LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 222-nkhani 223
  • Kodi Tiyenela Kukondwelela Maholide?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Tiyenela Kukondwelela Maholide?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Zikondwelelo Zonse Zimakondweletsa Mulungu?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Kodi Zikondwelelo Zonse Zimam’sangalatsa Mulungu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Zikondwelelo Zimene Mulungu Amadana Nazo
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 222-nkhani 223

ZAKUMAPETO

Kodi Tiyenela Kukondwelela Maholide?

ZIKONDWELELO zofala zacipembedzo ndi maholide amene anthu ambili amakondwelela masiku ano si zimacokela m’Baibo. Nanga zinacokela kuti? Ngati mungathe kufufuza mu laibulale, mudzadabwa zimene mabuku amakamba pa nkhani ya maholide ofala amene anthu amakondwelela ngakhale kumene mumakhala. Tiyeni tione zitsanzo zocepa.

Isitala. Buku lina limati: “Palibe paliponse pamene Cipangano Catsopano cimaonetsa cikondwelelo ca Isitala.” (The Encyclopædia Britannica) Nanga Isitala inayamba bwanji? Inacokela m’kulambila kwacikunja. Ngakhale kuti holide imeneyi ndi yokumbukila ciukililo ca Yesu, miyambo imene imacitika panyengo ya Isitala si ya Cikristu.

Kukondwelela Caka Catsopano. Tsiku la kukondwelela Caka Catsopano pamodzi ndi miyambo imene imacitika pa tsiku limenelo imasiyana m’maiko osiyana-siyana. Ponena za mmene cikondwelelo cimeneci cinayambila, buku lina linati: “Wolamulila waciroma Juliasi Kaisara anaika tsiku la January 1 kukhala tsiku lokondwelela Caka Catsopano m’caka ca 46 B.C. Aroma anapeleka tsiku limeneli kwa Janusi, amene anali mulungu wa zipata, zitseko, ndi ciyambi ca zinthu. Dzina la mwezi wa January linacokela kwa Janusi, amene anali ndi nkhope ziŵili, yoyang’ana kutsogolo ndi ina yoyang’ana kumbuyo.” (The World Book Encyclopedia) Conco, kukondwelela Caka catsopano kunacokela ku miyambo yacikunja.

Tsiku la Valentine. Buku lina limati: “Tsiku la Valentine linacitika pa tsiku laphwando lokumbukila Akristu aŵili ochedwa kuti Valentine amene anaphedwa kaamba ka cikhulupililo cao. (The World Book Encyclopedia) Koma miyambo imene imacitika patsikuli ioneka kuti inacokela ku phwando lakale-kale la Aroma lochedwa Lupercalia, limene linali kucitika pa February 15. Phwando limenelo linali kulemekeza Juno, mulungu wamkazi wa akazi aciroma ndi wa cikwati, ndi Pani, mulungu wa cilengedwe.”

Maholide Ena. N’zosatheka kufotokoza maholide onse amene amacitika pa dziko lonse. Komabe, Yehova sakondwela ndi maholide amene amalemekeza anthu kapena mabungwe a anthu. (Yeremiya 17:5-7; Machitidwe 10:25, 26) Dziŵaninso kuti, zikondwelelo zimene zimakondweletsa Mulungu ndi zija zimene ciyambi cakenso cimam’kondweletsa. (Yesaya 52:11; Chivumbulutso 18:4) Mfundo za m’Baibo zochulidwa m’nkhani 16 ya m’buku lino zidzakuthandizani kuti mudziŵe mmene Mulungu amaonela anthu amene amacita zikondwelelo za maholide amene si acipembedzo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani