LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 213-nkhani 215 pala. 2
  • Kodi Tsiku la Ciweluzo Lidzakhala Lotani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Tsiku la Ciweluzo Lidzakhala Lotani?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi pa Tsiku la Ciweluzo Padzacitika Zotani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2012
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 213-nkhani 215 pala. 2

ZAKUMAPETO

Kodi Tsiku la Ciweluzo Lidzakhala Lotani?

MUKAMVA za Tsiku la Ciweluzo, cimabwela m’maganizo mwanu n’ciani? Ambili amaganiza kuti, anthu mabiliyoni adzaonekela mmodzi-mmodzi ku mpando wacifumu wa Mulungu. Kumeneko, aliyense payekha adzaweluzidwa. Ena adzapatsidwa mphoto yokhala m’paladaiso kumwamba, ndipo ena adzapatsidwa cilango cokazunzika kosatha. Komabe, Baibo imakamba zosiyana ponena za nthawi imeneyi. Mau a Mulungu amafotokoza tsiku limeneli kukhala nthawi yofunika kuiyembekezela mwacidwi, nthawi yokonzanso zinthu, osati nthawi yocititsa mantha.

Pa lemba la Chivumbulutso 20:11, 12, mtumwi Yohane amafotokoza Tsiku la Ciweluzo kuti: “Ndinaona mpando wacifumu waukulu woyela, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathaŵa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimilila pamaso pa mpando wacifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweluzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwilizana ndi nchito zao.” Kodi Woweluza amene afotokozedwa pa lembali ndani?

Yehova Mulungu ndiye Woweluza wamkulu wa mtundu wonse wa anthu. Komabe, nchito yeni-yeni yoweluza anaiika m’manja mwa winawake. Malinga ndi Machitidwe 17:31, mtumwi Paulo anakamba kuti, Mulungu “wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweluza m’cilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzela mwa munthu amene iye wamuika.” Woweluza wosankhidwa ameneyu ndi Yesu Kristu woukitsidwa. (Yohane 5:22) Koma kodi Tsiku la Ciweluzo lidzayamba liti? Ndipo lidzakhala lalitali bwanji?

Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti Tsiku la Ciweluzo lidzayamba pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, pamene dongosolo la Satana lidzaonongedwa padziko lapansi.a (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:19–20:3) Pambuyo pa nkhondo imeneyi, Satana ndi ziŵanda zake adzaponyedwa m’phompho kwa zaka 1,000. Panthawi imeneyo, a 144,000 amene adzalamulila ndi Yesu kumwamba adzakhalanso oweluza, ndipo adzalamulila “monga mafumu limodzi ndi Kristu zaka 1,000.” (Chivumbulutso 14:1-3; 20:1-4; Aroma 8:17) Conco, tsiku la Ciweluzo si cocitika ca maola 24 cabe, koma lidzacitika kwa zaka 1,000.

Panyengo ya zaka 1,000 imeneyo, Yesu Kristu “adzaweluza amoyo ndi akufa.” (2 Timoteyo 4:1) “Amoyo” adzakhala “khamu lalikulu” limene lidzapulumuka Aramagedo. (Chivumbulutso 7:9-17) Mtumwi Yohane anaonanso “akufa . . . ataimilila pamaso pa mpando wacifumu” waciweluzo. Monga mmene Yesu analonjezela, akufa amene “ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Koma kodi anthu onse adzaweluzidwa pamaziko a ciani?

Malinga ndi masomphenya a mtumwi Yohane, “mipukutu inafunyululidwa,” ndipo “akufa anaweluzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwilizana ndi nchito zao.” Kodi m’mipukutuyi munali nchito zimene anthu anacita kale? Ai, ciweluzo cimeneco sicidzapelekedwa pa maziko a zinthu zimene anthu anacita akalibe kumwalila. Tidziŵa bwanji zimenezi? Baibo imati: “Munthu amene wafa wamasuka ku ucimo wake.” (Aroma 6:7) Conco, anthu amene adzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo, macimo ao adzakhala atafafanizika. Mipukutu imeneyo iyenela kuti iimila zinthu zinanso zimene Mulungu adzafuna kuti anthu acite. Kuti anthu amene adzapulumuka pa Aramagedo ndi amene adzaukitsidwa adzakhale kosatha, adzafunika kumvela malamulo a Mulungu, kuphatikizapo zinthu zatsopano zimene Yehova adzafuna kuti anthu azicita m’zaka 1,000. Motelo, anthu adzaweluzidwa pa zinthu zimene azicita mkati mwa nyengo ya Tsiku la Ciweluzo.

Panyengo ya Tsiku la Ciweluzo anthu mabiliyoni adzakhala ndi mwai woyamba wophunzila cifunilo ca Mulungu ndi kucicita. Zimenezi zitanthauza kuti padzakhala nchito yaikulu yophunzitsa. Ndithudi, “anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzila cilungamo.” (Yesaya 26:9) Koma si anthu onse amene adzafuna kucita cifunilo ca Mulungu. Lemba la Yesaya 26:10 limati: “Ngakhale munthu woipa atacitilidwa zabwino, sangaphunzile cilungamo. M’dziko locita zoongoka, iye adzacita zinthu zopanda cilungamo ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.” Anthu oipa amenewa adzaonongedwa kothelatu mkati mwa Tsiku la Ciweluzo.—Yesaya 65:20.

Pofika kumapeto kwa Tsiku la Ciweluzo, anthu amene adzapulumuka adzakhala ndi moyo wangwilo. (Chivumbulutso 20:5) Conco, mu Tsiku la Ciweluzo anthu adzabwezeletsedwa ku mkhalidwe wao wa poyamba wangwilo. (1 Akorinto 15:24-28) Ndiyeno ciyeso cotsilizila cidzacitika. Satana adzamasulidwa kuphompho, ndipo adzaloledwa kusoceletsa anthu kotsilizila. (Chivumbulutso 20:3, 7-10) Koma anthu amene adzatsutsa Satana adzasangalala ndi kukwanilitsika kwa lonjezo la m’Baibo lakuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Ndithudi, Tsiku la Ciweluzo lidzakhala dalitso kwa anthu onse okhulupilika.

a Ponena za Aramagedo, onani buku lakuti Insight on the Scriptures, Voliyamu 1, mapeji 594-595, 1037-1038, ndi buku lakuti Lambirani Mulungu Woona Yekha, mutu 20. Mabukuwa ndi olembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani