ZAKUMAPETO
Caka ca 1914 Ni Cofunika Kwambili M’maulosi a mu Baibo
PAFUPI-FUPI zaka 40 zapitazo caka ca 1914 cisanakwane, ophunzila Baibo anakambilatu kuti, m’caka cimeneci mudzacitika zinthu zapadela kwambili. Kodi zinthu zimenezi zinali ciani? Ndipo ndi umboni uti umene umaonetsa kuti caka ca 1914 cinali caka capadela?
Pa Luka 21:24 Yesu anati: “Anthu a mitundu ina adzaponda-ponda Yerusalemu, kufikila nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu [“nthawi zao za anthu akunja,” Buku Lopatulika] inawo zitakwanila.” Yerusalemu unali mzinda wa mtundu wa Ayuda, ndipo unali mpando wa mzela wa mafumu ocokela m’nyumba ya Mfumu Davide. (Salimo 48:1, 2) Komabe, mafumu amenewa anali apadela pakati pa atsogoleli a mitundu. Iwo anali kukhala pampando “wacifumu wa Yehova” monga anthu oimila Mulungu mwiniwake. (1 Mbiri 29:23) Conco, mzinda wa Yerusalemu unali kuimila ulamulilo wa Yehova.
Kodi ulamulilo wa Mulungu unayamba bwanji ‘kupondedwa ndi anthu a mitundu’? Ndipo zinayamba liti kucitika? Zimenezi zinayamba mu 607 B.C.E. pamene mzinda wa Yerusalemu unagonjetsedwa ndi Ababulo. Palibe munthu aliyense amene anakhala pa “mpando wacifumu wa Yehova,” ndipo mafumu a mumzela wa Davide anadulidwa. (2 Mafumu 25:1-26) Kodi ‘kuponda-ponda’ kumeneku kunali kudzacitika mpaka kale-kale? Iyai, popeza ulosi wa Ezekieli unakambapo za mfumu yotsilizila ya Yerusalemu, imene inali Zedekiya kuti: “Cotsa nduwila ndipo vula cisoti cacifumu. . . . Ufumu umenewu sudzapelekedwa kwa wina aliyense kufikila atabwela amene ali woyenelela mwalamulo kuutenga, ndipo ndidzaupeleka kwa iye.” (Ezekieli 21:26, 27) Munthu amene ali “woyenelela mwalamulo” kuvala cisoti caufumu ca Davide ndiye Kristu Yesu. (Luka 1:32, 33) Conco, ‘kuponda-ponda’ kunadzatha pamene Yesu anadzakhala Mfumu.
Kodi cinthu capadela cimeneci cinali kudzacitika liti? Yesu anaonetsa kuti anthu akunja anali kudzalamulila kwa nthawi yoikika. Nkhani ya m’buku la Danieli caputala 4 imaonetsa bwino utali wa nyengo imeneyi. Nkhaniyi imakamba za loto laulosi la Mfumu Nebukadinezala wa ku Babulo. Mfumuyi inaona cimtengo cimene cinadulidwa. Citsa cake sicinali kukula cifukwa anacikulunga ndi mkombelo wacitsulo ndi wamkuwa. Mngelo anati: “Padutse nthawi zokwanila 7.”—Danieli 4:10-16.
Mu Baibo, nthawi zina mitengo imaimila ulamulilo. (Ezekieli 17:22-24; 31:2-5) Conco, kudulidwa kwa mtengo wophiphilitsila kumaimila mmene ulamulilo wa Mulungu umene unaimilidwa ndi mafumu a ku Yerusalemu, unali kudzadulidwila. Komabe, masomphenya anaonetsa bwino kuti ‘kuponda-ponda Yerusalemu’ kudzakhala kwakanthawi—“nthawi zokwanila 7.” Kodi nyengo imeneyo ndi yautali wotani?
Lemba la Chivumbulutso 12:6, 14 limaonetsa kuti nthawi zitatu ndi theka ndi “masiku 1,260.” Conco, tikawilikiza nthawi zitatu ndi theka zikhala “nthawi zokwanila 7,” kapena kuti masiku 2,520. Koma anthu akunja sanaleke ‘kuponda-ponda’ ulamulilo wa Mulungu kwa masiku 2,520 kucokela pamene Yerusalemu anaonongedwa. Conco, n’zoonekelatu kuti ulosi umenewu unatenga nthawi yaitali kwambili. Malinga ndi lemba la Numeri 14:34 ndi Ezekieli 4:6, limene limanena za “tsiku limodzi kuimila caka cimodzi,” conco, “nthawi zokwanila 7” zinatenga utali wa zaka 2,520.
Zaka 2,520 zinayamba mu mwezi wa October m’caka ca 607 B.C.E., pamene Ababulo anagonjetsa mzinda wa Yerusalemu ndipo ufumu wa mumzela wa Davide unatengedwa. Nyengo imeneyi inatha mu mwezi wa October caka ca 1914. Panthawi imeneyo, “nthawi za amitundu zoikidwilatu” zinatha, ndipo Yesu Kristu anaikidwa kukhala Mfumu yakumwamba ya Mulungu.a—Salimo 2:1-6; Danieli 7:13, 14.
Monga mmene Yesu anakambilatu, “kukhalapo” kwake monga Mfumu yakumwamba kwadziŵika ndi zocitika za pa dziko lapansi, monga nkhondo, njala, zivomezi, ndi milili. (Mateyu 24:3-8; Luka 21:11) Zocitika zimenezo zimapeleka umboni wamphamvu wakuti, Ufumu wa kumwamba wa Mulungu unabadwa m’caka ca 1914, ndi kuti “masiku otsiliza” a dongosolo loipa lino la zinthu anayamba m’caka cimeneci.—2 Timoteyo 3:1-5.
a Kucokela mu October caka ca 607 B.C.E. kufika mu October caka ca 1 B.C.E. panapita zaka 606. Kucokela mu October caka ca 1 B.C.E. mpaka mu October 1914 C.E. panapita zaka 1,914. Tikaonkhetsa zaka 606 ndi 1,914, tipeza zaka 2,520. Kuti mudziŵe zambili zokhudza kuonongedwa kwa Yerusalemu mu caka ca 607 B.C.E., onani buku lakuti Kukambitsirana za m’Malemba, pamapeji 231 mpaka 233, lolembedwa ndi Mboni za Yehova.