ZAKUMAPETO
Tuzigawo twa Magazi Ndiponso Njila Zimene Amatsatila Pocita Opaleshoni
Tuzigawo twa magazi. Tuzigawo twa magazi tumatengedwa ku zigawo zinai zikuluzikulu za magazi. Zigawo zimenezi ndi maselo ofiila, maselo oyela, maselo othandiza magazi kuundana ndi madzi a magazi. Mwacitsanzo, maselo ofiila ali ndi puloteni yochedwa hemoglobin. Mankhwala opangidwa ndi puloteni imeneyi, amapatsidwa kwa odwala amene ali ndi magazi ocepa kapena amene ataya magazi ambili.
Madzi a m’magazi, amene pafupifupi onse ndi madzi wamba, ali ndi zinthu zambili zothandiza m’thupi monga mcele, mavitameni, shuga ndi zina. Madzi a m’magazi amathandizanso magazi kuundana, amakhala ndi maselo olimbana ndi matenda, ndipo amakhala ndi puloteni yochedwa albumin. Ngati wina wadwala matenda ena ake, madokotala angamupatse mankhwala opangidwa ndi madzi a m’magazi a munthu amene thupi lake linagonjetsa matenda amenewo. Maselo oyela angakhale ndi mapuloteni othandiza kucilitsa matenda ena oyambukila ndi a kansa.
Kodi Mkristu angalandile mankhwala amene apangidwa ndi tuzigawo twa magazi? Baibulo silipeleka malangizo acindunji pa nkhani imeneyi, conco aliyense ayenela kutsatila cikumbumtima cake popanga cosankha pamaso pa Mulungu. Ena angakane zigawo zonse za magazi, poganizila kuti cilamulo ca Mulungu kwa Aisiraeli cinanena kuti magazi a munthu kapena a nyama ayenela ‘kuthilidwa pansi.’ (Deuteronomo 12:22-24) Ena angakane kuikidwa magazi athunthu kapena zigawo zake zikuluzikulu, koma angalandile mankhwala amene ali ndi kacigawo kakang’ono ka magazi. Iwo angaganize kuti tuzigawo twa magazi tumenetu situimilanso moyo wa munthu.
Popanga cosankha pa nkhani yokhudza tuzigawo twa magazi, dzifunseni kuti: Kodi ndikudziŵa kuti kukana tuzigawo twa magazi kumatanthauza kuti ndakananso zithandizo zina za mankhwala monga mankhwala olimbana ndi matenda kapena othandiza magazi kuundana kuti munthu aleke kutaya magazi? Kodi ndingakwanitse kufotokoza kwa a dokotala cifukwa cake ndakana kapena kuvomela mankhwala amene ali ndi kacigawo kapena tuzigawo twa magazi?
Njila zimene amatsatila pocita opaleshoni. Njila zimenezi zimaphatikizapo kusungunula magazi ndi kupulumutsa maselo a magazi. Kusungunula magazi kumacitika mwa kucotsa magazi m’thupi la wodwala ndi kuikamo madzi oonjezela magazi, ndiyeno pambuyo pake magaziwo amawabwezeletsa m’thupi. Potsatila njila yopulumutsa maselo a magazi, magazi amene amatayika popanga opaleshoni amawapopa ndi kuwabwezeletsa m’thupi la wodwalayo. Magazi amene amapopedwa pacilonda kapena pamalo amene ang’amba, amatsukidwa kapena kusefedwa, kenako amawabwezeletsa m’thupi la wodwalayo. Popeza madokotala amagwilitsilila nchito njila zimenezi mosiyanasiyana, Mkristu ayenela kufunsilatu njila imene adokotala ake afuna kugwilitsila nchito.
Popanga cosankha cokhudza njila zimenezi, muyenela kudzifunsa kuti: ‘Ngati ena a magazi acotsedwa m’thupi langa ndi kusungidwa kwina ngakhale kwa kanthawi kocepa, kodi cikumbumtima canga cingandilole kuona kuti magaziwo akali mbali ya thupi langa ndi kuti sayenela ‘kuthilidwa pansi’? (Deuteronomo 12:23, 24) Kodi pa opaleshoni cikumbumtima canga cophunzitsidwa Baibulo cingandivute ngati angatenge magazi anga ndi kuwakonzakonza kenako n’kuwabwezeletsanso m’thupi langa? Kodi ndikudziŵa kuti kukana njila zonse za cithandizo ca mankhwala zogwilitsila nchito magazi anga, kumatanthauza kuti ndikukananso njila zopelekela cithandizo monga kucotsa magazi kuti apime matenda, kugwilitsila nchito makina osefa magazi kapena makina othandizila mtima ndi mapapo?’
Mkristu ayenela kusankha yekha mmene a dokotala angagwilitsile nchito magazi ake panthawi ya opaleshoni. N’cimodzimodzinso ndi njila zina zamakono zopimila matenda zimene zimafuna kucotsa magazi ocepa, kuwakonzakonza ndi kuwabwezeletsanso m’thupi.