LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 212-nkhani 213 pala. 1
  • Kodi Shelo ndi Hade N’ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Shelo ndi Hade N’ciani?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 212-nkhani 213 pala. 1

ZAKUMAPETO

Kodi Shelo ndi Hade N’ciani?

MU ZINENELO zoyambilila zimene Baibo inalembedwa, Ciheberi ndi Cigiriki, Baibo imagwilitsila nchito mau Aciheberi akuti sheʼohlʹ ndi mau ofanana Acigiriki akuti haiʹdes nthawi zoposa 70. Mau onse aŵili amakamba za imfa. Mabaibo ena amawatembenuza kuti “manda,” “helo,” kapena “dzenje.” Komabe, zinenelo zambili zilibe mau amene amamveketsa bwino tanthauzo la mau aciheberi ndi acigiriki amenewa. Conco, Baibo ya New World Translation imagwilitsila nchito mau akuti “Shelo” ndi “Hade.” Koma Baibo ya Buku Lopatulika m’malo ena imagwilitsila nchito mau akuti “Hade.” Kodi mau amenewa akuti “Shelo” ndi “Hade” amatanthauza ciani kweni-kweni? Tiyeni tione mmene Baibo imawagwilitsila nchito m’mavesi osiyana-siyana.

Lemba la Mlaliki 9:10 limati: “Kulibe kugwila nchito, kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu, ku Manda [kapena kuti Shelo] kumene ukupitako.” Kodi zimenezi zitanthauza kuti Shelo ni manda eni-eni kumene timaikako wokondedwa wathu akamwalila. Iyai. Baibo ikamakamba za manda eni-eni, imagwilitsila nchito mau ena Aciheberi ndi Acigiriki, osati sheʼohlʹ ndi haiʹdes. (Genesis 23:7-9; Mateyu 28:1) Ndiponso Baibo sigwilitsila nchito mau akuti “Shelo” kutanthauza manda amene anthu ambili amaikidwa pamodzi, monga manda a banja kapena dzenje limene amaikamo anthu ambili.—Genesis 49:30, 31.

Conco, kodi “Shelo” imaimila ciani? Mau a Mulungu amaonetsa kuti “Shelo,” kapena “Hade,” amatanthauza cinacake coposa ngakhale manda oikamo anthu ambili. Mwacitsanzo, lemba la Yesaya 5:14 limaonetsa kuti Shelo ‘yakulitsa malo ake ndipo yatsegula kwambili pakamwa pake kupitilila malile.’ Ngakhale kuti Shelo yameza kale anthu akufa ambili, titelo kukamba kwake, imaoneka kuti ikali ndi njala yofuna kumeza ena. (Miyambo 30:15, 16) Mosiyana ndi malo eni-eni, amene mungaikeko akufa oŵelengeka cabe, ‘Manda [kapena kuti Shelo] sakhuta.’ (Miyambo 27:20) Kutanthauza kuti Shelo sidzala ndipo ilibe malile. Conco, Shelo kapena Hade, si malo eni-eni opezeka kwina kwake. M’malo mwake, ndi malo ophiphilitsila kumene anthu onse amapita akafa.

Ciphunzitso ca m’Baibo ca kuuka kwa akufa cimatithandiza kudziŵa zambili pa tanthauzo la “Shelo” ndi “Hade.” Mau a Mulungu amaonetsa kuti Shelo ndi Hade amakhudza imfa imene anthu adzaukako.a (Yobu 14:13; Machitidwe 2:31; Chivumbulutso 20:13) Mau a Mulungu amaonetsanso kuti anthu amene ali m’Shelo, kapena Hade, amaphatikizapo osati cabe anthu amene anatumikila Yehova komanso anthu ena amene sanam’tumikile. (Genesis 37:35; Salimo 55:15) Conco, Baibo imaphunzitsa kuti kudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

a Mosiyanako, akufa amene sadzaukitsidwa amafotokozedwa kuti, sali m’Shelo, kapena Hade, koma m’Gehenna.” (Mateyu 5:30; 10:28; 23:33) Mofanana ndi Shelo ndi Hade, Gehenna nayonso si malo eni-eni.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani