata. Yesu anabadwila m’tauni imeneyi, ndendende monga mmene maulosi anakambila.—Mateyu 2:1.
Ulosi wina wa m’Baibo unakambilatu kuti mwana wa Mulungu adzaitanidwa “kuti atuluke mu Iguputo.” Pamene anali mwana, Yesu anapita naye ku Iguputo. Pambuyo pa imfa ya Herode, anabwelela naye kudziko lakwao, ndipo zimenezi zinakwanilitsa ulosi.—Hoseya 11:1; Mateyu 2:15.
Pa chati imene ili papeji 200, pali malemba amene aikidwa pansi pa mutu wakuti “Ulosi” amene ali ndi mfundo zokamba za Mesiya. Yelekezelani zimenezi ndi malemba amene ali pa mutu wakuti “Kukwanilitsika.” Kucita zimenezi kudzalimbikitsa kwambili cikhulupililo canu cakuti Mau a Mulungu ndi oona.
Pamene muona malemba aulosi amenewa, kumbukilani kuti analembedwa zaka mazana ambili Yesu akalibe kubadwa. Yesu anati: “Zonse zokhudza ine zolembedwa m’cilamulo ca Mose, mu zolemba za Aneneli ndi m’Masalimo ziyenela kukwanilitsidwa.” (Luka 24:44) Pamene muona m’Baibo yanu mudzapeza kuti, mbali iliyonse ya maulosi onsewa inakwanilitsika!